KUYAMBA NDI KRISTU
Hendrik Leendert Heijkoop
MAKALATA OSIYANASIYANA KWA OTEMBENUKA MTIMA KUMENE
(GAWO LOYAMBA)
ZA MKATIMU
- Kodi Munthu Akuyenera Kutembenuka Mtima?
- N’chifukwa Chiyani Munthu Akuyenera Kutembenuka Mtima?
- Ndingapeze bwanji Mtendere ndi Mulungu?
- Kumasulidwa ku Mphamvu ya Uchimo
- Kodi Mulungu Anayikiratu Anthu kuti Atayike?
Kusankha
MUTU 1
KODI MUNTHU AKUYENERA KUTEMBENUKA MTIMA?
Wokondedwa mzanga,
Mutu umene unabweretsa ndi wofunika kwambiri, tsopano mwamsangala ndidutsamo m’mutu umenewu.
Unalemba kuti mkukumana komanso mkukambirana ndi anthu ena wakhala ukuwuzidwa kuti ukuyenera kutembenuka mtima, koma iweyo sukuona kufunikira kwa kutembenuka mtimaku.
Watanganidwa kwambiri ndi maphunziro komanso ntchito yako. Uli ndi nyumba yabwino komanso amzako a pamtima. Ukuyembekezeka kukhala ndi udindo wabwino ku ntchito posachedwapa, ndipo ukuyembekezera kuona china chake m’dziko lapansi. Uli wokhutitsidwa zedi ndi nyengo zako, chilungamo chake ndi chakuti ukuona kuti kuwuzidwa kuti utembenuke mtima ndi zokutopetsa zedi ndiponso zakukwana.
Inetu ndingathe kumvetsa za zimenezi. Pali anthu ena amene akusamala kwambiri mu zochita za anthu ena, popereka uphungu wabwino tsiku ndi tsiku, kapena kuwuza ena za machimo awo. Izitu ndi zotopetsa kumauzidwa nthawi ndi nthawi makamaka ukaganiza kuti zimene akunenazo ndi zoona.
Ndipo, pofuna kutsimikizira kuti izi ndi zofunika kwambiri: Kodi anthuwo akulondola kapena akulakwitsa? Kodi ukuyeneradi kutembenuka mtima, kapena sikofunikira kwenikweni kutero? Koma ngati zikuoneka kuti ndi zopanda phindu, ukhoza kukhala chomwecho ngakhale pamapeto ungadzapezeke kuti umalakwitsa ndi iweyo.
Udzadziwa bwino nthawi ina. Koma kutembenuka mtima kumakhudzana ndi funso la kumene ukakhale moyo wako wonse. Chimenechi ndi chofunika kwambiri ndipo ukuyenera kutsimikizika nacho mtima.
Kodi unaganizirako mofatsa kuti umuyaya ndi chiyani? Ndikuvomereza kuti sitingamvetsetse za izi pokhapokha titafikako ku malo amuyayako. Komabe ndikofunika kulingalirapo komanso kukhala ndi chithunzithunzi cha zimenezi.
Ndinawerengapo nthano ya mnyamata wanzeru zochuluka pamene mfumu ya dziko inkafuna kumuyesa mnyamatayo. Mfumuyo inamufunsa kuti anene umuyaya ndi wotalika bwanji?
“Mfumu,” nayankha mnyamatayo, “kudziko lina lakutali kuli phiri lalitali lopangidwa ndi mkuwa, pamwamba pake pamafikira mlengalenga. Kamodzi pa zaka 100 zilizonse mbalame inkabwera paphiripo ndi kumanola mulomo wake pa phiripo. Pamene phirilo linatha pang’onopang’ono ndi kunoletsako, ndiye kuti mphindi imodzi ya umuyaya imadutsa”.
Yankho ili likutipatsa chithunzithunzi chabe cha kusatha kwa umuyaya, sichoncho kodi? Komabe siyankho lolondola. Popeza umuyaya ulibe mphindi. Kumeneko zaka 1000 zili ngati tsiku limodzi ndipo tsiku limodzi lili ngati zaka 1000 (2 Petro 3:8). Umuyaya ulibe mathero kapena muyeso umene tingayesere.
Komabe nkhani iyi imationetsa ubale pakati pa kutalika kwa nthawi imene timakhala pansi pano ndi umuyaya umene uli kubwera. Kodi zaka 10, 50, 80 kapenanso zaka 100 ndi chiyani kufanizira ndi umuyaya? Kodi sikofunikira tsopano kudziwa kuti umuyaya wathu tikakhala kuti ndipo tikakhala bwanji?
Ndikukumbutsidwa nkhani ina yakale. Ukudziwa kuti mzaka za m’ma 1460 maulamuliro ambiri amalemba ntchito anthu amene amanena nthabwala. Anthu amenewa makamaka amakhala olumala ndipo amavala zovala zosaoneka bwino ndipo amayenera kusangalatsa mbuye wawo ndi nthabwala. Awatu anali akatswiri a nthabwala m’nyengo imeneyo.
Tsiku lina mwana wa mfumu anapereka chipewa cha ‘wopusa’ kwa m’nyamata wake wa nthabwala — ichi chinali chipewa choperekedwa ngati mphoto kwa munthu amene wanena nthabwala yosangalatsa kwambiri kuposa onse. Chinali chokongoletsedwa ndi mabelu komanso anapatsidwa ndodo ngati chizindikiro cha ulamuliro wake.
Ndipo iye anakhazikitsa lamulo, kuti ngati pangapezeke munthu wina wa nthabwala kuposa iyeyo akuyenera kupereka chipewacho kwa munthuyo. Pasanapite nthawi, mwana wa mfumu uja anadwala wambiri. Wanthabwalayo anabwera kudzamuona, namufunsa kuti akupeza bwanji. Mwana wa mfumu uja anayankha kuti dotolo wanena kuti palibe kusintha kwenikweni ndipo kuti posakhalitsa amwalira.
“Chabwino” anatero wanthabwalayo, “mosakayika konse ndiyesa mwakonzekera mokwanira za ulendo waukulu umene mukuyenera kuyendawu ndipo kuti mwaonetsetsa kuti zonse ndi zokonzeka kumalo kumene akukakulandiraniko.”
“Ayi ndithu” anayankha chotero mwana wamfumu uja, “ngozi yagona pamenepo, sindikudziwa momwe akandilandilire”. “Koma inu simumadziwa kuti tsiku lina mukuyenera kudzayenda ulendo woterewu?” “Ndinkadziwa, koma sindinafune kuganizirako chifukwa panali zinthu zambiri zoyenera kuchita.”
“Koma” anayankha wanthabwalayo, “pamene munkapita pa ulendo ulionse, mumatumiza nthumwi patsogolo panu kuti awonetsetse chakudya, chakumwa ndi zofunikira zina kuti zilipo zokwanira. Mukapita kumalo ena kwa masabata angapo kapena miyezi ingapo zonse munkakonzeratu, antchito ambiri amapita tsiku la ulendo lisanafike kuti zonse zikhale m’malo mwake mukamadzafika.
Koma pa ulendo waukulu ngati umenewu kumalo amene mukakhaleko kwa muyaya simunakonzekere ngakhale pang’ono! Eni, tengani chisoti chanu cha “wopusa” ndi ndodo yanu ya chifumu popeza sindinakhaleko munthu wanthabwala kuposa inu!”
Kodi wanthabwalayu sanalondole? Unapita ku sukulu kwa zaka zoposera khumi, ndipo pano ukugwira ntchito masana komanso kuphunzira usiku ndipo ukuyembekezera kupeza udindo wabwino posachedwapa.
Wakhala wotanganidwa kwa zaka makumi awiri ndi cholinga chakuti zaka makumi anayi zikubwerazi udzakhale utapanga ndalama zambiri; ndiponso kuti udzakhale pamoyo ofewa kwa zaka zina khumi ukalandira ndalama zako zopumira pa ntchito, ndi kuti ukakhalabe ndi moyo mpaka kukalamba, zaka zina makumi awiri ukusangalalabe.
Kodi ukhoza kuganiza motani za makolo amene sangatumize ana awo ku sukulu ndi kuwonetsetsa kuti asaphunzire luso chifukwa chakuti amanena kuti “asiyeni anawa asewere.” Ana samaganiza konse za mtsogolo. Akakula ndi kuyamba kudzithandiza okha, apa ndi pomwe amaonekera m’mene adzikhalira moyo wawo.
Tsopano mukatenga kuzunzika ndi nsembe imene munapereka zaka zonsezi za moyo wanu ndi cholinga chofuna kudzakhala pabwino kwa zaka makumi asanu kapena makumi asanu ndi limodzi za mtsogolo, nanga simukuona kuti zilibe phindu kunyalanyaza za moyo wanu wa muyaya ukubwera mtsogolo, komanso osakhala ndi nthawi ya kudzifunsa nokha funso lakuti: “kodi ndikakhala kuti kwa muyaya?”
Pambali pa zonsezi, mulibenso chitsimikizo kuti mudzapeza malo abwino. Kuonjezera apa, akudziwa ndani kuti mwina mukhoza kudwala mwinanso kumwalira kumene musanafikepo pamene mukufuna kufikira? Koma mukudziwa ndithu kuti umuyaya ukukudikirani.” Ndi gawo limodzi la munthu kuti kamodzi adzamwalire (Ahebri 9:27).
Palibe munthu ngakhale onyoza kwambiri kapena wokanitsitsa kuti kuli Mulungu amene anakanapo zokhudza ndime imeneyi. Zimenezi sangakane. Aliyense akhoza kumuseka, nanga ndi ndani amene anapitako kumalo kumene sikupezeka imfa? Ndipo kumaliza kwake kwa ndimeyi “ndipo atafa chiweruziro” izinso ndi zoona ndithu!
N’zosathandiza konse kukhala osasamala za zimenezi, koma kungokhala ndi kudikira chondifikira chindifikire? Komabe, mudzapeza panokha komwe mukakhale kwa muyaya. Komatu panthawiyo zidzakhala kuti zakhadzikika mpaka kalekale! “Pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo” (Mlaliki 11:3).
Tsopano mukhoza kunena kuti, “Indedi, koma nanga ndithamangiranji? Ndine munthu wotanganidwa. Ndiye nditenge nthawi yanga pa kulingalira za zinthu zoopsa ngati imfa ndi kumwalira? Ndingathe kudzachita zimenezi ndikadzakula. Apa ndidzakhala nditaona komanso kusangalala ndi moyo wanga pa nthawi imeneyi, ndipo ndidzakhala ndi nthawi yokwanira kuti ndiganizire za imfa.”
Kodi muli ndi chitsimikizo kuti mudzakhala zaka zina makumi asanu mudakali ndi moyo? Kapena makumi atatu? Kapena zaka khumi? Kapena miyezi khumi ndi iwiri? Kapenanso maola khumi ndi awiri? Ndimakumbukira wogulitsa mu golosale wina amene ankayima kuseli kwa chitseko ndi kumamvetsera uthenga wabwino ukulalikidwa mu msewu. Ndipo uthengawu utatha anapita pa balaza, nakhala pampando — kenako anamwalira!
Ndipo mutati mwakhala nthawi yayitali, kodi mukufuna kukhala mwa inu nokha pokhapokha muli ndi mphamvu ndi thanzi kenako kudzapereka nthawi yokhala ya moyo wanu kwa Mulungu? ngati mukufuna kuchita izi (tingoyerekeza kuti mwakhala nthawi yayitali chomwechi), Kodi Mulungu akhoza kukulandiranibe?
Zoonadi, Mulungu “afuna anthu onse apulumuke” (1 Timoteo 2:14). Akuyitana anthu onse “Yanjanitsidwani ndi Mulungu” (2 Akorinto 5:30).
Analandira chigawenga pa mtanda paja ndi ena ambiri amene anatembenukira kwa Iye panthawi yawo ya kumwalira. Ineyo ndikudziwa za mayi wina amene anatembenuka mtima ali ndi zaka 85 zakubadwa.
Koma Yobu 33 akutiuza kuti Mulungu amalankhula kamodzi kapena kawiri kwa munthu ndipo munthu akapanda kulabadira, ‘Mulungu amatseka chilangizo chawo’. Pamene Farao anakana kangapo kumvera, Mulungu anaumitsa mtima wake kuti patapita nthawi iye asatembenukenso mtima.
Ndipo mkwatulo wa mpingo wa Mulungu ukadzachitika Mulungu adzatumiza chisokeretso kwa onse amene anamva uthenga wabwino koma sanaulandire, “kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupilire choonadi” (2 Atesalonika 2:11-12). Mulungu angathe kuchitanso izi ndi inu, ngati mukukanabe kuyitana kwake kuti mubwerere kwa Iye.
“Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu ali nkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima; Chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuyikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa” (Machitidwe 17: 30-31).
Kodi simungathe kukhala okhudzika pa nkhani imeneyi ndi kupita kwa Mulungu, kulapa machimo anu ndi kumufunsa iye akulandireni? “Chifukwa chake tili atumiki m’malo mwa Kristu monga ngati Mulungu ali kudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m’malo mwa Kristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo mmalo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye” (2 Akorinto 5:20-21). “Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu” (Ahebri 4:7).
Ndatha ine
H.L.H
MUTU 2
N’CHIFUKWA CHIYANI MUNTHU AKUYENERA KUTEMBENUKA MTIMA?
Wokondeka mzanga,
Unandifunsa kuti ndi chifukwa chiyani munthu akuyenera kutembenuka mtima komanso kutembenuka mtima kumatanthauza chiyani. Yankho lapafupi pafunso lako loyamba ndi ili: tikuyenera kutembenuka mtima chifukwa Mulungu akutero.
Mulungu akanena chinthu, amakhala mathero a kutsutsa kwina kulikonse. Chotero ife, wolengedwa ake, tayenera kuweramitsa mitu yathu ndi kumvera. “Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, undipangiranji ine chotero?” (Aroma 9:20).
Ndipo ku Machitidwe 17:30 timaona kuti “Nthawi ya kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu ali nkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;” Indetu, m’Chipangano Chakale muli masamba 80 komanso masamba 70 m’Chipangano Chatsopano omwe amafotokoza bwino za kutembenuka mtima.
Pakuti Mulungu amatiuza momveka bwino m’mau ake chifukwa chomwe akulamulira munthu kuti atembenuke mtima. “Komatu Iye aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa” (2 Petro 3:9). Ndipo Machitidwe 17 akutipatsa ngati chifukwa cha kulamulira anthu onse kuti atembenuke, chifukwa “wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi m’chilungamo”.
Tsiku likubwera limene munthu aliyense adzayenera kuwerengera kwa Mlengi mlandu wake. Ndipo Mulungu, amene adziwa munthu aliyense m’magawo onse, akudziwa chigamulo cha Oweruza momwe chidzakhalire. “Pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu” (Aroma 3:23).
Chifukwa chake Mulungu afuna anthu kuti atembenuke, “pakuti Mpulumutsi wathu Mulungu afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi” (1 Timoteo 2:3-4).
MUNTHU NDI WOCHIMWA
Ichi ndi choonadi chenicheni. Ndi zoona kuti ambiri saganizira za chinthu chimenechi, komanso pali anthu ena amene amakana kuti munthu ndi wochimwa. Koma anthu amenewa amatsimikizika kuti zomwe amakambazo ndi zoona? Kodi alipo woona mtima amene anganene kuti sachita zinthu zolakwa?
Kangapo ndakhala ndikufunsa munthu wina, amene wakhala akulalikira kuti amakhala moyo wabwino, ndi kuchitira anthu ena zabwino monga mwa kuthekera kwake, ngati chikumbumtima chake sichinamutsutsepo ataganiza kapena kuchita molakwika. Sikawirikawiri munthu wotereyu kulimba mtima ndi kuvomereza kuti zoterezi zidamuchitikirapo.
Munthu wochimwa ndi amene adachimwapo. Sakhala wochimwa chifukwa wapanga zinthu zambiri zolakwa! Tchimo limodzi lokha limapangitsa munthu kukhala wochimwa. Pamoyo wathu wa tsku ndi tsiku timazidziwa bwino lomwe za chimenechi. Palibe amene anganene kuti, “auje sichigawenga chifukwa anaphako munthu kamodzi kapena kawiri kokha.”
Komabe pamene zikukhudza ubale wake ndi Mulungu, pamenepo munthu amafuna kuyikapo mlingo wina. Chifukwa akapanda kutero adzadzitsutsa yekha
CHIKUMBUMTIMA
Mulungu anapereka kwa munthu aliyense chikumbumtima (Aroma 2:15), chimene chimamutsutsa ku zinthu zina zolakwika, koma chikumbumtima sichimaonetsa zinthu zonse zimene zili zolakwika. Chikumbumtima chimapangidwa ndi malo amene munthu ali. Pakuti chimapereka chenjezo pamene wina achita chinthu chimene ndi chovomerezeka kuti ndi cholakwika kumalo kumene munthuyo ali kapenanso kumene iye anakulira.
Mulungu anaonetsetsa kuti anthu onse — ngakhale iwo amene sanamveko za Mulungu ndipo sadziwa Mau ake — achenjezedwe pamene mwakudziwa akuchita zoipa, kuti abwerere ku umunthu wawo ndi kuzindikira kuti ali wochimwa komanso wotsutsika.
Mukakumbukira moyo wanu wa m’mbuyo, ndi machimo angati amene mwakhala mukuchita amene mukuwadziwa kale? Pano muli ndi zaka 18. Tiyeni tingoyerekeza kuti pa zaka 8 zoyambirira za moyo wanu simunachitepo choipa china chilichonse.
Ngakhale nokha mukudziwa kuti izi siziri choncho, pakuti mukudziwa bwino lomwe kuti chikumbumtima chanu chinakutsutsani kale isanafike nthawi imeneyi. Koma ndi kangati kamene chikumbumtima chanu chakhala chikukutsutsani kufikira lerolino?
Tingoyerekeza kuti mumasutsika kamodzi patsiku, ndiye kuti pa chaka mumasutsika ka 365, kutanthauza kuti pa zaka khumi ndinu osutsika kokwanira ka 3,650. Kwa wina wa zaka 28 kuchotserapo zaka 8 zoyambirira ndiye kuti n’kokwanira 7,300, wa zaka 68 n’kokwanira ka 21,900.
Ndipo tikhoza kunena kuti chikumbumtima chanu chakuuzani kuti mwakhala muli wochimwa kokwanira ka 3,650, ndipo kodi inu simunachimwe kuposera pamenepa? Kodi wina amene wachita machimo motere angathe kunenabe kuti siwochimwa? Kodi Mulungu wolungama sakuyenera kuweruza otere kuti azindikire pamaso pa Mulungu kuti anachimwira Iye ndipo kuti wayenera kutaika kwa muyaya.
MACHIMO OSAWADZIWA
Komatu pano pakubwera funso lina. Kodi munthu ndi wolakwa pokhapokha akachimwa akudziwa? Kodi sali wochimwanso akazindikira kuti zimene akuchitazo ndi zoipa? Kodi woweruza sagamula kuti munthu wachimwa ngakhale munthuyo atanena kuti samadziwa lamulolo? Amayenera kudziwa popeza malamulo amalembedwa.
Ndiye tili ndi mau akuti ‘Umbuli si chitetezo cha ku lamulo’ Pena oweruza akhoza kuganizirako umbuliwo pa chiweruzo kwa wolakwayo. Woyimira anthu pa milandu amene waphwanya malamulo ena amalangidwa kwambiri kusiyana ndi munthu wina wovuta kwambiri amene angapalamule mlandu womwewo. Komabe mu zonsezi chiweruzo chimakhalabe kuti “walakwa.”
Tikupezanso zomwezi m’Mau a Mulungu. “Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zili zonse azidetsa Yehova; angakhale analibe kudziwa koma wapalamula ... mphulupulu yake” (Levitiko 5:17).
Izi ndi zomveka bwino lomwe. Kodi munthu amene walengedwa ndipo ali ndi udindo kwa Mlengi wake n’kukhala ndi ufulu wakudzisankhira yekha ngati ndi wolakwa kapena ndi wosalakwa? Izi sizingakhale choncho! Mlengi, amene wapanga zolenga zake ndi kupereka ulamuliro kwa Iye yekha ali ndi mphamvu ya kuweruza ngati zolengedwa zake zachita monga mwa kufuna kwake. Mulungu yekha amanena kuti tchimo ndi chiyani, ndipo ngati tikufuna kudziwa kuti tchimo ndi chiyani tiyenera kufunafuna malingaliro ake.
Mau a Mulungu amakamba za mfundo imeneyi momveka bwino. Ku Genesis 1:28 ndi 2:15-17 tikupeza udindo umene Mulungu anapatsa kwa munthu. Amayenera kulima ndi kuyanganira munda wa Edeni modalira Mulungu ndi kumvera Iye. Chizindikiro cha kumvera chinali kuletsedwa kwa kudya za mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa.
Koma munthu anachita chiyani? Anagwiritsa ntchito mpata woyamba umene anali nawo kuwonetsa kumvera ndi kudalira kwake ngati mpata woti asamvere Mulungu, komatu kuti asamvere mwadala. Ichi chinali chiyambi. Patapita zaka 3000 Mulungu anayenera kulemba m’Mau ake: “Yehova m’mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.
