KODI KUFUNIKA KWA UBATIZO WA CHIKHRISTU NDI CHIYANI?

Anonymous

KODI KUFUNIKA KWA UBATIZO WA CHIKHRISTU NDI CHIYANI?

Ubatizo m’baibulo umatanthawuza , kudziwika ndi Khristu mu imfa yake. Monga Khristu anafa ndipo anayikidwa m’manda, tinabatizidwa. Tikuwerenga izi mu Aroma 6,3+4: “Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse, amene tinabatizidwa mwa Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake tinayikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa mu imfa: kuti monga Khristu anawukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano.” 

Ubatizo umatanthawuzanso, kuti iye amene akubatizidwa akuwonetsera, kuti tsopano ali wophunzira wa Yesu. Ubatizo sumapulumutsa! Njira yokhayo yopulumukira ndi mwa kuvomeleza Yesu monga Mbuye ndi mpulumutsi, Ubatizo ndi chinthu china chimene chimatsatira pambuyo pake. Dziwa kuti ubatizo monga wafotokozeledwa mbaibulo, sumakupanga kukhala chiwalo cha mpingo uliwonse kapena gulu lirironse, monga ena amaphunzitsa dero. Ayi ubatizo umatanthawuza kuti winawake mowonetsera akuudziyika iye yekha Pambali ya Mbuye wake Yesu.

KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI ZA KUSUDZULA + UKWATI?

Mulungu amatikonda ife ndipo amadziwa zosowa ndi zokhumba zathu. Ndi chifukwa chake anayika ukwati mu Genesis2. Baibulo likunena kuti mwamuna m’modzi akuloledwa kukhala ndi mkazi m’modzi ndipo ichi alinso malo okhawo a kugonana, atakwatilana.

Pa kusudzula Baibulo liri lomveka bwino: Mulungu amadana ndi kusudzula (Mal. 2,16). Mu Luka 16,18 timawerenga “Yense wakusudzula mkaziwake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.” Mulungu akufuna mamuna akonde mkazi wake ndi kumusamala, ndipo mkazi athandize mamuna wake. Nthawi zina, mwankhani ina ya padera pali kuthekera, koma chiphunzitso cha chindunji cha Baibulo ndi, kutsutsana ndi Baibulo kusudzula ndipo pamene chachitika ichi, palibe njira yakukwatilira munthu wina.

KODI TANTHAWUZO LA KULANKHULA MALILIME NDI CHIYANI? KODI NDI KWA LERO?

Mbali yachiwiri ya funso lako “kodi ndi kwa lero?” ili bwino kwambiri! Yankho ndi: ayi, siali alero. Kulankhula malilime ndi mafotokozeledwe ena a Mzimu Woyera zinapelekedwa Munthawi za akhristu woyamba, ndicholinga chothandizira uthenga wabwino womwe umapitiria. Baibulo likuti, kulankhula mmalilime uku kudzaleka patapita nthawi ina (1Akorinto 13,8): “kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka; kapena nzeru idzakhala chabe.”  Lerolino pali kugwilitsa tchito molakwikwa kwambiri zinthu iz,i makamaka mu afirika, chifukwa zikopa anthu. Koma mu gulu la akhristu amene amasonkhana pamodzi pamaziko a Baibulo, sudzapeza wina akulankhula malilime.

KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI ZA CHOPELEKA?

Chopeleka chimachitika pa tsiku la sabata mu mipingo. Zimagwilitsidwa tchito kuthandiza anthu wosawuka ngati akazi amasiye, ana amasiye, anthu okalamba, kapena iwo amene ataya katundu wawo, ndinso kuthandiza ogwira tchito ya ambuye. Sizina gwiritsidweko tchito yolipilira munthu monga m’busa kapena china chofanana, monga umazipeza kawiri kawiri mu masiku athuwano. Baibulo likuti aliyense (osati akuluakulu okha kapena anthu apadera) akuyenela kufuna kupeleka.  Ndi udindo wawukulu wa abale mu mpingo umodzi kugwilitsa tchito ndalama, zimene zapelekedwa , molingana ndi chifuniro cha Mulungu, chifukwa sindalama zawo, koma ndi za Mulungu.

KODI MKAZI WA KAINI NDINDANI?

Kaini ndi wa mbadwo woyambilira wa anthu pambuyoa pa makolo ake, Adamu ndi Hava. Mu Genesis 5,4 timawelenga, kuti Adamu ndi Hava anali ndi ana amuna 33 ndi ana akazi 23. Mu nthawi imeneyo kunali kwakuti munthu amkwatira m’longo (chemwali) wake ( chimene sichimaloledwa m’masiku athu ano). Kumbukira kuti mu nthawi izi anthu amakalamba kwambiri mosiyana ndi masiku athu lero. Adamu anali wazaka 930, nthawi imene anamwalira. Chomcho panali ana ambiri pa nthawi yayitali kwambiri. Tonse ndife ana aAdamu ndi Hava, monga anali anthu okhawo padziko lapansi Atatha maziko ake.

Zikomo kwambiri chifukwa cha mafunso ako Yamikani! Ndiri osangalara kuwayankha ndipo ngati uli ndi ambiri – chonde ndidziwitse. Ndidzayankha mofulumila kwambiri m’nthawi iyi! Chinthu chofunikira kwambiri pa moyo wako ndi, chakuti ubwere kwa Ambuye Yesu ndi kumulandira Iye monga Mbuye ndi Mpulumutsi, ndicho chomwe timapemphelera. 

Ambuye akudalitseni!