Anapatuka onse; Pamodzi anavunda mtima; Palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense” (Masalimo 14:2-3). Patapitanso zaka 1000 Mau a Mulungu anati: “Palibe m’modzi wakudziwitsa palibe m’modzi wakulondola Mulungu. Onsewa apatuka, pamodzi akhale opanda pake, palibe m’modzi wakuchita zabwino ndi palibe m’modzi ndithu” (Aroma 3:11-12). Kodi sizomveka bwino lomwe kuti chiweruzo cha Mulungu chikhale: “Onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu” (Aroma 3:23)?
KODI TCHIMO NDI CHIYANI?
Koma mungathe kunena kuti, “tikuyenera kuvomereza kuti nthawi zina timachita zinthu zolakwa. Koma sitimatha kuona kuti munthu ngakhale m’modzi angathe kuchita zabwino. Pali ndithu anthu ambiri amachita ntchito zabwino. Tangoganizirani anthu amene amapereka miyoyo yawo kuthandiza anthu ena. Ndipo ine mwachitsanzo ndikamadya ndi kumwa kapena kupita ku sukulu kapena ku ntchito, izi sizolakwika kuchita, sichoncho?
Kuziona mwakuthupi sizolakwika, koma kuzionanso mwauzimu zingathe kukhala zolakwika. Kudya nthochi sikolakwika koma mwana atadya nthochi yomweyo pamene mayi ake atamukaniza kumeneku ndiye kusamvera. Pamenepa timakhudza chindunji cha funso lakuti “Tchimo ndi chiyani?”
Munthu analengedwa ndi Mulungu ndipo analengedwa kuti amtumikire Iye. Tsono china chilichonse chimene munthu amachita chosiyana ndi udindo umenewu ngati wolengedwa komanso wopatsidwa udindo wotumikira Mulungu ndi tchimo. Timapeza izi mu 1 Yohane 3:4 “Tchimo ndi kusayeruzika” tchimo ndi mchitidwe uliwonse umene sulabadira ulamuliro wa Mulungu pa chilengedwe chake.
Mwachitsanzo kudya ngati kuchitika popanda kudalira Mulungu ndi tchimo. Ambuye Yesu ankadya pokhapokha Mulungu akamuuza kutero (Mateyu 4:4; onaninso Yohane 4:34). Ndi chifukwa chake Mau a Mulungu akutiuza kuti: “china chilichonse chosachokera pa chikhulupiliro ndi tchimo” (Aroma 14:23).
Tikatenga mlingo uwu pamoyo wathu, timapeza chiyani? Kodi ndi mchitidwe wanji umene tachita, ndi mau otani amene talankhula, komanso ndi malingaliro otani amene abwera mkati mwathu amene abwera pakumvera Mulungu kupyolera pafunso la mu mtima mwathu. “Ambuye, mufuna ine ndichite chiyani?” ngati sitingamalizitse ndi mau akuti – Palibe m’modzi! ndiye kuti zonse zimene tachita ndi tchimo!
Ichinso ndi chomwe Mau a Mulungu akunena “Palibe m’modzi wakuchita zabwino inde, palibe m’modzi ndithu” (Aroma 3:12). “Ndiponso kuti ndilingalire zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha” (Genesis 6:5). Ndi chifukwa chake Mulungu wolungama akuyenera kuweruza anthu. Ndi chifukwa chake Mulungu wachifundo akuyitana anthu onse kuti atembenuke kuti awapulumutse ku chilango choopsya chimene chikuwadikira.
KODI KUTEMBENUKA NDI CHIYANI?
Tsopano tikubwera pafunso lako lachiwiri — “Kodi kwenikweni kutembenuka mtima ndi chiyani?”
Liwu limeneli silimatanthauzidwa bwino kwenikweni, ‘Kutembenuka’ (nthawi zina kumatanthauzidwa ngati ‘kulapa’) sitanthauzo lake lenileni la chi Greek lomwe ndi “metanoia” limene linagwiritsidwa ntchito pachiyambi penipeni m’Mau a Mulungu. Palibe liwu ngakhale limodzi limene limapereka tanthauzo lenileni ku mau amenewa a chi Greek.
Kuchokera ku 1 Atesalonika 1:9 ndi zodziwikiratu kuti ganizo ili la ‘kubwerera’ likupezeka mu liwu limeneli. Pachiyambi anthu a ku Atesalonika anakhazikika m’moyo wawo wa mafano. Koma tsopano abwerera sakuyang’ananso mafano awo ndi kuti abwerera kwa Mulungu.
Koma ndime zina ngati Machitidwe 2:37,35.; 17:30,31; Chibvumbulutso 9:20,21 ndi ena otere amatsindika kuti kudziweruza wekha ndi moyo wakowako ndi zintchito zako pamaso pa Mulungu zikukhudzana ndi liwu limeneli la kutembenuka.
Ndiye tikhoza kunena kuti kutembenuka ndiko kupita kwa Mulungu, kudzichepetsa wekha pamaso pake pa kuvomereza kuti moyo wake sunali womvera Mulungu — ndi kuti iye ali wochimwa ndi wotsutsidwa. Kuonjezera pamenepa ndi kutinso ali wa chisoni chifukwa cha zimenezi.
Komabe ngakhale sichapafupi kupereka tanthauzo lenileni la kutembenuka, aliyense amene wabwera mu kuunika kwa Mulungu ndipo kuti waona chomwe ali pamaso pa Mulungu ndi kuti chigamulo chake ndi chotani alibe vuto lililonse pa ichi.
Mulungu amaona mtima ndi chikumbumtima, osati nzeru. Wokhoma msonkho anafuula “Ambuye mundichitire chifundo ine, wochimwa” (Luka 18:13) Koma Mulungu amene amayesa mitima, ndi “kudziwa zolingalira za mu mtima” (Ahebri 4:12), anadziwa kuti m’mau amenewa zonse zinalimo.
Osati mau amene timalankhula, ayi, koma momwe mtima wathu ulili pamene tikubwera kwa Mulungu zimanena ngati kutembenuka kwachitika mwa ife.
Ndipo tsopano ndifuna ndikufunse chinachake. Kodi ndiwe wotembenuka mtima? Kodi unapita kwa Mulungu ndi machimo ndi kutsutsika kwako, kuvomereza khalidwe lako lotayika kwa Iye?
Chonde usazengereze, koma tembenuka lero popeza za mawa sizidziwika.
MUTU 3
NDINGAPEZE BWANJI MTENDERE NDI MULUNGU?
Wokondedwa mzanga,
Ndinali wokondwa kumva kuti wadziona wekha kuti ndiwe wochimwa, wotayika ndipo kuti udzatayika mpaka kalekale utakhala kuti ukuonana ndi Mulungu tsopano. Komanso unavomereza machimo ako kwa Mulungu, Komabe sukudziwa ngati unakhululukidwa.
Ndipo pano ukufunsa kuti ukumva ngati kulapa kwako kunali kochepa komanso kutembenuka kwako sikunali kwakuya. Pamakhala masiku ena amene sumaganizirako ngakhale pang’ono.
Ndikutha kumvetsa malingaliro ako, popeza inenso ndinadutsamo mu zimenezi.
Kwa zaka zambiri (ndidakali wachichepere) ndinkadziwa kuti ndine wotayika. Masana sindinkaganizirako za izi kwenikweni, koma usiku ndikamagona ndimakhala ndi mantha. “Nditafa usiku uno, ndidzakhala wotayika mpaka muyaya” ndinkaganiza chomwechi.
Ndipo ndimalapanso kachiwiri machimo anga kwa Mulungu ndi kumufunsa kuti andikhululukirenso. Koma sindimalandira chitsimikizo kuti ndakhululukidwa. Nthawi ina mlongo wanga wamkulu anandiuza kuti wapeza mtendere. Ndinamufunsa chimene wachita, ndipo madzulo ake ndinachita zomwezo — koma popanda zotsatira.
Pamene ndinali ndi zaka 17 nditakhala pa kama wanga, nditafooka ndinaganiza, “kupemphera konse kuja sikukuthandiza. Kwa zaka zambiri tsopano wakhala ukufunsa Mulungu madzulo aliwonse kuti akupulumutse, ndipo palibe chosintha chilichonse.” Pa nthawi yomweyo Mulungu anandipatsa malingaliro akuti: Kodi sikunalembedwe kuti: “Ngati tivomereza machimo athu ali wokhulupirika ndi wolungama kutikhululukira machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse” (1 Yohane 1:9) Kodi sizoona zimenezi?
Indedi ndi zoona pakuti Mulungu sanama, ndinalingalira pomwepo Mulungu anandiunikira zomwe mauwa akutanthauza kwa ine. Zinatanthauza kuti machimo anga anakhululukidwa nthawi yoyamba yomwe ndinalapa moona mtima pamaso pa Mulungu.
Pa nthawi yomweyo mtendere unabwera mu mtima mwanga kapena kuti chikumbumtima changa chinapeza mtendere. Kuyambira madzulo amenewo ndinadziwa kuti machimo anga anakhululukidwa. Sindinakayikirenso, pakuti Mulungu ananena, sanatero kodi?
KODI TILAPE MOCHULUKA BWANJI?
Nanga ndi chifukwa chiyani zinanditengera zaka zambiri ndisanakhale ndi mtendere? Mosakayika, chimodzi mwa zifukwa zake ndi kuti kulapa kwanga sikunali kozikika ndi chikumbumtima cha tchimo langa chinali chosakula izi sizikutanthauza kuti Mulungu anayika mlingo womwe sakhululukira pamene chikumbumtima cha tchimo sichokwanira.
Palibe munthu anamvako kulapa mwakuya komanso kumva chikumbumtima cha tchimo pamene amalapa. Sitingadziwe mlingo wa machimo athu Pokhapokha titatembenuka mtima.
Komabe Mulungu safuna kuti ife timve nyengo ya kutayika kwathu.
Momwe kuya kwa chikumbumtima ichi chilili, ndiye kuti kutembenuka mtima kwathu kudzakhala kwakuya, kumvetsa kwa chiweruzo chimene chimatiyenera, ndiye kuti kulapa kwathu kukhala koona, ndiye kuti mpumulo ndi mtendere wathu sizikhala zakuya.
Kotero kuti Mzimu Woyera amagwira ntchito mu mtima mwa wochimwayo ndipo amafuna kubweretsa chikumbumtima chake mu kuunika kwa Mulungu pamenepo amamupangitsa kumvetsetsa nyengo yake yotayika ndi kuchuluka kwa machimo ake ndi kuti akadziwe chiweruzo cha Mulungu woyera ndi wolungama chimene amabweretsa pa ife. Komatu apa sipaphata penipeni pa nkhaniyi.
Chinthu chenicheni ndi chakuti ndimadziona ndekha monga ndilili osati kuyang’anira pa Mulungu, ndipo kuti Mau a Mulungu sanali okwanira pa ine. M’mene ndinaona machimo anga ndi kudziwa kuti ndinaipitsa chilichonse, ndinayenera kumvetsera liwu la Mulungu. Ndipo Mau a Mulungu ndi omveka bwino lomwe: “Ngati tivomereza machimo athu ali wokhulupirika ndi wolungama kuti atikhululukire machimo athu!”
Ndinkadikirira chinachake mumtima mwanga kapena m’moyo mwanga chimene chingandipatse chitsimikizo kuti ndalandira chikhululukiro. Koma ndinayenera kukhulupirira Mau a Mulungu amene amapatsa munthu aliyense wakuvomereza machimo ake chitsimikizo chakuti wakhululukidwa.
CHILUNGAMO CHA MULUNGU
Mulungu safanana ndi oweruza ofewa-mtima wa dziko lapansi. Ndi kotheka ife kuchita mogwirizana ndi oweruza otereyu ndi kuomboka mwachangu ku mlandu wathu kusiyana ndi wina amene sangathe kuchita zoterezi bwino lomwe.
Koma chikondi ndi chisomo cha Mulungu sizingathe kutsutsana ndi kulungama kwake. Ichi ndiye chinthu chodabwitsa pa uthenga wabwino. Mulungu yemweyo amene tsiku lina adzaonetsa chilungamo chake pa chiweruzo cha munthu aliyense wochimwa, koma tsopano akuonetsa chilungamo chake pa kukhululukira ndi kuchotsa zolakwa zonse pa wochimwa aliyense amene akubwera kwa Iye mwa chikhulupiriro mwa Ambuye Yesu.
“Pakuti m’menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza ku chikhulupiriro: monga kwalembedwa, koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro” (Aroma 1:17)“Komanso pakuonetsera kwa chilungamo chake nthawi yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu” (Aroma 3:26).
KULUNGAMITSIDWA
Indedi Mulungu akhoza kuchita molungama malingana ndi chilungamo chake. Ndi chifukwa chake munthu akadakhala wotayika pakadapanda maomboledwe a pamtanda. Chikondi cha Mulungu chimafuna kupulumutsa wochimwa ku chionongeko chosatha. Koma izi sizikanatheka, pakuti chilungamo chimayenera kuti wochimwa alangidwe. Komanso chikondi cha Mulungu sichingachite motsutsana ndi chilungamo chake.
Kenako chodabwitsa chinachitika chimene timawerenga ku Ahebri 10, Masalmo 40, ndi ndime zina. Chifuniro cha Mulungu chinali chakuti ochimwa onse apulumutsidwe (1 Timoteo 2:4). Ambuye Yesu anasandulika munthu nati “Onani, ndabwera Mulungu kudzachita chifuniro chanu!”
Anapita pamtanda kukathana ndi tchimo kamodzi kokha ndipo kunatha. Anakhala tchimo pamenepo, ndipo chiweruzo cha Mulungu pa tchimo chinamgwera Iye, ndi chilungamo cha Mulungu chinakwaniritsidwa pa chiweruzo chimenechi.
Koma Ambuye sanatenge chiweruzo chimenechi pa Iye yekha. Pakuti anali Woyera nthawi zonse, Wopanda banga, amene sanadziwa tchimo. Analangidwa m’malo mwa onse amene mwa chikhulupiriro adzamlandire Iye monga mpulumutsi wawo.
Tsopano Mulungu angathe kunena kwa wochimwa aliyense: “Yanjanitsidwani ndi Mulungu” (2 Akorinto 5:20). Si chikondi cha Mulungu chokha, komanso chilungamo cha Mulungu chimafuna kuti aliyense amene abwera kwa Mulungu mwa chikhulupiriro pa Ambuye Yesu alandire chikhululukiro.
KUUKA KWA AKUFA NDI CHITSIMIKIZO CHA CHILUNGAMO CHA MULUNGU
Koma ndikufuna kudutsa mu mfundo imeneyi mwatsatanetsatane. Ambuye Yesu anapita pamtanda, ndipo pamenepo anatenga mu thupi la Iye yekha machimo a onse amene anamulandira Iye ngakhale amene ati adzamulandire mtsogolo (1 Petro 2:24).
Pamenepo anakhala tchimo komanso anaweruzidwa ngati wochimwa (2 Akorinto 5:21; Aroma 8:3). Kodi chiweruzo chimenechi chinali chiyani tsopano? “Mphontho yake ya uchimo ndi imfa” (Aroma 6:23), Kulekana ndi Mulungu (Chivumbulutso 20:14-15). Pamtanda paja maola owopsya a mdima amenewa Iye anasiyidwa ndi Mulungu, ndipo pakutha pa maola amenewa anamwalira. Ndipo pamenepo anati, “kwatha”.
Koma Ambuye akadakhalabe m’manda atatsiriza ntchito ya chipulumutso? Chilungamo cha Mulungu, chimene chinabweretsa chiweruzo pa Iye, tsopano chinalamula kuti asakhalebe wakufa. Ntchito inatsirizika - chiweruzo chonse cha Mulungu chinatsanulidwa ndipo chilungamo cha Mulungu chinakwaniritsidwa ndi chifukwa chake Mulungu anamuukitsa kwa akufa (Aefeso 1:20).
Ichi ndi chitsimikizo kudziko lapansi komanso kwa ife kuti Mulungu walandira imfa ya Yesu m’malo mwathu ndipo wakhutitsidwa ndi imfayi (Yohane 16:8,10). Ambuye Yesu akadapanda kuuka kwa akufa ichi chikadakhala chitsimikizo chakuti ntchito siinatsirizike. Ndipo sipakadakhala chipulumutso chathu (1 Akorinto 15:17–18) kuchokera apa tikhoza kuona kuti kuuka kwa akufa ndiye maziko a Uthenga Wabwino ndipo kutsutsana ndi zimenezi ndi kuononga uthenga wabwino.
Ndi chifukwa chake Aroma 4:25 amati: “Amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu naukitsidwa chifukwa cha kuyesedwa wolungama kwathu” M’nyengo ino ya chisomo imene tikukhala Mulungu akuti kwa munthu aliyense: “Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu”
Komanso akunena kuti; “Ndipo ayesedwa olungama kwaulele, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Kristu Yesu; amene Mulungu anamuyika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m’mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake popeza Mulungu m’kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe” (Aroma 3:23-25).
Uthenga uwu ukupita “kwa onse” Koma maka “kwa onse amene akhulupira” (Aroma 3:22). Iwo okhawo alandira uthenga wa mulungu kuti iwo ndi osochera ndipo mwa chikhulupiriro alandira Ambuye Yesu ndi kukhala mbali yawo.
Tsopano Mzimu Woyera wagwira ntchito mu mtima mwanu ndipo mwaona machimo anu ndi kutayika kwanu. Munapita kwa Mulungu ndi kuvomereza pamaso pake chomwe muli ndi zomwe munachita. Mulungu anakulozerani kwa Ambuye Yesu ndi kuti: “anafera wochimwa; mukamulandira ndidzaika ntchito yake m’malo mwanu.”
Munamulandira Ambuye Yesu. Mukuyenera tsopano kukhulupirira kuti chomwe Mulungu wanena ndi choona, ndipo kuti machimo anu akhululukidwa. Sizikutengera kuti mukumva kapena simukumva kuti zonse zili bwino. Chinthu chokhacho chofunika ndi chakuti Mulungu wanena kuti zonse zili bwino.
Pamene m’ngelo wa imfa anapita ku Aigupto usiku wa Paska anapitirira nyumba imene anaona mwazi paphutu la khomo (Eksodo 12). Sizikutengera kuti mwana woyamba kapena a pabanja pake anaona kapena sanaone kuti zinthu zikasinthe.
Ngati adachita chimene Mulungu anawauza kuti achite ndiye kuti zonse zinali bwino. Kuti akhale ndi mtendere amayenera kukhulupirira kuti anali otetezedwa chifukwa Mulungu watero.
Chodabwitsa pa zonsezi ndichakuti Mulungu akulemekezeka mu zonse pamene akulandira wochimwa. Ndi zowonekeratu kuti chifundo chake, chisomo chake, komanso chikondi chake zikuonekera pamenepo.
Komatu sizokhazi ayi! Pamene wochimwa abwera kwa Mulungu mwa chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu, Mulungu amayika ntchito ya Ambuye m’malo mwake. Pakuti Ambuye Yesu ananyamula chiweruzo cha machimo, Mulungu amaona okhulupirira opanda tchimo ndi limodzi lomwe losaweruzidwa. Choncho Mulungu ndi wolungama pamene ayesa munthu wolungama ndi kumumasula ku chiweruzo chilinkudza.
Chilungamo chake ndi choonadi chake zimalemekezedwa, pakuti analonjeza izi m’Mau ake, sanatero kodi? Izi zimapereka tanthauzo labwino la 1 Yohane 1:9, kuti Mulungu ali wokhulupirika ndi wolungama kutikhululukira machimo athu ngati tiwavomereza.
MULUNGU ANADZIWA CHIMENE IFE TINALI
Tsopano mukuti: “Koma sindikuona kusintha kulikonse. Zoona zake ndi zakuti ndi kumachimwa kwambiri kuposa kale!”
Ndikuvomereza kuti ukuona machimo ambiri mwa iwe tsopano kuposa kale. Umu ndi momwe zikuyenera kukhalira, pakuti Mzimu Woyera wawalitsa maso ako. Koma Mulungu anadziwiratu iweyo bwino lomwe pamene unabwera kwa Iye.
Anadziwa mtima wako, moyo wako, machimo onse amene wakhala ukuchita, ndiponso machimo onse amene udzachite mtsogolo. Amadziwa ndipo ankadziwa kuposa momwe ungadziwire padziko lino lapansi. “Kukoma mtima ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka” pamene tinali “opusa osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m’dumbo ndi njiru, odedwa, odana wina ndi mnzake” (Tito 3:4,3).
“Pakut pamene tinali chikhalire ofoka … Kristu anawafera osapembedza ... Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo kuti pokhala ife chikhalire ochimwa Kristu adatifera ife ... Pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu” (Aroma 5:6-10; onaninso 2 Akorinto 5:20).
TILI NDI MTENDERE NDI MULUNGU
Ndipo tsopano, mutadziwa chimene munali, Mulungu anapereka Ambuye Yesu kuti mukhale ndi moyo wosatha ngati mudzakhulupirira mwa Iye. Iye ananena kuti mwayesedwa olungama kwaulele ngati mudzasendera kwa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa mwazi wa Ambuye Yesu (Aroma 3:23-25).
Ananena kuti mlandu wathu udzachotsedwa pakubwera kwa Iye mwanjira imeneyi, ndi kuti adzakhala wolungama akachita zimenezi. Kodi uwu siumboni owonekeratu kuti tsopano simulinso ndi chokutsutsani chifukwa munabwera kwa Iye mwa kuvomereza zolakwa zanu? Kumbali ya Mulungu, tsopano zonse zili bwino.
Kodi inuyo, n’kukhala ndi kanthu kumutsutsa nako Mulungu? ayi ndithu palibe. Simunabwera kwa Mulungu pozindikira kuti inu, osati Iye, munali wochimwa, ndipo kuti mumafuna kukhululukidwa?
Chifukwa chiyani tsopano mulibe mtendere? Mtendere ndi Mulungu zikutanthauza kuti palibe china chilichonse chimene mukuyenera kukonza pakati pa inu ndi Mulungu — kutanthauza kuti zonse zili bwino. Mulungu alibe kanthu kotsutsana nanu pakuti wakuyesani inu wolungama chifukwa munakhulupirira Ambuye Yesu ndipo pamenepo muli ndi gawo mu chipulumutso chosatha chimene Ambuye anatipezera (Aroma 5:1; Ahebri 9:12).
Ndipo inuyo mulibe mangawa alionse ndi Mulungu; mwayanjanitsidwa ndi Mulungu (2 Akorinto 5:20). Kotero muli ndi mtendere ndi Mulungu! Aroma 5:1 akunena kuti: “Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu”
KOMATU NDILIBE MTENDERE
Koma tsopano mukunena, “komatu ndilibe mtendere!” Izitu zikhoza kukhala chomwechi, pakuti simunavomereze mfundo yakuti mtendere ulipo kale. Ambuye Yesu anapanga mtendere. Iye ndiye mtendere wathu. Ndipo amalalikira mtendere umenewu kwa ife (Aefeso 2:16,14,17).
“Atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake” (Akolose 1:20). Pamene munamulandira Iye munali ndi gawo mumtendere umenewu. Koma kuti mumve kukoma kwa mtenderewu, mwayenera kukhulupirira kuti zimenezi ndi zoona. Mudzakhala ndi mtendere pomwepo mwakhulupirirapo kuti Mulungu akunena zoona pamene akunena kuti Ambuye Yesu anapanga mtendere pamtanda paja.
Mukuchita ngati zimene asilikali ena a ku Japan pa chilumba cha Pacific anapanga. Patapita zaka 5 chithereni nkhondo ya dziko lonse lapansi iwo amabisalabe kuganiza kuti nkhondo idakalipobe. Anali wokonzeka kuomberana ndi adani awo ndi zina zotero, monga momwe amachitira nthawi ya nkhondo. Chifukwa chiyani? iwo amaganiza kuti adakali mkatikati mwa nkhondo, pakuti iwo samakhulupirira nkhani yakuti nkhondo inatha.
Chifukwa chenicheni chomwe mulibe mtendere tsopano ndi chakuti simunakhulupirire kwathunthu Mau a Mulungu. Ukutu ndi kulephera kwakukulu pa inu. Koma pamwamba pa zonsezi ndi kusalemekeza Mulungu kuti simukhulupirira Mau ake. “Mulungu simunthu, kuti akaname” (Numeri 23:19).
Pamene inu mwangokhulupirira Mau ake monga pamenepo, mudzatha kumuyamika chifukwa cha zonse zimene wakupatsani inu, chifukwa cha chisomo chake chodabwitsa. Ndipo mudzamva mtendere mumtima mwanu komatu osati musanakhulupirire! Munthu amati “uyambe waona kenako ukhulupirire.” Mulungu akuti: “Uyambe wakhulupirira, kenako uwone”
Ndi mafuno onse abwino,
Ndine Mzako
H.L.H.
MUTU 4
KUMASULIDWA KU MPHAMVU YA UCHIMO
Wokondeka mzanga,
Tsopano chikumbumtima chako chapeza mpumulo mu ntchito imene Kristu adayitsiriza. Wavomereza machimo ako pamaso pa Mulungu ndipo wakhulupirira zimene Iye adanena zokhudza Ambuye Yesu Kristu ndi ntchito yake. Tsopano wazindikira kuti sudzafika ku chiweruziro, ndipo ukhoza kuyimba: “Machimo anga onse ochuluka m’mwazi wake asambitsidwa.”
Ngakhale izi zili chomwechi, kutengera pa zimene unanena zikuonetsa kuti ulibe chimwemwe chenicheni. Mwina unakhala ndi chimwemwe kamodzi kokha, koma tsopano ulibiretu chimwemwechi. Sindikuyeneranso kufunsa kuti chifukwa chiyani. Zomwe ine ndinadutsamo zimandiuza komanso Mau a Mulungu amavomereza za ichi.
Umakhala okhumudwa pa iwe wekha. Umaganiza kuti moyo wako ukhala wosinthiratu tsopano pakuti wapulumuka ndipo uli ndi mtendere ndi Mulungu. Koma wazindikira kuti izi sizili choncho! Malingaliro a uchimo amabwerabe m’maganizo ako.
Zolakwitsa zimene zinkaonekera mu khalidwe lako loyamba usanatembenuke zidakalipobe. Umakwiyabe ngati poyamba. Ndipo umaona ngati izi sizinayenere kukhala chonchi (apatu ukunena zoona) pakuti Mulungu sangavomereze zimenezi. Sumafuna kuchita zinthu zimenezi ndipo umayesetsa kuti usachite zimenezi.
Koma palibe chimene chikuthandiza — zinthu zikungoipirabe m’malo mwakuti zikhale bwino. Ndipo pamene ukuganiza kuti zinthu zikuyendako bwino mosakhalitsa umazindikira kuti zikuipiraipirabe monga kale. Wapemphera kwambiri kuti Ambuye akuthandize ukhale wogonjetsa tchimo, komaizi zikuonetsa sizikuthandiza.
Mwina ukumva mofanana ndi zimene Mlongo wina mwa Ambuye anandiuza, “Pamene ndikupemphera kwambiri ndi pamene zinthu zikuipiraipirabe.”
Ndinadutsakonso mu zinthu ngati izi pamoyo wanga. Zaka ziwiri zoyambirira nditapeza mpumulo mu chikumbumtima changa ndinali munyengo ngati imeneyi ndipo sindinafune kuuza wina aliyense kuti ndine wopulumutsidwa.
M’zaka zimenezo, mayi wanga anali m’modzi mwa anthu amene amandilimbikitsa kuti ndikuyenera kubadwanso kwatsopano, koma sindidawauze kuti ndinali kale wotembenuka mtima. Ndinaona kuti sandikhulupirira chifukwa cha m’mene amaonera machitidwe anga a zinthu.
Kodi izi zinachitika bwanji? Umu simomwe mwana wa Mulungu ayenera kukhalira, kuti moyo wake sumasinthika chifukwa cha utembenuka mtima kwake; kuti iye ngakhale sakufuna, komabe amachimwabe ndipo zotsatira zake amasokonekera!
Pali zifukwa ziwiri zochitira izi:
Sitimadziwa komanso kumvetsetsa tanthauzo lakuya la ntchito ya Ambuye Yesu monga momwe Mau a Mulungu amatiuzira.
Tikakhala ndi chidziwitso chimenechi, sitimazitengera kwa ife tokha ndi kuzikhadzikitsa m’miyoyo yathu — kutanthauza kuti sitimakhulupirira kuti chimenechinso ndi choonadi chifukwa Mau a Mulungu amatero.
MOMWE MUNTHU ALILI
Mu kalata yanga yomwe ndinalemba nthawi ya m’mbuyomu, ndinakuonetsa kuchokera mundime zoyambilira za kalata ya ku Aroma kuti anthu onse nachimwa ndipo kuti ali olakwa pamaso pa Mulungu. Komanso ndi zoona kuti munthu aliyense amene alandira Ambuye Yesu amalandira chikhulupiriro ku zolakwa zake.
Inde Mulungu amamuyesa wolungama iye ndi chifukwa chake wochimwa amene watembenuka akhoza kunena kuti: “Popeza tsonotayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu” (Aroma 5:1). Mulungu wapanga kuthekera konse kuti munthu wochimwa akhoza kupulumutsidwa.
Komabe, kuyambira pa Aroma 5:12 nkhani ina ikuyamba. Apa zambiri sizikunenedwa zokhudza machimo athu, zochita zathu za uchimo, koma akunena za momwe ife tilili. Kodi ndi chifukwa chiyani munthu sapanga kanthu kena kuposera kuchimwa? Chifukwa chakuti chilengedwe chake, mtima wake ndi zoipa.
“Mtima ndi wonyenga kupambana zinthu zonse, ndi wosachiritsika, angaudziwe ndani?” (Yeremiya 17:9). “Pakuti mkati mwake mwa mitima ya anthu mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa” akutero Ambuye Yesu (Marko 7:21-22).
Ndipo ku Tito 3:3 mtumwi Paulo akutipatsa chithunzithunzi cha momwe ife tilili: “Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu – mitundu, okhala m’dumbo ndi njiru odanidwa, odana wina ndi mnzake.” Palibe m’chitidwe wa uchimo umene ukutchulidwa apa, koma akukamba za chikhalidwe chathu.
MONGA MWA CHIFANIZO NDI CHIKHALIDWE CHA MULUNGU
Aroma 5:12-21 akutiuza chifukwa chimene tili ndi chikhalidwe cha uchimo chimenechi. Chifukwa ndi chakuti ndife ana a Adamu.
Adamu analengedwa mu chifanizo ndi chikhalidwe cha Mulungu (Genesis 1:26, 5:1). “Mu chifanizo cha Mulungu” izi zikutanthauza malo amene Adamu anapeza mu chilengedwe. Ngati wantchito wa Mulungu amayimira Mulungu padziko lapansi, ndipo pa chifukwa chimenechi anakhala mutu wa chilengedwe chonse padziko lapansi.
Ngakhale zambiri zasintha chifukwa cha kuchimwa ndi kusokonekera kumene kunabwera chifukwa cha zimenezi, Adamu komanso munthu wina aliyense obwera pambuyo pake adakali chifanizo cha Mulungu mu chilengedwe cha Mulungu (1 Akorinto 11:7).
“Mu chikhalidwe cha Mulungu” Izi zikutanthauza chiyero ndi chilungamo cha Adamu. Panali chikhalidwe chofanana pakati pa chilengedwe ndi Mlengi. Koma mwatsoka, chikhalidwe chimenechi sichinatenge nthawi. Adamu anachimwira lamulo la Mulungu nataya chiyero chake, nakhala wochimwa, wotsutsika.
Zambiri sizikunenedwa za Adamu atachimwa, ngakhale mbeu yake, kuti adakali mu chikhalidwe cha Mulungu. Mau amenewa akupereka chithunzithunzi pa chilengedwe chake chokha (Genesis 1:26, 5: 1; Yakobo 3:9).
CHITAPITA CHIFANIZO NDI CHIKHALIDWE CHA ADAMU
Genesis 5 imakamba momveka bwino pa mfundo imeneyi. Mu ndime 1 timawerenga kuti Mulungu analenga munthu m’chifanizo ndi m’chikhalidwe chake. Koma mu ndime 3 pamene Adamu anali ndi mwana wa mwamuna, mwanayu anali ‘m’chikhalidwe chake chitatha chifanizo chake’.
Atakhala monga wochimwa wotsutsika, wa chilengedwe chogwetsedwa kuchoka kwa Mulungu. Mwa ichi mwana aliyense wobadwa ali wochimwa kale mwa chibadwidwe, chifukwa ali ndi chilengedwe cha makolo ake.
Yobu adanena kuti; “Angachotse munthu wangwiro kuchokera ku choipa ndani? Palibe ngakhale mmodzi!” (Yobu 14:4). Davide anati: “Taonani mu zolakwa ndinatuluka, ndi mu uchimo mayi anga anandibala” (Masalmo 5:5).
Ndipo Aroma 5:12-21 akuomba mkota kuchokera ku mfundo imeneyi: Kudzera m’kuchimwa kwa Adamu ambiri anafa, pakuti imfa inachita ufumu kudzera mu kuchimwa kwa Adamu (ndime 15-17); zotsatira za kuchimwa kwa Adamu zinafikira anthu onse ku chiweruzo chawo (ndime 18); ndipo mwa kusamvera kwa Adamu ana ake onse anapezeka wochimwa (ndime 19).
M’makambidwe ena, chikhalidwe cha munthu aliyense akabadwa chimafanana ndi cha Adamu adakali wochimwa – wochimwa amene akudikira imfa, wothamangitsidwa m’munda mwa Edeni komanso pamaso pa Mulungu.
Ndime imeneyi tsopano imalankhula za momwe munthu alili osati za machimo amene wachita. Munthu asanachite tchimo lililonse chikhalidwe chake chimakhala kuti ndi cha uchimo kale ndipo amadikira imfa monga chiweruzo chake. Sikuti amakhala wotsutsidwa m’chibadwidwe chake.
Koma amakhala wotsutsika monga mwa machitidwe ake, m’machimo amene amachita. Mu Chivumbulutso 20:12 tikupeza kuti akufa anaweruzidwa monga mwa zintchito zawo, osati monga m’mene iwowo alili. Komabe momwe munthu alili zinamupangitsa kukhala operewera kukafika kumwamba.
Mulungu sangalole m’kupezeka kwake munthu amene ali ndi chikhalidwe cha uchimo. Mulungu amene ali woyera akuyenera kuthamangitsa kwa muyaya munthu wa chikhalidwe cha uchimo pamaso pake. Mulungu amene “ndiye kuunika ndipo mwa Iye monse mulibe mdima” (1 Yohane 1:5), sangalole aliyense amene ali “mdima” (Aefeso 5:8) pamaso pake.
Akuyenera kuwaponya iwo “ku mdima wakunja, kumenenso kudzakhala kulira ndi kukukuta mano” (Mateyu 8:12;22:13). Ndipo ngati Ambuye Yesu akadakhala kuti sanatsirize ntchito ya chipulumutso, palibe munthu akadatha kufika kumwamba — kuphatikizako ana amene amafa adakali ang’ono ndipo sanachitepo tchimo lina lililonse.
KUKHULULUKIDWA KWA MACHIMO SIKUKUKWANIRA!
Kuchokera apa tikuona kuti sizokwanira kungokhululukidwa machimo. Ngati Ambuye Yesu akanatenga machimo anga pamtanda, Koma osachitapo kalikonse kwa ine, ndiye kuti sindikadatsutsidwanso chifukwa cha machimo anga, komabe ndikadakhala wotayika kwa muyaya. Mulungu akhoza kukhululukira machimo; koma osati machitidwe oipa, chikhalidwe cha uchimo.
Mulungu munjira ina iliyonse yothekera wapereka mpata kwa munthu kuti awone ngati muli chinthu chabwino mwa iye. Panali mpata onse chisanachitike chigumula, Mulungu asanapereke lamulo lililonse, asanayambe kuletsa zinthu ndiponso chitatha chigumula, pamene Mulungu anaika boma kuti lithane ndi zoipa (Genesis 9:5-6).
Kenako anapatula Israeli kuti akhale anthu ake ndipo mwakukoma mtima kwake anabwera kudzakhala pakati pawo (Deuteronomo 4:6-8). Zitatha izi anawapatsa iwo oweruza, aneneri ndi mafumu. Anawalera iwo mwa mwambo wake. Ndipo pomaliza, Iye mwini “Mulungu anaonekera m’thupi,” anabwera padziko mwa chisomo.
“Mulungu anali mwa Kristu ali kuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawerengera zolakwa zawo” (2 Akorinto 5:19). Kenako chinachitika ndi chiyani? “Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamulandire Iye” “Ndipo kuunikaku kunawala mumdima, ndi mdimau sunakuzindikira.” Ndipo anthu anakonda mdima kuposa kuunika” (Yohane 1:11;5:3:19).
Munthu anali wochimwitsitsa kufikira anakana Mulungu amene anadzionetsera yekha mwa chisomo, inde, mpaka anatsogozedwa “Mulungu anadzionetsera yekha mu thupi” (1 Timoteo 3:16) pa mtanda. Pa mtanda paja zinaonekera kuti munthu anali wotayikiratu ndi woyipa, ndipo Mulungu sakadachitira mwina kuposa kumuweruza.
Ichi ndi chifukwa chake Ambuye Yesu sakunena ku Yohane 3: “pokhapokha machimo a munthu akhululukidwe, sadzaona ufumu wa Mulungu” Koma akunena kuti “ngati munthu sabadwa kwatsopano sakhoza kuona ufumu wa Mulungu”.
YANKHO LA MULUNGU
Koma ku Aroma 5:12-21 tikupeza yankho la umulungu pafunso lovutali. Munthu woyamba, Adamu woyamba, anapereka udindo wa uchimo kwa onse okhala m’banja lake (kunena kuti kwa anthu onse obadwa) atagwa mu uchimo. Kenako Mulungu anatumiza Ambuye Yesu Kristu, Munthu Wachiwiri, Adamu Wotsiriza (1 Akorinto 15:45 - 47), kudziko lapansi kuti apereke moyo ndi udindo umene anaupeza atamaliza ntchito yake pa mtanda kwa onse amene ayanjana naye.
Tsopano pakubwera funso; Kodi udindo umenewu ndi uti? Ambuye Yesu anasenza machimo athu pa mtanda paja pansi pa chiweruzo cha Mulungu (1 Petro 2:24). Koma sanangochita izi zokha! Aroma 8:3 amanena kuti “Mulungu anatumiza mwana wake wa Iye yekha m’chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo mthupi” ndipo ku 2 Akorinto 5:21 timawerenga kuti: “Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu, kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.”
Ndime ziwiri zimenezi sizikunena za machimo athu, machitidwe athu oipa, koma uchimo wathu – mfundo zoipa, gwero la machimo, chikhalidwe chathu choyipa. Aroma 8:3 akulankhula za “thupi la uchimo” ndi “uchimo m’thupi” kufotokoza uku kukugwiritsidwa ntchito pa mutu 5 mpaka 8 ya buku la Aroma kulongosola bwino lomwe za chibadwidwe chathu choipa.
Mu ndime zimenezi, akunena kuti Mulungu anampanga Ambuye Yesu, pamene anali pa mtanda kukhala tchimo. Ambuye Yesu sikuti anangosenza chabe machimo athu, koma anapangidwanso kutenga malo a chibadwidwe chathu cha uchimo pomwepo.
Ndipo pamenepo Mulungu anamuweruza amene sanadziwa uchimo ngati kuti anali munthu wochimwa ndi wachibadwidwe cha uchimo, chiweruzo cha Mulungu pa chibadwidwe chochimwa cha munthu komanso zochita zake zochimwa zinatsanulidwa pa Ambuye Yesu. Ndi chifukwa chake Ambuye Yesu anafa ndi kuikidwa m’manda.
ADAMU WOTSIRIZA
Koma mphamvu ya Mulungu inamuukitsa iye kwa akufa (Aefeso 1:20). Ichi ndi chitsimikizo kuti chilungamo cha Mulungu chakwaniritsidwa, pa chiweruzo cha machimo athu komanso chibadwidwe chathu cha uchimo.
Ambuye Yesu wauka ndipo chiweruzo chadutsa. Akuyima pamaso pa Mulungu mu udindo watsopano, wa Iye yekha amene wadutsa mu chiweruzo cha Mulungu pa machimo ndi uchimo, koma Iye woukitsidwa ndi Mulungu mwini — chitsimikizo kuti chiweruzo chakwaniritsidwa — ndipo kuti tsopano akukondwera ndi moyo wa kuuka kwa akufa. Uwu unali udindo wa Munthu Wachiwiri, Adamu Wotsiriza, pamene anakhala munthu wa banja latsopano, banja la Mulungu.
Aroma 5:12-21 imatiuza kuti yense amene wayanjanitsidwa ndi Iye amakhala naye pa udindo umenewu. Chisomo cha Mulungu ndi mphatso yaulere mwa chisomo, imene inapangidwa ndi munthu m’modzi yekha Ambuye Yesu, yafikira kwa ochuluka (ndime 15). Kuchita kwa kukondera kuli ndi milandu yake yotitengera ku chilungamitso (ndime 16). Onse amene analandira kuchuluka kwa chisomo, ndi mphatso ya ulere ya chilungamo, amalamulidwa m’moyo wawo ndi Ambuye Yesu yekhayo (ndime 17).
Ntchito ya Ambuye Yesu inatsatira mu kuyesedwa wolungama m’moyo, ndi mwa kumvera kwake ambiri adzayesedwa olungama (ndime 18-19). Chisomo chilamulira mwa chilungamo cha moyo wosatha (ndime 21). Ngati tikhala ofanizidwa ndi Iye m’maonekedwe a imfa yake, chomwechonso tidzakhala mu chiukitso chake (Aroma 6:5). Aefeso 2:5,6 ikupitirizabe. Taukitsidwa ndi Iye ndipo tikhala naye m’mwamba mwa Kristu Yesu.
Tsopano tikudziwa ntchito ya Ambuye Yesu ikutanthauza zambiri kwa ife koposa kukhululukidwa kokha kwa machimo. Pamene wochimwa apita pamaso pa Mulungu navomereza machimo ake nakhulupirira pa Ambuye Yesu, Mulungu amamubweretsa iye m’banja la Mulungu, ndiye kuti ali wa Ambuye Yesu. Ntchito yonse ya Ambuye Yesu imakhala m’manja mwake.
Izi zikutanthauza kuti chilango cha machimo ake (machitidwe ake a uchimo) zinanyamulidwa pa mtanda paja, ndi machimo ake alipidwa. Koma chibadwidwe chake cha uchimo chinaweruzidwa ndiponso chinafa mwa Ambuye Yesu, pa mtanda. Tsopano ali ndi gawo mu chiukitso cha Ambuye Yesu.
Adamu wotsiriza (Mzimu woukitsidwa — 1 Akorinto 15:45) wapumiramo mwa Iye ndipo wapereka chiukitso cha moyo wa Iye yekha (Yohane 20:22). Tsopano ali ndi moyo wosatha, Ambuye Yesu mwini ndiye moyo wake (Yohane 3:15-16; 1 Yohane 1:1-2; 5:11-13,20).
KUFA NDI KRISTU
Tikamvetsetsa chimenechi, sitimayeseranso kudzikonza tokha. Timazindikira kuti ndi zosatheka kudzikonza pa chimene Mulungu wachisiya kuti ndi chopanda pake. Timazindikiranso kuti Mulungu wabweretsa ife mu imfa ya Ambuye Yesu pa mtanda. Tinavomereza izi pa ubatizo pamene tinabatizidwa mu imfa ya Kristu Yesu ndi kuikidwa ndi Iye mwa ubatizo wa imfa (Aroma 6:3-4).
(M’mene choonadi ichi chimabisikira ndi pamene munthu walandira ubatizo ongowaza, osati onyikidwa!). Timadziwa kuti Mulungu amangoona ife m’moyo watsopano, umene sungachimwe. Ndipo timadzionanso tokha moteremu — timadzidziwa tokha kuti tili akufa ku uchimo ndi amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu (Aroma 6:11).
Sitikuyenera kulimbana ndi uchimo umene uli mwa ife. Palibe pamene timapeza kuti m’Kristu akuyenera kutero. Koma kuti kupanga mosiyana ndi izi. Tikuyenera kuziona tokha akufa ku uchimo. (Ahebri 12:4 sikulankhula za uchimo okhala mkati koma tchimo la m’dziko lomwe lili pa udani ndi ife).
Zoonadi zake ndi zakuti tchimo lili mwa ife limapangika lokha kudziwika. Likufuna lidzionetsere lokha kuti lidakali ndi moyo, koma sitikuyenera kuvomereza zimenezi. Sitikuyenera kulimvera, koma m’malo mwake tikuyenera kuyang’ana kwa Ambuye Yesu.
Pamene tchimo likugwira ntchito mu mtima mwanga ndi kufuna kuti ndilimvetsere, sindikuyenera kulimvera — ndikuyenera kutembenuza malingaliro anga kwa Ambuye Yesu. Panthawi yomweyo ndachita izi, sindiganiziranso zokhudza tchimo.
Ndi pakuyang’ana kwanga pa Ambuye Yesu, moyo watsopano ukhoza kuwonekera mwa ine “Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalilole ulemelero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera ku ulemerero kunka ku ulemelero monga ngati kuchokera kwa Ambuye mzimu” (2 Akorinto 3:18).
Ndikachita zinthu izi Mzimu Woyera amene amakhala mwa ine, adzamenya nkhondo ndi thupi (chibadwidwe cha uchimo) pa Iye yekha (Agalatiya 5:17). Iyitu sintchito yathu. “Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu” (Aroma 6:11).
ZOKUMANA NAZO
Chifukwa chiyani tsopano okhulupirira ambiri amabuula ndi mphamvu ya uchimo monga momwe ndalembera kumayambiriro kwa kalatayi? Komanso ndi chifukwa chiyani palibe okhulupirira ngakhale m’modzi amene sadziwa za nyengo imeneyi komanso nkhondo yolumikizana ndi izi potengera zimene takumana nazo?
Sizoona, monga m’mene nthawi zina amanenera, kuti nkhondo iyi yayenera kutha moyo wake onse wa okhulupirira. Tiyamika Mulungu, izi sizili choncho. Ambuye Yesu anapeza chipambano pa Satana ndi uchimo. Aliyense amene ali ndi mbali mwa Iye akhoza kuima pa ufulu (Agalatiya 5:1,13,16) ndipo akhoza kukhala moyo wa chigonjetso (Aroma 8:1-4).
Yense wakukhazikika pa Aroma 8:1-11 ngati chikhalidwe cha moyo wake, ali mfulu ku mphamvu ya Satana, tchimo komanso imfa. Chipatso cha Mzimu chimapezeka mwa iye (Agalatiya 5:22-23) ndipo kuyesedwa wolungama kumene chilamulo chimafuna kumakwanitsidwa mwa iye (Aroma 8:4).
Koma yense mwa ife amadziwa nkhondo iyi chifukwa mamasulidwe akhoza kudziwika kupyolera mu kukumana ndi zimenezi. Pamene wina watembenuka mtima amaona machimo ake ndipo amatanganidwa nawo, chifukwa chiweruzo cha Mulungu chili patsogolo pake. Amalandira moyo watsopano ndipo amakhala ndi chifuniro chatsopano chimene chimafunitsitsa kutumikira Mulungu.
Amafunitsitsa chifuniro cha Mulungu, nafuna kuchita monga mwa lamulo. Ndi njira yokhayi imene amaphunzira chibadwidwe chake cha uchimo, chikhalidwe chake. Aroma 7 akukamba za chimenechi kwa ife.
M’ndime zinayi zoyambirirazo tikuona chiphunzitsochi ngati poimikika pathu. Timafa pakupereka ulemu ku lamulo, ndipo tinalumikizika kwa munthu wina, ndiye Kristu woukayo. Ndime 5 ndi 6 ikutichotsa ku chiphunzitso kutifikitsa ku zokumana nazo.
Chokumana nacho choyamba ndi chakuti lamulo lilibe mphamvu. Lili loyera, lolungama, komanso labwino. Linali “lamuyaya” pakuti “yense amene achita malamulowo adzakhala ndi moyo!” Koma zimene ndaona ndizakuti lamulo limagwira ntchito ya imfa pa ine, pakuti mwa zolamulira zake, kukhumba zonyansa kwauka mu mtima mwanga, ndipo lamulo limakana kukhumba zonyansa. Tsopano zimenezi zinandibweretsa ku kumvetsa kwanga kwa chibadwidwe chakale Pakuti ndidziwa kuti mkati mwanga, ndiko mthupi langa, simukhala chinthu chabwino” (ndime 18).
Komabe, chokhacho chakuti ndikufuna kuchita zabwino, komabe ndikuchita zoipa zimene sindifuna, zimanditsogolera ku kusiyanitsa pakati pa “INE” amene ndikufuna kuchita zabwino, inde, ngakhale kufunitsitsa chilamulo cha Mulungu pa munthu wamkati mwanga (ndime 22), ndiponso mphamvu ya mkati mwanga, uchimo, umene umandipangitsa kuchita zoipa (ndime 20).
Ndipo ndimafika ku chizindikiritso chenicheni kuti ndine kapolo wa tchimo la mkati mwanga. Ndi “lamulo la uchimo” lamulo lokhazikitsidwa limene limandipanga kukhala wochimwa, ndipo sindikhalanso ndi mphamvu yotsutsana nalo — ndine kapolo wake wa lamulolo.
Mzimu Woyera amandibweretsa ku chizindikiritso kuti ndili wosowa chiyembekezo mu chitayiko changa, ndipo ndimafuula: “Munthu wosauka ine, adzandilanditsa ndanim’thupi la imfa iyi?” (ndime 24). Pamenepo panabwera yankho kuchokera m’Mau a Mulungu mu ndime 25: “Ndiyamika Mulungu mwa Kristu Ambuye wathu.”
MAMASULIDWE
Ndinamasulidwa ku thupi ili laimfa! Linaweruzidwa mwa Kristu pa mtanda (ndime 3). Sindikhalanso ndi moyo koma Kristu akhala ndi moyo mwa ine (Agalatiya 2:20). Ndili mwa Kristu ndiye kuti ndili malo amodzi amene Iye anatenga atauka. Tsopano ndilibe kutsutsidwa (Aroma 8:11).
Mzimu Woyera wagwira ntchito ya moyo watsopano mwa ine, moyo umene siwochimwa — ayi, sungachimwe — koma uli m’chiyanjano ndi Mwini Wake (Yohane 3:5,6). Kuonjezera apo Mzimu Woyera monga munthu anakhala mwa ine ndipo ndi mphamvu imeneyi inapangitsa moyo watsopano kukagwira ntchito monga mwa magwiridwe ake (1 Akorinto 6:14; Yohane 4:14; 7:38-39).
Komanso ndi amene amatenga pa Iye yekha nkhondo yolimbana ndi thupi (Agalatiya 5:17). Ndiye kuti chilamulo (lamulo losasinthika) la Mzimu wa Moyo mwa Kristu Yesu landimasula ine kuchoka ku chilamulo cha uchimo ndi imfa (Aroma 8:12; onaninso Aroma 7:23 ndi kusiyanitsa). Sindirinso m’thupi (chibadwidwe changa choyamba). Koma mwa Mzimu.
Malo anga akudziwika ndi kupeza kwa moyo umene Mzimu Woyera wandipanga kupyolera m’kubadwanso mwatsopano (Yohane 3), komanso kukhala kwa Mzimu Woyera mwa ine (Aroma 8:9). Nthawi yomweyo izi zikutanthauza kuti ndili wake wa Kristu ndipo kuti ndine Mkristu.
Ichi ndicho chikhalidwe chenicheni cha wokhulupirira: womasulidwa kwa Satana, uchimo komanso imfa, ali mfulu kukatumikira Mulungu, komanso mfulu wokhala ndi chiyanjano chopanda malire ndi Mulungu (1 Yohane 1:3-4).
Mulungu atithandize iwe ndi ine kuti tikhale m’moyo umenewu nthawi zonse.
Mafuno onse abwino, ndine mbale wako mwa Ambuye Yesu.
H.L.H.
Mutu 5
KODI MULUNGU ANAYIKIRATU ANTHU KUTI AKATAYIKE?
Wokondedwa m’bale,
Unasokonezeka pang’ono ndi munthu wina amene ananena kuti; “pakuti sudziwa ngati uli wosankhidwa sungazindikire pano padziko lapansi ngati unapulumutsidwa kapena ayi.”
Chabwino, ukadatha kumuyankha mosavuta kuchokera m’Baibulo. Mau a Mulungu akuti, “yense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale nawo moyo wosatha” (Yohane 3:16). Ngati tsopano Mulungu akulankhula choonadi, ungathe kuchidziwa choonadicho. Ndipo palibe ngakhale m’modzi akhoza kukana kuti Mau a Mulungu amalankhula choonadi.
Ndinafunsapo munthu wina amene amanena chimodzimodzi, naganiza kuti mtumwi Paulo anali ndi Mulungu ndipo anawerenga buku la uphungu wa Mulungu mwini. Iye nayankha kuti sakuganiza choncho. Kenako ndinam’funsanso “Nanga ndi chifukwa chiyani tsopano analemba kwa anthu a ku Atesalonika “podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, chisankhidwe chanu” (1 Atesalonika 1:4)!
Zimatheka bwanji m’makalata ake onse, kulembera anthu ndi kuwatchula kuti oyera mtima?” Sanathe kundiyankha, koma tsiku lotsatira anandipeza nanena, “tsopano inenso ndadziwa kuti ndine wopulumutsidwa.”
Zoonadi, Mau a Mulungu amalankhula momveka bwino zokhudza kusankhidwa. Ndi mwana wa Mulungu wotani amene sanawerengeko mothunthumira ndime ngati Aefeso 1:4-5, Aroma 8:29-30; 1 Petro 1:2 ndi zina zotero, kenako ndi kulambira Mulungu wake chifukwa cha chisomo chotere?
KUSANKHIDWIRATU
Mwatsoka munthu sanakhale nacho chimene chalembedwa m’Mau a Mulungu, koma anavomereza malingaliro ake kudutsa chimenechi ndi kudzilembera yekha chimene chimatchedwa mfundo zodziwikiratu. Zotsatira zake ndi zakuti munthu amachita zinthu zosiyana ndi Mau a Mulungu zimene zili mwachidziwikire, zosapereka ulemu kudzina lake.
Chiphunzitso chokhudza kusankhidwiratu kwa anthu onse ndiko kuonjezera kwa chithunzithunzi cha ulemelero chimene Mau a Mulungu amatipatsa monga mwa kusankhidwiratu.
Chiphunzitso cha kusankhidwiratu chimanena kuti Mulungu anasankhiratu anthu ena ku chipulumutso cha muyaya, ndipo amanena kuti Aroma 9:8-23 ndi umboni wa mfundo imeneyi, kuti Mulungu anachita chisankho chakukana ena. Kotero mukuyenera kuwerenganso ndime imeneyi.
CHISOMO — SI CHA AYUDA OKHA
Mitu isanu ndi itatu yoyambirira ya buku la Aroma tikupeza nyengo imene munthu amakhala komanso yankho la Mulungu pa nyengo imeneyo monga m’mene zafotokozedwa kwa ife. Munthu ali wosochera ndi wopanda chiyembekezo. “Pakuti palibe kusiyana; pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere ndi chisomo chake” (Aroma 3: 22-24).
Ngati onse apulumutsidwa potengera chisomo chokha, ndiye kuti chisomochi sichikukhudza Ayuda okha. Chisomochi chimakhudzanso anthu amitundu ina, amene sanali Ayuda.
Komatu Ayuda sakanachipeza chisomochi paokha. Iwo anali ndi malo abwino ndipo anafunitsitsa kudzisungira okha chisomochi. Ndi chifukwa chake udani wawo waukulu unaonekera pamene Uthenga omwewu umalalikidwa kwa amitundu — onani, mwa chitsanzo, Machitidwe 13:45-50; 15:1; 17:5; komanso 28:25-29.
Ku Aroma 9 mpaka 11 mtumwi akuyankha mafunso otsatirawa: Ayuda ndi Amitundu, onse ali mlingo umodzi potengera Uthenga Wabwino; koma Ayuda anaikidwa mwa chikhalidwe kukhala ndi malo apadera pa maso pa Mulungu. Kodi madera awiri amenewa akugwirizana bwanji?
MBEU YA ABRAHAMU
Mfundo yoyamba imene Ayuda amalimbikira ndi yakuti iwo anali mbeu ya Abrahamu. Izitu ndi zabwino, anatero mtumwi, koma mukuyenera kukumbukiranso Ismayeli, pakuti nayenso anali mbeu ya Abrahamu. Koma ngati munganene kuti mai ake a Ismayeli anali mzakazi chabe, chabwino, nanga Esau, Aluya.
Yakobo ndi Esau tate wawo anali m’modzi komanso mayi m’modzi. Anali amapasa. Komabe Esau ngakhale anali wamkulu, sanakhale wa mbeu ya anthu a Mulungu — osati chifukwa chakuti Yakobo anali wopambana. Iwo asanabadwe, Mulungu anali ataneneratu kuti wamkulu adzatumikira wamng’ono.
Kotero sikunatengera chifukwa chimenechi kuti Ayuda akhale ndi mwayi wopezeka pa malo amenewa, koma zinatengera ulamuliro wa Mulungu. Ngati akufuna kugwiritsa ufulu wina ulionse, akuyenera kuganiziranso kuti Aluya ndi anthu a Mulungu, koma zimenezi mwachidziwikire sangapange.
Koma ngati anali anthu a Mulungu potengera ulamuliro wa Mulungu okha, nanga Mulunguyo alibenso mphamvu yovomereza anthu enawo ku mdalitso wake?
Kotero tingathe kuona kuti palibe funso lokhudza kusankhidwa kapena kukanidwa kwa muyaya, koma iyi ndi nkhani yokhudza maudindo okhala nawo pansi pompano.
NDINAKONDA YAKOBO, NDIPO NDINADANA NDI ESAU
Mau amenewa omwe akupezeka pa ndime 13 akhala akugwiritsidwa ntchito kwambiri pofuna kuteteza chiphunzitso cha kukanidwa. Anthu amene amachita zimenezi amaphatikiza ndime 12 ndi 13. Ndi zoonadi Mulungu analankhula zimene timawerenga pa ndime 13 pamene anawa anali asanabadwe — koma osati asanakhazikitsidwe maziko a dziko lapansi, monga momwe timawerengera ku Aefeso 1:4.
Apatu akufotokoza za mipando yopezeka padziko lapansi, ndipo Mulungu ananena izi ana aja atangosala pang’ono kubadwa (ndime 11). Koma ndime 13 inatengedwa kuchokera ku Malaki 1. Mulungu ananena izi zaka 1400 zitapita chimwalirire Yakobo ndi Esau, kutanthauza kuti amadziwa miyoyo imene iwo ndi mbeu yawo anakhala.
Ku Ahebri 12:16,17 Esau akutchulidwa munthu wa chigololo ndi wamnyozo, amene anagulitsa ukulu wake chifukwa cha mtanda umodzi wa chakudya, amene sanapeza malo akulapa. Kodi pali chodabwitsa chilichonse Mulungu kumutchula munthu wotereyu kuti adana naye? “Mudana nawo onse akuchita zopanda pake” (Masalmo 5:5).
Kenako tifika pa ndime 15 ya mutu wathu: “Ndidzachitira chifundo amene ndim’chitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.” (Mau amenewa anatengedwa kuchokera ku Eksodo 33:10). Anthu anadzipangira iwo okha fano la ng’ombe ya golide ndipo anam’kana Yehova (Eksodo 32:4).
Anadzisankhira chiweruzo (Eksodo 32:10). Koma Mose anawapembedzera iwo. Kenako Mulungu anaonetsa chisomo chake ndipo anawakhululukiranso anthu ake. Apatu mau amenewa akuonetsera poyera kuti Mulungu amaonetsera chisomo ngakhale panyengo imene wakonza kale chiweruzo.
Chinali mwa chisomo cha Mulungu kuti a Israeli akhale anthu a Mulungu. Koma mau amenewa angathe kukhala bwanji chitsimikizo chogwirizana ndi chiphunzitso cha kukanidwa?
Ndime 15 ikutsimikizira za mfundo ya chisomo. Pamenepa onse anali pansi pa chiweruzo, chisomo cha Mulungu chokha chingathe kubweretsa chiombolo. Chingachitike ndi chiyani kuti munthu kuyambira lero kupita mtsogolo asadzachimwenso — tingoyerekeza kuti wachitadi zimenezi! Akuyenerabe kupita ku chiweruzo chifukwa cha machimoamene wakhala akuchita
Ine mzako
H.L.H.
m’mbuyomu. ?
MULUNGU AMAUMITSA MITIMA YA ANTHU ENA
Ndime 17 ikuchokera pa Eksodo 9:16. Mulungu akumuuza Farao kuti aumitsa mtima wake, cholinga kuti aonetse mphamvu yake pa iye. Choyamba, tikuyenera kuwerenga zimene zinachitika zisanafike izi. Ku Eksodo 5:2 Farao akuti: “Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israeli apite?
Sindim’dziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israeli apite.” Ndipo iye anaonjezabe ntchito imene ana a Israeli amagwira (Eksodo 5:7). Ngakhale Mulungu anamuonetsera zozizwa ndi chiweruzo, komabe iye sanamvere chifuniro cha Mulungu. Ndipo Mulungu anati: “Tsopano ndidzaumitsa mtima wako kuti kulemera konse kwa chiweruzo changa kugwere pa iwe.”
Ndi zoonadi kuti Mulungu analankhuliratu za izi kuti adzaumitsa mtima wake (Eksodo 4:21), pakuti anali atadziwiratu kuti Farao sadzamvera Mulungu. Iye amadziwiratu mtima wa Farao (Eksodo 3:19).
Koma atalankhula mobwerezabwereza ndi Farao komanso atamutumizira zozizwa ndi miriri yochuluka, ndipo Farao kwa nthawi yochuluka atanena kuti alola a Israeli kuti apite, koma nthawi zonse iye amaphwanya lonjezano lake, pamenepa ndi pamene Yehova anaumitsa mtima wake (Eksodo 9:12). Pamenepa ndi pamene Mulungu analankhula mau amenewa kwa Farao.
Ndi zoonadi kuti Mulungu nthawi zina amaumitsa mitima ya anthu. Anapanga izi ndi Farao. Komanso nthawi zina lerolino amapanga chimodzimodzi. Komanso mkwatulo wa mpingo ukadzangochitika adzachita chimodzimodzi kwa onse amene anamva Uthenga Wabwino, koma sanauvomereze (2 Atesalonika 2:11). Koma Mulungu sachita zimenezi asanapereke mpata kuti munthu atembenuke (Yobu 33:14-30). Izitu zikusiyana kwambiri ndi zimene chiphunzitso cha kukanidwa chimafotokoza.
MULUNGU ALI NDI ULAMULIRO M’MACHITIDWE AKE
Ku Aroma 9:19-21, tsopano funso lofunika limene tikuona ndi lakuti, kodi Mulungu alibe ufulu wakuchita monga mwa chifuniro chake ku chilengedwe chake? Ngati Mulungu atafuna kupanga wina kukhala chotengera cha ulemu ndi wina chotengera chopanda ulemu, kodi alibe ufulu wakuchita zimenezi? Kodi chilengedwe chingathe kum’zenga mulandu Mlengi wake pa zimenezi?
Monga Mlengi, Mulungu ali ndi ufulu wakupanga chimene afuna ndi chilengedwe chake. Ali ndi ufulu wa kukhululukira wina ndi kutumiza wina ku chionongeko cha muyaya. Koma Mulungu sanachite chisankho cha kugwiritsa ufulu umenewu. Mulungu ndi Kuwala komanso Chikondi, ndipo sapanga zosemphana ndi zimene Iye ali.
Ndime 21 ndi imene imafotokoza za izi mwachindunji. Ndi chithunzithunzi cha Yeremiya 18. Pamenepa Mulungu anagwiritsa ufulu wake wakuchita zimene anafuna kuchita ndi Israeli. Woumba anaumba mbiya ya dothi, koma pamene inasokonekera anaumbanso mbiya ina ndi dothi lomwelo. “Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Nyumba ya Israeli inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? ati Yehova. Taonani monga dothi m’dzanja la woumba, momwemo inu m’dzanja langa, nyumba ya Israeli.” (Yeremiya 18:5,6).
Koma Mulungu amagwiritsa bwanji ufulu umenewu? “Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga; ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chawo, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire. Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wake ndi kuuoka; koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo
ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire.” (Yeremiya 18:7-10).
Ngati munthu walapa zochimwa zake ndipo watembenuka mtima, Mulungu amasintha chiweruzo chake chimene amafuna kupereka ndi kuonetsera chisomo. Mpaka lerolino Mulungu akugwiritsabe ulamuliro umenewu!
CHOTENGERA CHA MKWIYO CHIKUYENERA CHIONONGEKO
Aroma 9:22,23 ikutsimikizira chinthu chimenechi, ngakhale kuti ndime imeneyi imatengedwa ngati umboni waukulu wa chiphunzitso cha kukanidwa. Koma kunena zoona ndi umboni waukulu wotsutsana ndi chiphunzitso chimenechi.
Ndime 22 imafotokoza za chotengera cha mkwiyo choyenera chionongeko. Kodi akuyenera zimenezi ndani? Zimenezi sizinafotokozedwe apa. Koma kuti Mulungu sanachite zimenezi pali umboni waukulu m’ndimeyi. Kodi kapena zinanenedwa kuti Mulungu anapirira zimenezi ndi kuzunzidwa kwakukulu ngati Iye mwini m’lowa m’malo wa chilango chawo?
Taonaninso kusiyana kwa ndime imeneyi ndi ndime 23, pamene akufotokoza kuti anakonzeratu chotengera cha chisomo. Ndi zodziwikiratu kuti iwo anadzilowera okha m’malo. “Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, uli kudziunjikira wekha mkwiyo pa dzuwa la mkwiyo ndi lakuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu” (Aroma 2:5).
MAU A MULUNGU SADZIWA ZA CHIKONZERO CHA M’KUKANIDWA
Ayi ndithu, palibe umboni ndi umodzi omwe m’Mau a Mulungu pamene amafotokoza kuti Mulungu anaikiratu chikonzero cha m’kukanidwa — mwanjira ina, kunena kuti Iye anakonzeratu kuti anthu ena akhale otaika kwa muyaya. Zimenezi zikusemphana ndi zimene Mulungu anavumbulutsira zokhudza Iye mwini m’Mau ake.
Iye ndi Mpulumutsi wathu — Mulungu, amene amafunitsitsa kuti anthu onse apulumutsidwe, ndipo anapereka Mwana wake, Yesu Kristu, “nsembe ya tonse” (1 Timoteo 2:4,6), kuti onse akakhale ndi gawo mu chiombolo chake.
Tsopano zingatheke bwanji Iye kusankhiratu ena pamene mwini wake akunena kuti “onse” komanso ndi kuchita chisankho kuti awa asakhale nawo m’gawoli, koma kuti akakhale m’kutaika kwa muyaya? Tingathenso kutchula ndime zina zochuluka zoterezi — mwachitsanzo taganizirani za Yohane 3:16; Aroma 3:22; 1 Yohane 2:2 ndi zina zotere.
Ayi ndithu, thokozani Mulungu, pali chisankho chimene chaikidwa kwa ochimwa kuti akathe kubwera ku ulemelero. Koma palibe m’Mau a Mulungu pamene palembedwa kuti munthu wasankhidwira ku chionongeko. Motsutsana ndi izi, Mau a Mulungu akunena kuti: “Iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere” (Chivumbulutso 22:17), ndipo “Mulungu Mpulumutsi wathu; amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi” (1 Timoteo 2:4).
Ngati sitingathe kulumikiza pamodzi zinthu ziwirizi — kusankhidwa kwa ena ku moyo komanso kuitanidwa kwa onse kufika kwa Iye, ndiye kuti Yesaya 55:9 ndi yathu: “Maganizo anga ali atali kupambana maganizo anu.” Zimene munthu amayesera kuganiza kuti maganizo ake ali othekera kumvetsetsa ndi kugamula nzeru komanso njira za Mulungu? koma munthu wa chikhulupiriro angathe kunena ndi Abrahamu, “kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?” (Genesis 18:25).
Ndi malonje anga onse, ine m’bale wako mwa Ambuye Yesu,
H.L.H.
Mutu 6
KUSANKHA (KUPITILIZA KALATA YATHU YA M’MBUYOMU)
Wokondeka Amzanga,
Tsopano funso lakuti, kodi ndingadziwe bwanji kuti ndasankhidwa? lingathe kufunsidwa.
Choyambirira tikuyenera kuzindikira kuti Mau a Mulungu safotokoza kwa osakhulupirira zokhudza kusankhidwa. Mau a Mulungu amafotokoza kwa osatembenuka za kutaika kwawo ndi chiweruzo cha Mulungu, komanso kuitana kwa Mulungu kuti atembenuke; pamene Ambuye Yesu Kristu ndi ntchito yake zikupezeka, ndi cholinga chakuti akakhulupirire.
Pamene iwo atembenuka ndi kukhulupirira mwa Ambuye Yesu iwo amauzidwa kuti iwo ndi osankhidwa. Kodi angadziwe bwanji za zimenezi? 1 Atesalonika 1:4-6 ikutipatsa yankho. Pamenepo mtumwi akulemba kuti: “Podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, chisankhidwe chanu, kuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa timakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu. Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m’mene mudalandira mauwo m’chitsautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
Iwo anavomereza Mau — ichi ndicho chitsimikizo chake. Ngati munthu walandira Uthenga Wabwino nakhala ndi mtendere ndi Mulungu, ichi ndi chitsimikizo cha kusankhidwa kwake.
KODI MAU A MULUNGU AMANENA CHIYANI ZOKHUDZA KUSANKHIDWA?
Ngakhale kuti kusankhidwa kwalembedwa m’malo ambiri m’Mau a Mulungu (mwachitsanzo, onani, 1 Petro 1:2; 2 Timoteo 1:9; Tito 1:2; ndi ena otere), chiphunzitso chimenechi chikupezeka koyamba m’buku la Aroma 8:28-30 komanso ku Aefeso 1:3-14.
Ku Aroma 8:29,30 timawerenga kuti: “Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri; ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso wolungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.”
Choyambirira apa tikuona kuti Mulungu adawadziwiratu anthu. Sakunena kuti adadziwiratu chikhalidwe chawo, m’mene moyo wawo udzakhalire, kapenanso kuti adzapulumutsidwa kapena ayi, ndi zina zotere. Ayi ndithu, Iye anangowadziwa anthuwa. Ndipo ku Aefeso 1:4 amanena kuti mauwa amatanthauza kuti izi zinachitika lisanakhazikike dziko lapansi, kunena kuti kale la muyaya.
Anthu amenewa — osachotserapo ndi m’modzi yemwe — anawaikiratu kukakhala monga mwa chifanizo cha Mwana wake. Kusankha kumeneku! Kunachitika ife tisanabadwe, Adamu asanalengedwe, inde, ngakhale chilengedwe cha kumwamba ndi dziko lapansi chimene Genesis 1:1 chimanena, Mulungu anaganizira za ife, ndipo mwa upangiri wake anakhazikitsa kuti tikakhale monga mwa chifanizo cha Mwana wake.
Mau a Mulungu amanena za Kristu kuti ali “fanizo la Mulungu wosaonekayo” (Akolose 1:15). Apatu tikupeza kuti tidzasandulika mu chifanizo Chake. Akuyenera kukhala woyamba kubadwa pakati pa abale ambiri. Ngakhale kuti Iye akutenga malo a woyamba kubadwa, komabe tidzakhala ngati Iye.
Apatu, sakunena Ambuye ali mu umwana wake wa muyaya. Koma akukamba za Mulungu wa muyaya ndipo Iye ndi amene ayenera kukhala basi. Apa akufotokozedwa ngati Mwana wa Mulungu wobadwa m’dziko lapansi, amene anatsiriza ntchito ya pa mtanda paja, ndipo mwa Iyeyu uphungu onse wa Mulungu uyenera kukwaniritsidwa (Akolose 1:19-21; Aefeso 1:10,20-23).
Chiyambi cha mdalitso wathu chili pamenepa kulumikizana ndi zotsatira zonse — umuyaya umene unalipo chisanachitike chilengedwe cha kumwamba ndi dziko lapansi ukulumikizana ndi umuyaya umene udzakhala kumwamba ndi dziko lapansi zitapita.
Uphungu wa pamtima pa Mulungu ukulumikizana ndi kukwaniritsidwa kwa uphunguwo monga momwe akutionetsera ku 1 Yohane 3:2: “Tidziwa kuti, pakuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, pakuti tidzamuona Iye monga ali.” Monga “ana a kuuka kwa akufa” (Luka 20:36) tidzaonetsedwa monga ana a Mulungu, pamene Iye “adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemelero” (Afilipi 3:21).
KUITANIDWA, KULUNGAMITSIDWA NDI KULEMEKEZEDWA
Mu ndime 30 tili ndi kulumikizana pakati pa uphungu wa Mulungu ndi nyengo. Pamene tinabadwa, tinayang’anitsa nkhongo zathu kwa Mulungu; tinali ochimwa, koma Mulungu anatiitana ife. Apatu sinkhani yokhudza kuitana kwa chisawawa kwa anthu onse kuti atembenuke. Apa akukamba za machitidwe ake aluso a Mulungu, amene “amaitana zinthu zoti palibe, monga zilipo” (Aroma 4:17). Ndipo amene Iye wawaitana amawalungamitsanso.
Apatu zinthu zonse zikuoneka monga mwa maonedwe a Mulungu ndi uphungu wake. Nthawi imene kalata ya ku Aroma imalembedwa onse osankhidwa anali asanaitanidwe — mwinanso ochepa okha, pakuti nkhani ya kusankhidwa inachitika dziko lapansi lisanalengedwe, ndipo izi zikukhudza mpingo okha. A Israeli, komanso okhulupirira onse utachitika mkwatulo wa mpingo, anasankhidwa pachiyambi cha dziko lapansi (Chivumbulutso 13:8).
Ngakhale lero lino sikuti onse osankhidwa anaitanidwa. Izitu zidzachitika pokhapokha pamene mpingo udzakwatulidwa ndipotu mogwirizana ndi chiwerengero choikika. Koma molingana ndi uphungu wa Mulungu ndi zosakaikitsa kuti izi zidzachitika. Ndi chifukwa chake m’malankhulidwe a uneneri zimakambidwa ngati kuti izi zinakwaniritsidwa kale.
Ngakhalenso kulemekezedwa kumakambidwa ngati kuti kunachitika kale, ngakhale Aroma 5:2 amanena kuti ulemerero wa Mulungu udakali chiyembekezo, komanso Aroma 8:11 amanena kuti matupi athu akufa adzapatsidwa moyo. Koma izi ndi zosakaikitsa kuti zidzachitika. Zosenzi kutichitira ubwino kutipatsa malo, amene molingana ndi kusankha kwa chisomo cha Mulungu tikuyenera kukakhala, tidzatengedwa ndi kukafika ndi Iye popanda ife kuthandizirapo. Ichi ndicho chitsimikizo chathu.
MULUNGU WATHU NDI ATATE WATHU
Ku Aefeso 1:4,5 akukamba zambiri za izi. Mu ndime 3 Mulungu akutchulidwa kuti ndi Mulungu komanso Atate wa Ambuye Yesu Kristu. Ngati munthu, Ambuye Yesu analankhula za “Mulungu Wanga” (mwa chitsanzo ku Mateyu 27:46). Monga Mwana wa Mulungu, Yesu anatchula Mulunguyo kuti Atate Wake (Yohane 17:1;5:17,18 ndi ena otere).
Atauka kwa akufa, Ambuye anabweretsa ake omwe mu chiyanjano chomwecho ndi Mulungu. “Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17). Komabe, kusiyana kudzakhalapobe. Iye sakunena kuti Atate “wathu” ndi Mulungu “wathu”. Yesu adakali woyamba kubadwa pakati pa abale ambiri. Komabe Mulungu wakhala Mulungu wathu ndi Atate wathu mwa Ambuye Yesu Kristu.
Ku Aefeso 1:4,5 udindo womwewu umene talandira kudzera m’kusankhidwa ukukhala ndi machitidwe ofanana. Mu ndime 4 tikupeza malo athu pa Mulungu ngati Mulungu ndipo mu ndime 5 malo athu pa Mulungu ngati Atate. Ndipo kuti malo amenewa tikawakhale mwangwiro tinasankhidwa mwa Kristu. Ali ndi malo amenewa mwa ubwino wa ulemelero wake ndi ufulu wake. Ndipo ife timalandira mwa Iye.
WOYERA NDI WOPANDA BANGA PAMASO PAKE M’CHIKONDI
Taonaninso Aefeso 1:4: “Monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m’chikondi.”
Apatu tili ndi chikhalidwe cha umulungu pakati pathu. Mulungu ndi woyera m’chikhalidwe chake, wopanda banga m’machitidwe ake, ndipo chikondi ndicho chikhalidwe chake (1 Yohane 1:5; 4:8-16). Tikuyenera kugwirizana ndi chikhalidwe chake ngati tikufuna kubwera m’kupezeka kwake monga Iye amafunira.
Zingatheke bwanji kuti anthu amene aipitsidwa ndi tchimo kukhala naye pamodzi, Iye amene ali woyera kwambiri kuti sangangoyang’anira tchimo, ndipo Iye amene tsiku lina adzaponya onse amene alumikizana ndi uchimo m’nyanja ya moto? Iyetu wasankha ife kuti tikakhale mogwirizana ndi chikhalidwe chake chomwe.
Komatu sizinathere pomwepa. Tikuyenera kulowa mu chikhumbokhumbo cha mtima wake, mkati mwa malingaliro a Mulungu amene ali chikondi. Pa chifukwa chimenechi ndime 4 ikunena, ‘Pamaso pake m’chikondi.’
Pang’ono ndi pang’ono pamene tidzakhala ndi Iye tidzakhala ‘oyera ndi opanda banga pamaso pake m’chikondi.’ Kenako, kalikonse kamene kamakhala chikumbutso cha uchimo mwa ife kadzachotsedwa — kufooka kwathu konse, kulephera kwathu, komanso machimo athu. Kenako thupi lidzaonongedwa.
Komabe Mulungu amaona kuti izi zatichitikira kale. Iye amationa m’moyo wathu watsopano umene Ambuye Yesu Kristu watipatsa. “Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Kristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m’menemo. (Aefeso 2:10). “Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa” (Ahebri 10:14). “Chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m’dziko lino lapansi” (1 Yohane 4:17).
Chisomo chotani kwa ife, osauka, chilengedwe cha uchimo monga ife tili!
M’KULELEDWA (MONGA ANA) KWA IYE YEKHA
Izitu sizinathere pomwepa. Tikanatha kulandira zonse zimene zalembedwa pamwambapa ndi cholinga chakuti tikaikidwe monga a kapolo pamaso pa Mulungu. Ngakhalenso nawo angelo akuyenera kukhala monga mwa ulemerero ndi chiyero cha Mulungu. “Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Kristu” (Aefeso 1:5).
Pali ubale wokhazikika: ubale wa atate kwa ana ake komanso wa ana kwa tate wawo. Mwana wa Mulungu, ataukitsidwa, komanso mwa chiyambi cha ntchito yake pa mtanda paja Iye anatibweretsa pamalo ake: kukakhala ana a Mulungu.
Koma pano ku Aefeso tikuphunzira kuti Mulungu anatiikiratu pamalo amenewa — lisanakhale dziko lapansi. Kenako Mulungu anakonzeratu kuti tikakhale pamalo amenewa. Nanga anachita izi pa chifukwa chanji? Anachita izi ‘molingana ndi kusangalatsidwa kwabwino kwa chifuniro chake.’ Chikondi chake chokha ndicho phata la mdalitso umenewu.
CHIKRISTU CHIMABEREKA MCHITIDWE WA UMUYAYA
Koma pali mfundo yofunikira kwambiri imene tingathe kuombera nayo mkota m’ndime zimenezi. Iye “anatisankha mwa Iye (Kristu) lisanakhale dziko lapansi.” Kusankhidwa kumeneku kuli kunja kwa nthawi ndi kwa muyaya, osati kwa dziko lapansi. Ndime 3 ikulankhulanso za “mdalitso wauzimu m’zakumwamba.”
Israeli ndi fuko losankhika padziko lapansi (Eksodo 19:5; Levitiko 25:2,23; Deutoronomo 7:6). Koma ‘nkhosa’ ku Mateyu 25:31 kupita mtsogolo zikuuzidwa kuti: “lowani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Awatu ndi madalitso a dziko lapansi (ufumu) olumikizidwa ndi nthawi (ya chikhazikiro chake cha dziko lapansi).
Kuchokera pamenepa zotsatira zake ndi malo abwino amene ife tikhalapo. Timapezeka mu chikonzero (Chikristu) ndi ku thupi (mpingo) umene umapezeka kunja kwa nthawi yokhazikidwa. Chiyambi chawo ndi kuchokera asadakhazikitsidwe maziko a dziko lapansi pamene Mulungu anawakhadzikitsa mwa Kristu.
Iwotu siadziko lapansi (Yohane 17:14), ndipo adzapitirirabe ngakhale likadzapita dziko lapansi. Amakhala ndi chikhalidwe cha uzimu ndi chamuyaya. Zimenezi zimatipatsa maonekedwe akuya a Chikristu.
Ichitu ndi chifukwa chake Aefeso 1:3-5 sakufotokoza za udindo komanso zinthu zonse zimene zikulumikizana ndi izi. Izi zinayamba Adamu atalengedwa kale ndi kuikidwa m’munda wa Edeni, ndipo zidzatha chikadzapita chiweruzo cha pampando wachifumu waukulu woyera (Chivumbulutso 20).
Mitengo iwiri inaima m’munda mwa Edeni. Panali mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, umene ukuimira mfundo ya kudziyang’anira, pakuti “tsiku limene udzadya umenewo udzafa ndithu”; komanso mtengo wa moyo, umene umaimira mfundo ya moyo. Adamu anadya chipatso cha mtengo woyambirirawo ndipo sanathe kudya cha mtengo wachiwiriwo, pakuti analandira imfa ngati chiweruzo chake.
Pa mtanda paja timapeza mitengo iwiri imeneyi italumikizana. Ambuye Yesu anadzitengera yekha zotsatira za udindo wa onse akukhulupirira, monga Iye Wakuukitsidwa wa apatsa moyo m’malo mwake. Iye monga Mtengo Wamoyo.
Koma zonse izi zinachitika mu ‘nthawi yake’ padziko lapansi, ndipo izi sizikupanga gawo lililonse la uphungu wa muyaya wa Mulungu. Komabe kunali kofunikira, ndipo kusankha kunachitika “mwa Iye,” mwa Kristu; ndipo chikonzero chonse ndi uphungu wa Mulungu unavumbulutsidwa koyamba utapita mtanda, pamene Adamu wotsiriza anakhala Mutu wa chilengedwe chatsopano, Mutu wa banja la Mulungu.
N’kokoma kotani kuona kuya kwa malingaliro a Mulungu ndi kuona luso la nzeru zake — komanso nthawi yomweyo kuganiza kuti ndife chipango cha malingaliro ake!
Ndi malonje anga onse, ine m’bale wako mwachikondi cha Mulungu,
H.L.H.
MUTU 7
KRISTU, WAMKULU WATHU WANSEMBE
Okondedwa Amzanga,
Wina akazindikira zomwe wokhulupirira ali nazo, pamenepo amaganiza kuti palibenso china chimene angachifune, pakuti amadziwa kuti: Machimo ake akhululukidwa ndipo ali ndi mtendere ndi Mulungu.
Kupyolera m’kubadwa mwatsopano walandira moyo watsopano. Chilengedwe chatsopano, moyo wa umulungu umene sungachimwe. Mulungu waweruza umunthu wake wakale pa mtanda paja ndipo wachotsa umunthuwo, kotero kuti tsopano Mulungu akuona wokhulupirirayu m’moyo wake watsopano, ndipo kotero kulibenso kutsutsika kwa iwo ali mwa Kristu Yesu.
Mzimu Woyera akhazikika mwa iye. Iye wawomboledwa ku mphamvu ya Satana, dziko komanso uchimo — anawomboledwa ndi cholinga chokamtumikira Mulungu. Wavomerezedwa pakati pa okondedwa. Tsopano angathe kunyada m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu, chifukwa akudziwa kuti zimenezi zakonzedwera kwa iye.
Tsopano molingana ndi umuyaya komanso kumwamba, ndi zoona kuti munthuyu sakufunikanso kena kalikonse koonjezera. Komabe mwana wa Mulungu amakhalabe ndi zosowa pano padziko lapansi. Chifukwa chakuti iyeyu ndi mwana wa Mulungu komanso mzika ya kumwamba (Afilipi 3:20) ndi mlendo padziko lapansi, ndipo chifukwa chakuti ali pa ulendo wopita kumwamba iye ndi wa paulendo.
Koma kupatula zimenezi iyeyu wawomboledwa ku mphamvu ya mdierekezi ndipo akufuna kutumikira Mulungu, pakuti ichi ndi chilakolako cha mtima wake. Koma chifukwa cha chimenechi walowa mu udani waukulu ndi mdierekezi komanso ndi anthu omwe sanatembenuke. Ntchito ya mdierekezi, ndiyo kupangitsa anthu kukhala osamvera Mulungu.
Kotero amagwiritsa ntchito mphamvu zake zonse komanso machenjerero ake onse ndi cholinga chokopa okhulupirira kuti akachimwe, kusamvera Mulungu. Izitu sizibweretsa mpungwepungwe wina ulionse kwa Satana ndi osakhulupirira. Mwa chikhalidwe chawo safuna kumvera Mulungu. Mitima yawo imafunitsitsa kuchimwa ndithu, ndipo akachimwa mitima yawo imakwanitsidwa (Genesis 6:5; Marko 7:20-23; Aroma 3:10-20).
Awa ndi maziko amene dziko lapansi komanso anthu okhalamo anamangikira. Anthu anagwirizana pamodzi pa chifukwa chimenechi kuti asakakhale odalira Mulungu ndi kuti akachite mogwirizana ndi malingaliro awo (Genesis 9:1; 11:4-9). Koma chifukwa chakuti munthu sangakhale odziimira pa yekha anatenga mdierekezi kukhala mfumu yake, ndipo atam’kana Mwana wa Mulungu, munthu anatenga mdierekezi kukhala mulungu wake (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4).
Kuyesetsa kwa m’Kristu, ndi kotsutsana kwambiri ndi kuyesetsa kwa dziko lapansi. Munthu wokonda za dziko lapansi ndi mdani wotheratu wa m’Kristu amene amatengedwa ngati chiopsezo chobweretsa mavuto. Akuyankhula kwa okhulupirira Ambuye anati ku Yohane 7:7 “Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza ine ndi lichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.”
Ndipo zokhudza okhulupirira ku Yohane 17:14 akuti: “Ndipo dziko lapansi lidana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi.” Ndipo ku Yohane 16:33 akuuza ophunzira ake kuti: “M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto.” M’Kristu adzavomerezedwa ndi dziko lapansi ngati iye sangadzionetsere yekha monga m’Kristu.
Koma m’malo mwake alowerera m’zochitika zake ndi kudzipereka yekha pansi pa ulamuliro wa Satana. Koma kuti achite izi zingamtsogolere iye kukakhala wosakhulupirika pa maso pa Mulungu. M’Kristu wotere ndiye wa chinyengo wokhalanso kumbali ya mdani.
Apatu ndi pomwe pamayambira nkhondo ya m’Kristu. Satana amabwera ndi kuyesa kumutengera iye ku uchimo. Amamunong’oneza malingaliro oipa a uchimo. Amamuonetsa zinthu za uchimo. Amamulola kumva mau opanda umulungu ndi kuyesa kumutengera ku malo opanda chiyero.
Ndipo pamwamba pa zonsezi amalola dziko lapansi kuonetsera udani wake. Zonsezi zimamvetsa chisoni munthu watsopanoyu. Koma m’Kristu adakalibe ndi umunthu wake wakale, umene umakonda kuchimwa kusiyana ndi kukondweretsa Mulungu. Apatu ndi pomwe Satana amapezera mpata wolowera. Pali chiopsezo chachikulu kuti Satana angathe kupambana ndi kum’kopa iye ku uchimo.
Komanso chikondi cha Mulungu chapereka kuthekera kwake.
KRISTU, WANSEMBE WATHU WAMKULU
Zinthu zimenezi zaonetsedwa kwa ife mu kalata ya ku Ahebri. Pamenepa tikuona m’Kristu monga wa paulendo komanso mlendo. Akuyenda kupita ku ulemerero (Ahebri 11:40), pakuti maitanidwe ake ndi a kumwamba (Ahebri 3:1). Koma padakali pano ali m’chipululu kukomana ndi zovuta komanso zoopsa zopezeka pano padziko.
Ndipo Wansembe wathu akuonetsedwa kwa ife. Ambuye Yesu Kristu kumwamba ndiye Wansembe wathu Wamkulu amene, pakuona zovuta ndi zoopsa zathu, akutipembedzera m’malo mwathu pamodzi ndi Mulungu.
Nthawi zambiri anthu amaganiza kuti unsembe wa Ambuye Yesu umaima molumikizana ndi machimo athu. Koma kunena zoona ili ndi bodza. Komabe, chiyambi cha kuonekera kwake ngati Wansembe Wamkulu kunali kolumikizana ndi machimo athu.
Ahebri 2:17 amanena kuti: “Kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wa chifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.” Koma Ahebri 10:12 akunena kuti: “Koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja la manja la Mulungu chikhalire.” Ndime 14 ikupitiriza, “Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa”.
Kalata ya ku Ahebri ikuonetsera wokhulupirira monga m’chiyanjano chake kukhala cholengedwa cha Mulungu. Pakuti Ambuye Yesu anamaliza ntchito ya pa mtanda paja pamene Mulungu wakhutistidwa kwambiri, nkhani ya tchimo inathetsedwa kwa muyaya. Iye wapeza “Chiombolo chosatha” (Ahebri 9:12). Wokhulupirira ‘walungamitsidwa kwa muyaya.’ Kristu anachotsa tchimo ndi nsembe ya Iye yekha (Ahebri 9:26).
Nkhani ya tchimo sidzamvekanso pakati pa Mulungu ndi wokhulupirira. Kotero, palibenso china chimene chinanenedwa chokhudza uchimo m’makalata opita ku Ahebri. Machimo amene wokhulupirira amachita akatembenuka mtima simakhalanso nkhani pakati pa Mulungu ndi cholengedwa chake, komano pakati pa Tate ndi mwana wake. Zimenezi timazipeza m’kalata yoyambirira ya Yohane.
WANSEMBE KUMWAMBA
Ngakhale kuti ntchito ya Ambuye Yesu monga Wansembe Wamkulu inachitika kale padziko lapansi, ndipo inali yolumikizana ndi machimo athu, unsembe wa Ambuye tsopano sukugwiranso ntchito imeneyi. Atatsiriza ntchito yonse anakhala pansi kwa muyaya kudzanja la manja la Mulungu kumwamba. “Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife...wakukhala wopitirira miyamba” (Ahebri 7:26).
“Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe” (Ahebri 8:4).
Tsopano ife tili ndi wansembe kumwamba amene molingana ndi machimo athu anaika kena kalikonse m’malo mwake, amenenso tsopano akukhala kupembedzera ake omwe (Ahebri 7:25).
Kodi wansembe ameneyu ndi ndani? Ahebri 1 akutiuza za wansembeyu. Iye ndi Mwana wa Mulungu! Ichi ndi chifukwa chake amatipembedzera nthawi zonse ndi Mulungu. Ndani angakwanitse kuchita izi kuposa Mulungu?
Koma kuti akapembedzere anthu akuyenera kukhala monga munthu. Ndipo ku Ahebri 2 akunena kuti Iye anakhaladi munthu. Iye ndi Mwana wa Munthu. Iyetu anali munthu weniweni kuposa m’mene analili Adamu, pakuti Iye anabadwa mwa mkazi (Agalatiya 4:4).
Zodabwitsa! Mulungu kudzionetsera m’thupi! Mau anakhala thupi! Iye amene anali Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, amene analenga munthu — Iye mwini anakhala munthu.
Ahebri 2 ikutipatsa zifukwa ziwiri zomwe Mulungu anakhalira munthu. Ndime 14 mpaka 17 zimatiuza kuti amafuna kukwaniritsa ntchito ya kutilungamitsa ife ku machimo athu ndi kutiombola ife ku mphamvu ya mdierekezi komanso imfa. Koma ndime zina zotsalirazo zikutipatsa chifukwa china: wayenera kukhala Wansembe Wamkulu wa chifundo ndi wokhulupirika. Kodi zimenezi sizikuyankhula mwamphamvu ku mitima yathu?
Ambuye Yesu anadziwa zimene ife tidzakhale. Iye anadziwa kuti kudzakhala zoopsa ndi zovuta panjira pathu. Kotero anakhala munthu nalowa m’malo mwathu kuti akakumane ndi zovuta zonse, zisoni zonse, yesero lililonse, ndi cholinga chakuti akathe kuima nafe mu zinthu zonse zimene tikuyenera kugonjetsa.
ANAPHUNZIRA KUMVERA
Iye amadziwa zotsatira za kumvera Mulungu pamene tili munyengo ndi malo amene agalukira Mulungu. Kodi Iye sanaphunzire kumvera Mulungu (Ahebri 5:8)? Iye sanamvere, chifukwa anali Mulungu wa M’mwambamwamba.
Komano ngati munthu padziko lapansi anaphunzira kuti kumvera ndi chiyani. “Iye anandigalamutsa m’mawa ndi m’mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira. Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m’mbuyo.” Iye anayankhula chomwechi ku Yesaya 50:4,5.
Komanso anakomana ndi zotsatira zimene zimabwera padziko lapansi zokhala pa udani ndi Mulungu. “Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi Masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa” (Yesaya 50:6). Anamenyedwa chifukwa cha kunena zoona (Yohane 18:23).
Chinachitika kwa Iye ndi chiyani, Woyera wa Mulungu, pamene ananena naye: “Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamaliya, ndipo muli ndi chiwanda?” komanso “Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda” (Yohane 8:48-52)?
Komanso anawona mphamvu ya Mulungu ikumusamalira. “Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi. Iye ali pafupi amene alungamitsa ine” (Yesaya 50:7,8).
Tikuyenera kuphunzira kumvera chifukwa ifeyo tinali zolengedwa zosamvera ndi zochimwa. Iye angathe kutimvetsa bwino lomwe pamene ife tili m’kati kuphunzira. Pamene zotsatira za kumvera kwathu zikhala kunenedwa, kusekedwa mwinanso kutaya zinthu zomwe tinali kuzipeza, kusalidwa pa kupatsidwa mwayi wakubooleza m’moyo, kapenanso zinthu zina zimene zingatipindulire pamoyo wathu, Iye amakhudzika nafe pamodzi.
Ndipo pakukhudzika kwathunthu kumeneku amatithandiza ndi kutipembedzera, ndi cholinga chakuti tikapeze chifundo ndi chisomo kuti zikatithangatire mu nyengo yotereyi (Ahebri 2:18, 4:16).
Kumvera Mulungu kungathe kutipatula ife ku anthu kapena zinthu zimene mitima yathu inakangamirako. Inde, ngakhalenso ku zinthu zimene zimaoneka zabwino zimene tinalandira kuchokera kwa Ambuye.
Mwinanso kutipatula ku anthu amene timawakonda kwambiri pano padziko lapansi, chifukwa Iye amawatenga anthuwa kwa ife, komanso pa chifukwa chakuti tikufunitsitsa kukamumvera Iye chotero sitikufunikanso kukayenda ndi anthu amenewa. Tingathenso kuleka zochitika zathu zosiyanasiyana ngakhale ntchito ya uzimu imene tikufuna kuchitira Iye, imene mwa zoonadi anatipatsa ife kuti tim’gwirire.
Ambuye Yesu amadziwa zonsezi kulinga mu zomwe Iye anadutsamo kale. Anadzikhutula yekha nakhala womvera kufikira imfa, indetu, ngakhale imfa yake ya pamtanda paja (Afilipi 2:5-8). Anasautsika m’malingaliro ali m’munda mwa Getsemane ndipo anapemphera: “Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine” (Luka 22:42). Kodi moyo wake woyera sukanabwerera m’mbuyo kapena kugwa kumene mu njira imeneyi, pamene kumvera pa Mulungu kunamutsogolera zofunika kuchita?
Inalidi njira yowawitsa, imene Iye Woyerayo anayenera kudutsamo atatisenzera machimo athu m’thupi mwake pa mtengo paja, inde, pamene Iye anatengedwa monga wochimwa (1 Petro 2:24; 2 Akorinto 5:21). Njira imene inam’pangitsa Mulungu kumusiya yekha Yesu Kristu ndi kuti chiweruzo chake chimgwere Yesu Kristu (Mateyu 27:46; Zekaliya 13:7; Aroma 8:3).
Zoonadi, Iye anayenda m’njira ya kumvera kwakuya kuposa ana onse a Mulungu amene anayendako m’njirayi kapena amene akuyembekezera kuyenda njira ya kumvera. Kotero, pa chifukwa chimenechi, sipangapezeke ‘nsembe ya kumvera’ popanda Iye kumvetsetsa momwe mitima yathu ikumvera, komanso kumvetsetsa kulimbana kwa mkati mwathu.
Koma atadutsa m’njira ya kumvera mpaka kumapeto — “Osati kufuna kwanga, koma chifuniro chanu chichitike” — Iye akudziwa kudzera mu zomwe anakumana nazo chimene Mulungu amatanthauza mumtima mwa munthu mu nyengo yotereyi, ndiponso thandiz limene Mulungu amapereka“Ndipo anamuonekera Iye mngelo wa Kumwamba namlimbikitsa Iye” (Luka 22:43). N’chifukwa chake amabwera kudzatithandiza kuti “tipeze chisomo komanso thandizo la mu nyengo yake.”
MAYESERO A SATANA
Mitima yathu imakhala yokhumudwa kwambiri pamene Satana amabweretsa mayesero ake. Moyo wathu watsopano umavutika pamene iye atibweretseranso malingaliro oipa mwa ife, pamene apangitsa mitima yathu kukhala yosamvera, pamene mobwereza bwereza amalimbana nafe osatipatsa mpata wopumira, pakusokoneza malingaliro athu pamene ife tikuwerenga Mau a Mulungu, pamene autsa malingaliro oipa m’mitima yathu pamene ife tikupemphera ngakhalenso pamene tili m’misonkhano yofunikira zedi.
Ambuye Yesu Kristu anayesedwa ndi Satana kuposa munthu wina aliyense. Kwa masiku makumi anayi otsatizana Iye anayesedwa (Luka 4:2). Satana anagwiritsa ntchito mphamvu zake zonse komanso kuchenjera konse pa Iye amene ali Wolungama ndi Woyera.
Atagwa mosavuta mu uchimo, Satana anali ndi ntchito yosavuta pa munthu. Anali bwenzi la mphamvu mu mtima mwa munthu wochimwa, wogwetsedwa, bwenzi limene nthawi zonse limasangalatsidwa ndi uchimo. Malingaliro onse a mtima wa munthu anali oipa okhaokha (Genesis 6:5).
Izitu sizinali zoona zake za Adamu asanachimwe. Iyetu analengedwa mwangwiro ndi Mulungu. Ngakhale Satana analibe gawo lolumikizana ndi mtima wa Adamu, kugonjetsa kamodzi kokha kanali kokwanira kukwaniritsa cholinga chake. Adamu anachimwa ndipo anakhala kapolo wa Satana.
Tsopano panabwera Munthu watsopano padziko lapansi amene analibe mtima wa uchimo. Iye sanadziwe tchimo lililonse. Ndi munthu ameneyu, Satana anayesetsanso kulimbana naye, koma pamenepa nkhondo inayenda mosiyana ndi yoyamba ija.
Adamu anagonjetsedwa m’munda mwa Edeni kumene chilichonse chimaonetsera ukulu wa Mulungu. Ambuye Yesu Kristu anapambana m’chipululu — malo amene amaonetsera matemberero a dziko lapansi — kumalo kumene kunalibeko chake. Kumeneku Satana anagwiritsa ntchito mphamvu zake zonse ndi nzeru zake zonse kuti achimwitsenso Woyerayo.
Nkhondoyi inatenga masiku makumi anayi ndipo Satana anagwiritsira zida zake zonse kufikira anagonjetsedwa. Satana anathawa osati Ambuye Yesu Kristu. Ndani amene akudziwa mayesero onse amene Yesu Kristu anakumana nawo? Ndani amene akudziwa machenjerero onse a Satana, zida zonse za wolamulira wa mumdima? Ndi anthu atatu okha amene tikuuzidwa.
Tangoganizirani kuti Wolungamayo, Woyerayo, amene sanadziwa tchimo, akanagonja ku zida za ku mdima! Mzimu wake ukanasautsidwa kwambiri. Iye amatimvetsetsa, amakhudzika nafe, pamene Satana abweretsa machenjerero ake pa ife. Kodi pali yesero limene Satana akhoza kutibweretsera limene sanaliyeserepo pa Ambuye?
Ichi ndi chifukwa chake angathe kutithandiza. Iye anapempherera Petro kuti chikhulupiriro chake chisalephere. “Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa” (Ahebri 2:18). “Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo” (Ahebri 4:15).
KUKHUDZIKA KWAKE M’MAVUTO ATHU NDI MU NTHAWI YA CHISONI
Pamene okondedwa achotsedwa pakati pathu, ndani amene amakhudzika ndi kupwetekedwa mtima kwathu ngati IYE amene analira kumanda a mzake? Pamene tili tokha, ndani amene anakhalako yekha kuposera IYE, amene ananena kuti: “Ndidikira, ndikhala ngati mbawa ili yokha pamwamba pa tsindwi” (Masalmo 102:7)?
Pamene abwenzi atithawa, ndani amene angamvetsetse ngati IYE amene Malemba ananena: “Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa” (Marko 14:50)? Ngati anthu sakutimvetsetsa, kapena anthu amene tikuwafotokozera za zovuta zathu sakuonetsa chidwi chotithandiza, ndani amene anakhala payekhayekha ngati IYE amene analira: “Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza” (Masalmo 69:20)?
Iye ndi amene, atauza ophunzira ake kuti adzaperekedwa ndi m’modzi wa iwo nanenanso kuti Iye adzafera iwo, sanazindikira kena kalikonse, koma anatsutsana pakati pawo kuti wamkulu ndi ndani (Luka 22:19-22). Pamene tikufuna kuwala, ndani amene angatithandize kuposa IYE amene zinanenedwa za Iye kasanu ndi kawiri ku Luka kuti anapemphera, inde, anachezera usiku onse kupemphera pamene anali ndi zinthu zofunikira kwambiri kuchita!
Ameneyu ndi Wansembe wathu Wamkulu kumwamba, amene nthawi zonse amakhala kutipembedzera (Ahebri 7:25). Iye sakumananso ndi mavuto ena alionse — kwa Iye nkhondo yonse inatha! Koma Iye anadzipereka kwathunthu kuti akatithandizire ife, kugwiritsa ntchito chidziwitso chake chonse pa zovuta ndi zokhoma zimene Iye anakumanako nazo pamoyo wake.
Kodi ndikukamana ndi zovuta komanso kuponderezedwa pamoyo wanga? Ngati ndi choncho ndingathe kupeza thandizo m’mapembedzero a Kristu. Iye akutipembedzera kwathunthu podziwa chitonthozo chimene chisomo cha Mulungu chimapereka, chifukwa akuyenera kudziwa chitonthozochi chimene chinamuthandizira Iye pamene anali padziko lapansili.
Iye amadziwa kutonthoza moyo pamene uli m’mavuto. Amandipatsa chilichonse chimene ndimafuna ndipo amachonderera pamaso pa Mulungu monga mwa chidziwitso chake kuti andipatse zimene ndikusowa. Kodi ndikufunika kuunika? Kodi ndikufunika chitsogozo pa njira yanga? Mulungu angathe kundipatsa. Ndidzalandira zonse zimene Mulungu ali thandizo langa. Zonsezi ndi chifukwa cha mapembedzero a Kristu.
Kodi ndikulandira zonsezi chifukwa chakuti ndikudzipempherera zinthuzo? Iye anapempherera Petroyo, asanadziwe kalikonse komuchitikira. Ifetu sitimupempha Ambuye kuti azitipembedzera.
Ichi ndi chisomo chabe kwa ife kuchokera mu mtima wa Mulungu chimene chimabweretsa zonsezi. Ndipo amatidziwitsa ife za chimenechi, ndi cholinga chakuti “tikafike ndi chilimbiko pa mpando wa chisomo, kuti tikalandire chisomo, ndi kupeza chisomo mu nyengo yake yakufunika thandizo.”
Ndi mafuno onse abwino, ndine mzako,
H.L.H.
MUTU 8
KUBADWA KWATSOPANO
Okondedwa Amzanga,
M’kalata yapitayi taona kuti m’kristu ndi munthu amene anafa pamodzi ndi Kristu. Chikhalidwe cha munthu wakale ndi choipa kotero kuti chikuyenera kuweruzidwa ndi Mulungu. Ku Yohane 3 Ambuye Yesu akuonetsera za mfundo imeneyi kwa Nikodemo, komanso akumuonetsera yankho lochokera kumwamba pa mfundo imeneyi.
Ndimeyi ikuyambira maka pa mutu 2:23. Pamenepa tikuona Ambuye mu Yerusalemu. Pamene anali pa mwambo wa Paska ndi kuchita zodabwitsa, “Koma pamene anali m’Yerusalemu pa Paska pa phwando, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi” kenako zotsatira zake: “Yesu sanakhulupirira iwo kuti akhale nawo, chifukwa Iye anadziwa anthu onse, ndipo sanasowa wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.” Ndipo pamene m’modzi wa iwo anadza kwa Iye, Mulungu anayankhula mau opweteka awa: “Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu!”
MWANA WA MUNTHU AMENE ALI KUMWAMBA
Mundime 11 ndi 13 ya mutu 3 Ambuye akudzivumbulutsira yekha kuti Iye ndi ndani. Iye ndi Mwana wa Munthu amene ali kumwamba! Apatu tili ndi chinsinsi chodabwitsa chokhudza umunthu wake. Yohane 1:1 imatiuza kuti Iye ndi Mulungu, Wamuyaya. Koma pa ndime 14 akunena kuti: “Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife” - “Mulungu anaonekera m’thupi”. Mulungu ndi munthu kukhala munthu m’modzi! Zodabwitsa kwambiri!
Ambuye Yesu Kristu ndi Mulungu wamuyaya. Anadzichepetsa yekha nakhala munthu! Komatu izi sizikutanthauza kuti analeka kukhala Mulungu.
Zimenezi sizingatheke. Anatenga nawo gawo m’mwazi ndi m’thupi (Ahebri 2:14). Iye anakhala munthu weniweni (Agalatiya 4:4; 1 Timoteo 2:5). Koma Iye amene anali munthu analinso Mulungu Wamuyaya nthawi yomweyo (Yesaya 9:6).
Pamene anagona modyera ng’ombe monga khanda, nthawi yomweyonso anali Wosunga ndi Wosamala zinthu zonse. Pamene anatopa ndi ulendo, ndi kumva njala ndi ludzu anapempha madzi kwa mzimayi wa ku Samaliya, anadzionetsera yekha monga Wamphamvu zonse amene amapereka Mzimu Woyera komanso ngati Wodziwa zonse amene angathe kuvumbulutsira poyera moyo wonse wa mzimayiyu.
Monga munthu weniweni Yesu Kristu anagona m’bwato muja. Kenako anadzuka ndi kuletsa namondwe. Anatchula dzina lake ndipo asirikali onse anagwa pansi, kenako anamugwira namumanga, namulavulira kumaso, nam’nyoza Iye.
Pamene amayankhula ndi Nikodemo padziko lino lapansi nthawi yomweyo analinso kumwamba. Anayankhula zimene amadziwa, pakuti ndi Mulungu yekha amene amadziwa tanthauzo la mau akuti “kudziwa.” Palibe munthu amene anapitako kumwamba; kotero palibe amene angathe kunena za zinthu zakumwamba.
Koma Iye, Mwana wa Munthu, anatsika kuchoka kumwamba. Inde, komabe Iye anali adakali kumwamba. Pamene amayankhula za zinthu zakumwamba, amayankhula za zinthu zimene anaziona komanso zimene amaziona, zokhudza zimene Iye amazidziwa, pakuti kunali kumwamba kwake ndi ulemerero wake.
Mwa Iye Mulungu ndi munthu analudzanitsidwa pamodzi, pakuti Iye anali Mulungu ndi Munthu kukhala Munthu m’modzi. N’chifukwa chake angelo anayankhula pakubadwa Iye: “Mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo” (Luka 2:14). Anam’dziwa Mulungu ndi ulemerero wake; komanso anam’dziwa munthu.
CHIKHALIDWE CHA MUNTHU
Ku Yohane 2:23-25 timapeza malingaliro ake pa munthu. Awatu sanali anthu opanda umulungu amene anamukana pa udani wa poyerayera. Anamzindikira Iye, pakuti iwo anakhutitsidwa ndi zozizwa zake kuti anali Mesiya.
Iwo anakhulupirira pa dzina lake. Kungowerenga mopanda kuzama zingathe kutipangitsa kuganiza kuti awa ndi anthu amene pa mutu 1:12 akutiuza kuti kwa iwo kunapatsidwa mphamvu ya kutchedwa ana a Mulungu. Koma za awa pa mutu 2 akunena: “Koma Yesu sanakhulupirira iwo, chifukwa Iye anadziwa anthu onse, ndipo sanasowa wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.”
Anthu awa anangokhulupirira koma sanatembenuke. Anakhulupirira padzina lake, koma iwo sanamlandire Iye (Yohane 1:12). Iwo anaona zizindikiro ndipo malingaliro awo ndi m’kati mwawo anatsimikizika kuti ndiye Mesiya. Kunalitu anthu ambiri otere mu nyengo imeneyi, ndiponso alipo zikwizikwi lero lino oterewa.
Sakaikira konse za zoonadi za chiKristu. Malingaliro awo ndi mkati mwawo zimawapangitsa kuzindikira zimene zili zogwirika ndi zapamwamba kwa iwo. Ndipo mu njira imeneyi avomereza chiKristu. Izitu ndi zimene munthu amafuna, pakuti mu njira imeneyi amakhala pamwamba pa choonadi komanso pamwamba pa Mulungu. Iye wakhulupirira zimene malingaliro ake kapenanso m’kati mwake mukuonera kuti zili bwino.
Zimakhala zosiyana pamene chikumbumtima chimabwera m’kuwala kwa Mulungu. chimaona kusokera kwake ndi kutsutsika kwake. Kotero sichiganiza za kuweruza Mulungu kapenanso chimene Mulungu wavumbulutsira. Chimene chimachitika ndi kuziweruza tokha ndi kulira pamaso pa Mulungu kuti alandire wochimwa.
Munthu wa kuthupi amavomereza kufunikira kwa kubadwanso kwa iwo amene amapembedza mafano kapena kwa iwo amene akukhala mu uchimo owirikiza. Koma kuti aliyense akabadwe mwatsopano, izi munthu wakuthupi sangazimvetsetse.
Panali Ayuda, ngakhale Afalisi, ngakhalenso iwo amene anafunira Ambuye zabwino, amene anakhulupirira m’dzina lake — inde ngakhalenso Nikodemo, Mfalisi, mkulu wa Ayuda, mphunzitsi m’Israeli, amene anapereka ulemu waukulu kwa Ambuye Yesu Kristu ulemu umene sukuyenera munthu wina aliyense, “Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye” (Yohane 3:2).
Munthu wa kuthupi sangathe kumvetsetsa kuti ngakhale wotere akuyenera kubadwanso mwatsopano (ndime 7). Koma Iye amene anena izi ndi amene amayankhula zimene azidziwa (ndime 11), pakuti ali Mulungu wamuyaya. Kodi mfundo imeneyi sakungonenera adani ake okha komanso kuti iwo amene amazindikira za Iye, kodi zimenezi sizikutipatsa chithunzithunzi cha momwe munthu anatayikira, m’mene kungamvutire munthu wa kuthupi kukapezeka pamaso pa Mulungu?
NGATI MUNTHU SABADWA MWATSOPANO, SAKHOZA KUONA UFUMU WA MULUNGU
Apatu Ambuye akufotokoza za ufumu monga momwe unavumbulutsidwira m’nyengo imeneyo. Dziko lonse lapansi lidzauona ufumuwo pamene udzavumbulutsidwa mu ulemerero pang’onopang’ono. Ndipo lero lino molingana ndi chikhalidwe cha chiKristu (ngati titagwiritsira mau amenewa) molingana ndi ufumu umenewu, chofunika kuchita chimakhalapobe.
Pamene Ambuye Yesu anabwera padziko lapansi ufumu unabwera mwa Iye. Ndipo okhawo amene anamzindikira Iye, amene anamuona Iye monga analili — monga Mwana wa Mulungu — okhawa anatha kuona ufumu. Awa anali okhawo amene anabadwanso mwatsopano.
Kodi ife sitinakhudzikepo mumtima kuti ngakhale abale a Yesu Kristu sanam’khulupirire Iye? Ndithudi, ngakhale ku Marko 3:21 amanena kuti: “Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka”
Kodi sanamdziwe Ambuye? Kodi sanathe kuchitira umboni za moyo wake wangwiro ndi chiyero umene anakhalamo m’nyengo zimenezo ku Nazaleti, tsiku ndi tsiku, ola ndi ola? Kodi Maliya ndi Yosefe sadawauze kuti kubadwa kwake kunali koloseredwa ndi Angelo komanso zinthu zonse zodabwitsa zimene wakhala akuchita zimene zinafotokozedwa, mwachitsanzo, ku Luka 2?
Kodi iwo sanamve umboni umene m’suweni wawo Yohane anachitira za Iye? Kodi iwo sanaone zodabwitsa zimene anali kuchita? Makamaka potengera zimene Yohane analemba: “Ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate” (Yohane 1:14); ndiponso poganizira momwe kumwamba kunatsekulidwira Iye ndi mau ochokera kumwamba nanena kwa Iye: “Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa iwe ndikondwera bwino” (Marko 1:11); abale ake ananena kuti wayaluka ndipo anafuna kumgwira Iye!
Tingafunenso umboni wina otani potengera mau amene Ambuye Yesu anayankhula: “Indetu, indetu ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona ufumu wa Mulungu!”
KUBADWANSO MWATSOPANO
Izitu sizimatanthauza zimene Nikodemo amaganiza kuti zikutanthauza, ngakhalenso zimene zimapezeka mu nzeru za akunja osapembedza ndi odalira chidziwitso chawo: kunena kuti munthu wokalamba amathanso kubadwa ngati khanda kapena kuti munthu akakalamba amadzasandukanso mwana. Mwana wobadwa kumene amakhala ndi chikhalidwe cha chibadwidwe monga cha makolo ake — si kuti chake chimakhala chabwinoko.
Seti, mwana wa Adamu wakugwayo, anali m’chifanizo cha uchimo cha atate wake (Genesis 5:3). Yobu ananena kale kuti: “Adzatulutsa choyera m’chinthu chodetsa ndani? n’nena m’modzi yense!” (Yobu 14:4). Ndipo ku Aroma 5:19 amatiuza kuti mbeu yonse ya Adamu inayesedwa yochimwa chifukwa cha kusamvera kwake. “Chobadwa m’thupi chikhala thupi” (Yohane 3:6). Ngakhale Nikodemo akanabadwanso kakhumi mu njira imene anabadwira koyamba kaja — mwa makolo ochimwa — palibe chimene chikanasintha potengera chiyanjano chake ndi Mulungu.
Munthu akuyenera kubadwanso mwatsopano, kapena kuchokera kumwamba, mwanjira ina yatsopano, kuchokera kugwero latsopano la moyo.* Ambuye Yesu akutiuza mu ndime 5 kuti moyo umenewu ukuchokera kuti. “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.” M’Malemba, madzi ndicho chitsanzo chodziwikiratu cha Mau a Mulungu pakuti amaperekedwa kwa munthu ndi Mzimu Woyera. Aefeso 5:26 amatisonyezera zimenezi mwachindunji, chimodzimodzinso Yohane 13:10 kuphatikiza ndi Yohane 15:3.
* Mau a Chigiriki akuti GENNETHEI ANOTHEN amene agwiritsidwa apa sakufanana ndi PALINGENESIASIAS omwe akupezeka ku Tito 3:5, kumene tikuuzidwa za kusambitsidwa mwa kukonzedwanso kwa Mzimu Woyera.
Madzi amayeretsa chinthu chimene chathiridwa madziwo. Mau a Mulungu amene anathiridwa ndi Mzimu Woyera amayeretsa zikhumbokhumbo zoipa, malingaliro oipa, komanso machitidwe a munthu. Nthawi yomweyo Mzimu Woyera akugwiritsa ntchito Mau pokonza ndi kuikiza moyo watsopano mwa iye — moyo wosiyana komanso wapaderadera umene sukhala ndi chikhalidwe cha umunthu wa makolo ake, koma chikhalidwe cha Iye amene wabweretsa moyo watsopanowo. “Chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu” (Yohane 3:6).
Mfundo yakuti kubadwanso kumachitika mwa Mau a Mulungu kukutsimikizidwa kawirikawiri m’Malemba. Paulo akulembera Akorinto kuti anawabala mwa Uthenga Wabwino (1 Akorinto 4:15). Ku Yakobo 1:18 tikuuzidwa kuti: “Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi.” Ndipo Petro akulemba ku 1 Petro 1:22-25: “Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi…mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa Mau a Mulungu a moyo ndi okhalitsa…” Ku 1 Atesalonika 1:5 kumeneko tikupezanso Mau ndi Mzimu Woyera kutchulidwa pamodzi.
Ambuye akuyankhula pamenepa za kufunikira kwa kubadwanso ndi cholinga cha kukaona ndi kukalowa mu ufumu wake, pakuti akuyankhula ndi Nikodemo, wamkulu wa Ayuda. Koma m’mene Ambuye akuyankhulira zikungosonyeza kuti iyi ndi mfundo yofunikira kwambiri, monga momwe tikupezera mu zolembedwa za Yohane. Kuchokera m’kuchimwa kwa munthu kufikira kutha kwa dziko lapansi, kubadwanso mwatsopano ndi kofunikira ndi cholinga chokalowa m’chiyanjano ndi Mulungu.
MWANA WA MUNTHU AKUYENERA KUKWEZEDWA
Koma pamene kuyambira ndime 12 kupita mtsogolo Ambuye akuyamba kuyankhula zinthu za kumwamba, pakuonekanso chinthu china chofunikira. Mwana wa Munthu amene ali kumwamba akudziwa za ulemerero wa kumwamba, malo okhalako Iye amene “ndiye kuunika ndipo mwa Iye monse mulibe mdima” (1 Yohane 1:5). Ndipo ngati anthu afuna kulowa mu ulemerero, pamenepo vuto la uchimo likonzedwe kaye.
Mulungu, amene wakhala akunyazitsidwa ndi tchimo la munthu, akuyenera kukhutitsidwa pokhuzana ndi tchimolo. Ndipo munthu akuyenera kuyeretsedwa ku zilizonse zimene zingamupangitse kusakalowa mu ulemerero wa Mulungu. Kodi munthu amene wachimwa kowirikiza nathamangitsidwa m’paradizo wa dziko lapansi chifukwa cha uchimo, angakalowe m’paradizo wa kumwamba, kumalo okhalako Mulungu mwini?
Kodi zimenezi zingatheke bwanji pokhapokha Iye, amene ali Mulungu ndi Munthu mwa m’modzi, akamalize ntchito imene zonse zofunikira zikakwaniritsidwe? “Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupirira akhale nawo moyo wosatha mwa Iye” (Yohane 3:14,15).
Kodi chimenechi si chinthu chachikulu chimene Mulungu angathe kutipatsa?
Palinso zinthu zina zambiri zolumikizana ndi zimenezi. Tingathe kulira “Abba, Atate” chifukwa Mzimu Woyera amachitira umboni pamodzi ndi moyo wathu watsopano mwa ife kuti tili ana a Mulungu (Aroma 8:15,16). Ndife olandira cholowa pamodzi ndi Kristu ndipo pang’ono ndi pang’ono tidzalamulira ndi kuweruza dziko lapansi pamodzi ndi Iye (Aroma 8:17; Aefeso 1:10,11; 1 Akorinto 6:2,3; ndi zina zotere).
1 Yohane 3:1 ikutiika pa mlingo umodzi ndi Ambuye Yesu Kristu posakhala ozindikiridwa ndi dziko lapansi. Ndime 2 ikutiuza kuti akadzaonetsedwa tidzakhala ngati Iyeyo, pakuti tidzamuona monga alili. 1 Yohane 4:17 akunena kuti potengera m’tsiku la mlandu, tili monga iyeyu ali kumwambako, momwemo ifenso m’dziko lapansi.
Mu ndime 19 timapezeka kuti tikukonda, chifukwa tili ndi chikhalidwe cha kumwamba chimene chili chikondi, kodi simomwemu? Timagonjetsa dziko lapansi (1 Yohane 5:4). Kenako timazindikira kuti Malemba amatenga zinthu zochuluka.
Kodi kukhala pa chiyanjano ndi Atate komanso Mwana wake si chinthu cha mtengo wapatali? Molingana ndi mau a Ambuye Yesu Kristu ku Yohane 3 sitingathe kuona kapena kulowa mu ufumu wadziko lapansi. Tinali ochimwa osokera amene timayembekeza chilango kumoto, adani a Mulungu, odedwa m’maso mwake.
Tikum’dziwa Atate ndi Ambuye Yesu Kristu (1 Yohane 5:20) - osatinso monga zolengedwa zimadziwira Mlengi, komatu monga ife tilili. Tili m’chiyanjano ndi Atate komanso Mwana Wake Yesu Kristu. Chiyanjano chimenechi sichidzakhala cha pang’onopang’ono kumwamba kokha. Koma ngakhale pamene tidakali padziko lapansi, kulekanitsidwa kunja ndi ena onse amene ali pansi pa mphamvu ya Satana, tili ndi chiyanjano chimenechi.
Pamene tazindikira zimenezi ndi kudzipanga kukhala zoona m’moyo wathu, kodi chisangalalo chathu sichingakhale chodzala?
Ndi mafuno onse abwino,
H.L.H.
MUTU 9
CHIYANJANO NDI ATATE KOMANSO MWANA
Okondedwa Amzanga,
Taona kuti aliyense wokhulupirira mwa Ambuye Yesu samangolandira chikhululukiro cha machimo chokha, komanso amalandira moyo wosatha kupyolera m’kubadwanso mwatsopano. Iye anabadwa mwa Mulungu (Yohane 1:13), ndipo potero amakhala nawo moyo wa umulungu, chikhalidwenso cha umulungu (2 Petro 1:4).
Moyo umenewu m’kupambana kwake umatchedwa moyo wosatha, ndipo 1 Yohane 5:20 ikunena za Ambuye Yesu Kristu: “Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha” Ambuye Yesu Mwini ndiye moyo wathu.
Mfundo imeneyi ili ndi zotsatira zopanda malire kwa ife. Tatengedwa m’kukonderedwa ndi Wokondedwayo (Aefeso 1:6), ndipo zatanthauzidwa “m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake” (Akolose 1:13). Timaima pamaso pa Mulungu mukuvomerezedwa kwa Iye amene Mulungu amamutchula “Wokondedwa.” Ife tinadziwika ndi Ambuye Yesu. “Dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye” (1 Yohane 3:1).
Tili padziko pano monganso Iye (tsopano ali kumwamba — 1 Yohane 4:17). “Pakuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye” (1 Yohane 3:2). Faniziraninso 1 Yohane 4:12,13 ndi Yohane 1:18. Ndipo 1 Yohane 5:20 imanena kuti: “Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo.” Apatu akuphatikiza zinthu zonse.
Mu nthawi ya chilengedwe Mulungu anapereka chidziwitso kwa Adamu. Pamenepa ndi pamene munthu amasiyanirana ndi chinyama. Koma chidziwitso cha munthu chinali cha dziko lapansi, kotero kuti amangodziwa zinthu za dziko lapansi. Angelonso sangam’dziwe Mulungu, ngakhale iwo chilengedwe chawo n’chokwererako kusiyana ndi munthu. Iwo ndi atumiki amphamvu amene amakhala tcheru kutumikira molingana ndi chifuniro cha Mulungu; koma amalakalaka zinthu zimene zaperekedwa kwa ife (1 Petro 1:12).
Koma tsopano kwa ochimwa osochera amene anali adani ake, koma amene avomereza Ambuye Yesu Kristu, Mulungu wawapatsa Mwana wake ngati moyo watsopano. Nthawi yomweyo, mwa Iye komanso kudzera mwa Iye, analandira chidziwitso chimene akum’dziwira nacho Mulungu.
Tingathe kuona ulemerero wake wovumbulutsidwa, umene posakhalitsa dziko lapansi udzauona, pamene Ambuye Yesu Kristu adzatulukira m’mitambo n’kubweranso padziko lapansi, pamene diso lililonse lidzamuone. Koma tidzamuona monga momwe alili — osati monga amadzivumbulutsira yekha. Tingathe kumvetsetsa malingaliro ake tsopano. Timaona ulemerero wake wa m’kati ndipo umadzala m’mitima mwathu.
Timakhala ndi kumva komanso kuganiza mofanana ndi Mulungu. Amatsegulira mtima wake kwa ife ndi kuyankhula nafe za zinthu zimene zadzala mu mtima mwake, ndipo tingathe kumvetsa mau ake ndi kugawana naye m’mene Iye akumvera. Tili ndi:
CHIYANJANO NDI ATATE KOMANSO MWANA WAKE, YESU KRISTU
Kodi chimene chimadzala mu mtima mwa Atate ndi chiyani? Kodi si Mwana wake ndi ulemerero wa umunthu Wake ndi ntchito Yake? Pamene Mwana anali padziko lapansi pano “kunamkomera Atate kuti chidzalo chonse chikhalire” mwa Iye (Akolose 1:19). Pachiyambi pa utumiki wa pagulu wa Ambuye (Luka 3:22) komanso cha kumapeto (Mateyu 17:5) Atate ananena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa mwa iyeyu ndikondwera.” Zitatha zimenezi inabwera ntchito ya pa Gologota!
Inaliditu ntchito imeneyi kwa Atate! “Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso” (Yohane 10:17). Indedi, atate am’konda Iye amene modzipereka anakhomedwa pa mtanda, amene anafa kulemekeza dzina la Mulungu ndi kuchita chifuniro chake, amene mpaka kumapeto kwake “anasenza machimo athu mthupi mwake” (1 Petro 2:24), anapangidwa “kuyesedwa wochimwa m’malo mwathu” (2 Akorinto 5:21), anatenga chiweruzo cha Mulungu ndipo anakanidwa ndi Iye, amene mu zonsezi anali wangwiro — “Kristu amene anadzipereka yekha wopanda chirema kwa Mulungu” (Ahebri 9:14).
Atate amatiuza, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa,” ndipo ife timayankha “Uyu ndiye Mpulumutsi wathu wokondedwa.” Atate amanena kuti, “Chifukwa cha kundikonda Ine (Eksodo 21:5) anatenga masautso onse pa Gologota ndi kutsiriza ntchito yonse.” Ndipo ife timayankha, “Kristu anatikonda, nadzipereka yekha m’malo mwathu” (Aefeso 5:2). Ndipo pa ine ndekha ndimati, “Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine” (Agalatiya 2:20).
Munthu wa ulemerero yemweyu amene amakwaniritsa mtima wa Atate yemweyunso amakwaniritsa mtima wanga. Atate amationetsera ulemerero wa Mwana, ndipo timayankhula kwa Atate pa zonse zimene tazipeza mwa Mwana. Ichi ndicho chiyanjano — chimene aliyense amayenereka kumva ndi kulakalaka. Munthu yemweyu amakwaniritsa mitima yathu ndi chisangalalo komanso chimwemwe.
Kodi zimenezi sizilinso chimodzimodzi ndi Mwana? Iye wavumbulutsira Atate kwa ife. Tinamva Iye akunena, “Abba, Atate” (Marko 14:36) ndipo tsopano nafenso timati, “Abba, Atate” (Aroma 8:15).
Kodi umenewu si mwayi waukulu kuposa mwayi ulionse — kumumvetsetsa Mulungu, inde,kumudziwa Iye! Osati kungomva bwino ndi madalitso ake ndi zinthu zakumwamba, komanso kumumva bwino Mulungu mwini Kukhala ndi chiyanjano mu zimenezi ndi Mulungu Atate komanso Mulungu Mwana!
Palibenso chinthu china chokoma kuposa chimenechi. Tikapanga zimenezi kukhala zoona m’moyo mwathu, mitima yathu idzakhala yokondwa padziko lino lapansi. N’chifukwa chake mtumwi akunena kuti: “Ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe” (1 Yohane 1:4).
MULUNGU NDIYE KUWALA, NDIPO MWA IYE MULIBE MDIMA ULIONSE
Chiyanjano chimenechi ndi Atate komanso Mwana chikuyenera ntheradi, kugwirizana ndi chikhalidwe cha Mulungu. Mulungu ndi kuwala, ndipo ife tikuyenera kukhala m’kuwala kuti tikakhale mu chiyanjano chimenechi. Ife amene “kale tinali mu mdima” tili “tsopano m’kuwala mwa Ambuye” (Aefeso 5:8).
Tikuyenda m’kuwala, pamenepo nkukhala m’chiyanjano wina ndi mzake. Ndipo mwazi wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu uli pamenepo ngati msanamira kapena maziko a pamalo tilipo komanso ngati umboni wa kuyenerezedwa kwake.
Ku 1 Yohane 1:7 funso si lakuti timayenda bwanji, koma timayenda kuti. Tikanena nkhani ya kuyenda mu mgwirizano ndi kuwala, ndi zachidziwikire kuti ndi nkhani yokhudza machitidwe athu a tsiku ndi tsiku. Koma pamenepa ikukhudza nkhani ya komwe timayenda. Ndipo aliyense amene anabadwa mwatsopano, amene anamasulidwa mu ulamuliro wa mu mdima ndipo wayenerezedwa kugawana nawo mu cholowa cha oyera mtima m’kuwala (Akolose 1:12,13), ameneyo akuyenda m’kuwala.
Ndipo pamenepo, ngati chitsimikizo kuti ndili pamalo panga, ndi mwazi umene umatsuka machimo onse. Kugwiritsira ngati chifanizo: Ngati ndikugwira ntchito ndi manja mu ndowa ya madzi osakaniza ndi sopo, manja anga sangade. Mphamvu ya madzi a sopo, imene inatsuka manja anga kumayambiriro, imathandizira kuti manja anga asadenso.
Akhala bwanji akuda pamene ali m’madzi amene ali ndi kuthekera kwa kutsuka zonse zooneka zakuda. Chimodzimodzi mphamvu ya mwazi, imene imalamulira m’kuwala, ndi chitsimikizo kuti ine ndili mu mgwirizano ndi kuwalako.
Koma izi sizimasintha mfundo yakuti chikhalidwe changa chakale chidakalipobe. Ngati ndingakane zimenezi, ndikunena kuti ndilibe uchimo, ndidzinyenga ndekha, ndipo choonadi mwa ine mulibe. Ndiponso ndikanena kuti sindinachiteko zinthu zolakwa, kapena kuti, sindinachimweko, ndimuyesa Mulungu kukhala wabodza, pakuti Mulungu ananena kuti: “Onse anachimwa.”
1 Yohane 1:10 sakunena kuti, “Ngati tinena kuti sitimachimwa” koma akunena kuti, “sitidachimwa,” kugwiritsa mau ofotokoza za m’mbuyo. Mau a Mulungu sakunena kuti ndi kofunikira kuti okhulupirira achimwe. Tili ndi chilengedwe chatsopano chimene sichimachimwa, ndipo tili ndi mphamvu ya umulungu m’kati mwathu, Mzimu Woyera, amene amatipangitsa ife kuyenda molingana ndi moyo watsopano. Mayendedwe athu ali m’kuwala, pomwe timaona bwino zonse zosagwirizana ndi kuwala.
Mwachisoni tonse tikuyenera kunena, “Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri” (Yakobo 3:2). Koma palibe pothawira pamenepa.
Ndikhulupirira tiona bwino mfundo imeneyi mu kalata yathu yotsatira, kuti kalatayi isatalike kwambiri.
Ndi mafuno onse abwino,
H.L.H.
MUTU 10
KRISTU WOTIYIMIRA MLANDU
Okondedwa Amzanga,
Tsopano ndipitiriza kuchokera pamene ndinasiyira m’kalata yapitayi, ndipo nditenga mfundo:
NGATI WOKHULUPIRIRA ACHIMWA
Ngati ife okhulupirira tichimwa, chimachitika ndi chiyani? Kodi zimenezi zimatisintha kukhalabe ana a Mulungu? kodi tikuyenera kuchotsedwa pamaso pa Mulungu?
Tili ndi yankho ku Ahebri 9 ndi 10. Kristu anatipezera chiombolo chamuyaya. “Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa” (Ahebri 10:14). Chiyanjano chathu ngati olengedwa a Mulungu chakonzedwa kwa nthawi zonse. Tabweretsedwa m’chiyanjano cha ana ndi Atate. Chiyanjano chimenechi sichingasokonezedwe.
Kodi Atate wathu, amangoyang’anira machimo a ana ake? Atate wathu ndi Kuwala ndipo ndipo mwa Iye mulibe mdima ulionse. Iye ndi woyeretsetsa kotero sangangoyang’anira tchimo. Akuyenera kupatsidwa ulemu ndi iwo akubwera chifupi ndi Iye. Mulungu angathe kulekerera machimo a osakhulupirira, inde, iwo a m’dziko lakudana ndi Mulungu — koma sangalekerere machimo alionse mwa ana ake.
Kodi zingatheke bwanji Mulungu Woyera, kukhala m’chiyanjano ndi tchimo kapenanso kwa munthu amene waipitsidwa ndi tchimo. Ndi chifukwa chake chiyanjano chathu ndi Atate komanso Mwana wake chimasweka nthawi yomweyo pamene taganiza maganizo a uchimo, ndi mau onse auchimo kapena wopanda pake komanso machitidwe a uchimo.
Chiyanjano chimenechi sichibwenzeretsedwa pokhapokha tchimolo lachotsedwa m’njira ya umulungu. “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chili chonse” (1 Yohane 1:9). Kudzera m’kuvomereza ndi kuzindikira kulakwa kwathu timayeretsedwa.
KUZINDIKIRA KULAKWA KWATHU NDIYO NJIRA YOKHAYO YAKUSUNGIRA CHIYANJANO CHATHU
Imeneyi ndi mfundo imene timaipeza m’Buku lonse Lopatulika, mu Chipangano Chakale ndi Chatsopano chomwe. Tiyeni tione zitsanzo zina kuchokera m’Chipangano Chakale.
Ku Levitiko 4 ndi 5 komanso mbali ina ya mutu 6 ndi 7 timapeza malangizo amene anaperekedwa kwa m’Israeli amene adachimwa. Apatu sakufotokoza za wochimwa kutembenuka, ngakhale mlaliki wina akhoza kugwiritsa ndime imeneyi kulalikira uthenga wabwino. Mitu imeneyi ikuonetsera Israeli ngati anthu obweretsedwa kwa Mulungu pansi pa maziko a nsembe ya tsiku lalikulu la chiombolo (Levitiko 16), ndipo mkatikati mwa iye amene Mulungu amakhalira pansi pa kupitiriza nsembe yopsereza (Eksodo 29:38-46).
Ndipo tsopano kuti anabweretsedwa m’kupezeka kwa Mulungu monga anthu ake ndipo atsitsimuka m’kukomoka kumene kunawafikira “kwa ufulu mwa Wokondedwayo” (Aefeso 1:6; Levitiko 1 ndi 7:8); tsopano kuti analandira chinthu ku mitima yawo (nsembe ya ufa ku Levitiko 2) pamene anali pa ulendo m’chipululu: ndipo tsopano kuti angathe kukhala pa chiyanjano ndi Mulungu pakutenga nawo ndi kusangalala ndi chinthu chimenechi (nsembe ya mtendere yoyamika ku Levitiko 3 ndi 7:11-34); tsopano nkhani yokhudza chidetso cha tsiku ndi tsiku inayenera kuthetsedwa.
Levitiko 5:1-4 ikutionetsera poyamba magulu onse akuluakulu atatu a chidetso pamoyo wa tsiku ndi tsiku. Ndime 1, ngati munthu alephera kuchitira umboni motsutsana ndi choipa kapenanso kugwirizana ndi chabwino. Kusiyakonso kanthu kena, kungathe kukhala tchimo.
Ndime 2 ikukamba za chidetso chochokera mu zinthu zochokera kunja, kukamba zokhudzana ndi zotsatira zosafuna kusiyanitsidwa ndi zinthu za dziko lapansi. Ndime 4 ikufotokoza za zotsatira za kusaugwira mtima ndi kukhala munthu wosadziletsa — chidetso chimene chimachokera mkati mwa mitima yathu yomwe. Ndime 15 kupita mtsogolo ikupitiriza kuonetsera chinachake chimene Mulungu anadzisungira yekha pa ubwino wa ife tomwe. Ndipo mutu 6:1-7 akufotokoza za kutenga kapena kusunga kanthu kamwini wake.
Ngati m’Israeli achimwa, kodi adzayeretsedwa bwanji? Panali njira imodzi yokha, ndipo ikufotokozedwa pa mutu 5:5,6 “Ndipo kudzali, atapalamula chimodzi cha izi, aziulula chimene adachimwa nacho; nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndipo msoti wa nkhosa, kapena msoti wa mbuzi, ukhale nsembe ya uchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetedzera chifukwa cha kuchimwa kwake…” Zinthu zina zingathe kuonjezedwa pamenepa, monga kuonjezera pa zinthu zimene zatengedwa kwa Mulungu kapena m’bale wako (5:16;6:5). Koma chinthu choyambirira, chofunikira kuchita, chinali kuvomereza machimo ndi kubweretsa nsembe yopalamula.
Kuzindikira kulakwa kwako — kuulula machimo ako ndi kulephera kwako ndizo zinthu zabwino kuchita pokhudzana ndi kukhululukidwa ndi kubwenzeretsedwanso (onani, mwachitsanzo, 1 Akorinto 11:31 ndi 1 Yohane 1:9). Mulungu akufuna kutibweretsa ku kuzindikira kulakwa kwathu koona; kunena kuti, akufuna tizindikire osati zimene takhala tikuchita zokha, komanso m’mene ifeyo tilili, monga Davide anachitira ku Masalmo 51:5-7. Kotero akulozetsa maso athu pa mtanda, kuti pamenepo tikaphunzire kuti tchimo ndi chiyani. Si kuti mwazi wa Kristu ukaikidwenso pa ife kawiri. Izi zinachitika kamodzi kokha kwamuyaya.
Koma tikuyenera kuzindikira kuopsa kwa machimo — ngakhale tchimo limene ndangochita kumene lija, timachita zimenezi pakuona zimene Ambuye Yesu anatichitira pakuvutika pa mtanda chifukwa cha machimo athu (nsembe yopalamula). Ku Levitiko mutu 1-7, pamenepo, tikupeza osati mtandawo ayi, koma kuyang’ana kwa pa mtanda. Mtanda monga maziko a kuyandikana kwathu ndi Mulungu ukupezeka pa Levitiko 16 ndi Eksodo 29.
Inde, pakungoyang’ana m’mene Ambuye Yesu adavutikira pa Gologota chifukwa cha machimo athu timaphunzira kuopsa kwake kwa tchimo. Iye anakanidwa ndi Mulungu pamenepo, anayenera kutenga chiweruzo cha Mulungu, anayenera kufa, chifukwa Iye “amene anasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake pa mtanda” (1 Petro 2:24). M’njira imeneyi timatha kudziweruza tokha moonadi ndi kudzimvera chisoni pa zimene takhala tikuchita.
Tiyeni tisachepetse tchimo. Komanso tisaiwale kuti kuvomereza kutsutsika kwathu ndi njira yokhayo ya kubwenzeretsedwa m’chiyanjano ndi Mulungu — kuvomereza pamaso pa Mulungu, komanso pamaso pa anthu, pamene anthu apsinjika ndi zimene tawachitira.
MACHIMO OSADZIWIKA
Koma tsopano timafika pa vuto lalikulu. Nthawi zambiri timachita machimo osadziwa kuti tachimwa, ndiponso nthawi zambiri timaganiza kuti tikuchita zabwino. Komatu kusadziwa sikungatipangitse ife kukhala osalakwa! “Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake” (Levitiko 5:17). Ndi chifukwa chake Davide akupemphera ku Masalmo 19:12 “Mundimasule kwa zolakwa zobisika.”
Ngati tivomereza machimo amenewa ndi kupeza kubwenzeretsedwa m’chiyanjano ndi Atate, tikuyenera koyambirira kuzindikira machimo athuwo. N’chifukwa chake mitu imeneyi ya ku Levitiko ikunena mobwerezabwereza, “Ngati tchimo lake, wachimwa, nakazindikira...” Kodi akuyenera kuchita zimenezi ndi ndani? Ndani amene angatizindikiritse za malingaliro athu, malankhulidwe athu, ndi machitidwe athu amene anthu ena samawadziwa?
Ndipo ndi ndani amene angatitsutse pamene tikuona ngati tikulondola? Pa zimenezinso, chikondi cha Mulungu chapereka njira. “Tiana tanga izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama” (1 Yohane 2:1). Tiyeni tiwerenge ndime imeneyi mosamalitsa ndi kuilingalira.
KRISTU WOTIYANG’ANIRA
Mau a m’Chigiriki akuti “parakletos” amene akutanthauzira “woyang’anira,” akupezeka ku Yohane 14 ndi 16 komanso mu ndime iyi yokha. Ku Yohane 14 ndi 16 akukamba za Mzimu Woyera ndipo akutanthauzidwa ngati “nkhoswe.” Mau oonjezera pansi pa tsamba m’buku la J.N. Darby amatiuza kuti mau amenewa amatanthauza, “Iye amene amatenga mavuto a aliyense ndi kumuthandiza.” Ena amatanthauzira mau amenewa a ku 1 Yohane 2 kuti “wotiimira pa mlandu” kapena “wamkulu wa malamulo”.
Ambuye Yesu Kristu akutenga udindo umenewu kumwamba m’malo mwathu. Iye sakunyamula udindowu pamaso pa Mulungu, koma pamaso pa atate, pakuti molingana ndi Mulungu, mlandu wathu unathetsedwa pa mtanda paja.
M’kalata yapita ija taona kuti Ambuye Yesu ndi Wansembe wathu Wamkulu, amene Iye ndi Mulungu amatipembedzera ife potengera kufooka kwathu ndi zina zochitika padziko lapansi. Pamenepa tikupeza chimene Ambuye Yesu ali, kapena ntchito yawo molingana ndi machimo amene timachita tsiku ndi tsiku.
Iye ndi amene amatiimira ife pa milandu, wotiyang’anira ndi Atate pamene tachimwa. Sakhala wotiimira milandu pamene talapa ndi kuvomereza machimo kokha. Ayi ndithu, ngakhale pa nthawi imene ndachimwa Iye adakali wondiimira mlandu kumwamba amene amakamba za milandu yanga ndi Atate.
Kodi tanena kuti Wotiyang’anira ameneyu ndi ndani? Iye ndi Yesu Kristu Wolungamayo. Iye amakhala bwino pa mlingo wa kulungama kwa Atate, komanso nthawi yomweyo Iye ndi chilungamo changa (1 Akorinto 1:30).
Koma osati zokhazi ayi! Iye anatsiriza ntchito imene ili ya ngwiro mwakuti Iye si wotiombola kokha ku machimo athu, komanso Iye ndi momboli wadziko lonse lapansi. Izitu zili kumbali zonse Umunthu wake ndi Ntchito zake, Iye ali wovomerezeka kwathunthu pamaso pa Atate — komanso pamene Iye ali wondiyang’anira, pamene ndachimwa.
Koma pa nthawi yodutsa taona kuti pali chikhululukiro pokhapokha tavomereza. Choncho gawo lachiwiri la utumiki wa Ambuye Yesu ngati Wotiyang’anira ndi lakuti amatanganidwa kwambiri ndi ife ndi kutibweretsa ku kuvomereza uchimo wathu.
KUSAMBITSA MAPAZI
Pa usiku omwe Ambuye anagwidwa anayambitsa utumiki umenewu ngati chizindikiro. Iye amafuna kukhazikitsa mgonero wake, chisonyezo cha chiyanjano ndi Iye, Mpulumutsi amene anamwalira, komanso onse a mthupi la Kristu (1 Akorinto 10:16,17). Koma pakadakhala bwanji chiyanjano pakati pa ophunzira amene anadetsedwa ndi Ambuye amene anafa kusonyeza kuononga tchimo! Ichi chikungosonyeza chiweruzo cha odetsedwa (1 Akorinto 11:26-32).
Tsopano, pa chizindikiritso chonse cha zomwe Iye ali, koma chifukwa chikondi chake chinapita pa mlingo waukulu nthawi yomweyo chinafikanso pamapeto, Ambuye anatenga malo a kapolo nasambitsa mapazi awo.
Ndipo Mulungu anagwiritsa ntchito kusamvetsetsa kwa Petro (pakuti Iye sanamvetsetse kuti zimene Ambuye amapanga zimakhala zabwino nthawi zonse, ndipo kuti tikuyenera kugonjera ku zimenezi nthawi zonse, ngakhale mu nyengo imene sitikuzimvetsetsa) kuti kusambitsa kwa mapazi kukhale ndi tanthauzo lomveka kwa ife.
Ophunzira anali oyeretsedwa chifukwa anasambitsidwa kwathunthu (kusambitsidwa — kubadwanso). Koma ngati anafuna kukhala nalo gawo ndi Iye, kukasangalala mu chiyanjano ndi Iye, anayeneranso kuyeretsedwa ku zidetso zimene anakumana nazo pa mayendedwe awo a tsiku ndi tsiku (Yohane 13: 8-11).
KUKANA KWA PETRO
Uthenga Wabwino umafotokoza kwa ife m’mene Ambuye amagwirira ntchito imeneyi pa ife. Timapezanso zimenezi, mu nkhani ya Petro. Petro anataya chiyanjano chake ndi Ambuye. Zochitika zazikulu zinali zisanachitike, pakuti iye mwini samadziwapo china chilichonse ndipo palibe amene anamudziwitsa za chimenechi. Koma pamene Ambuye ananena kuti onse adzakhumudwa chifukwa cha Iye, zinali zodziwikiratu kuti Petro amayembekezera kenakake kwa iye yekha.
Indedi, anatsimikizika kuti chikondi chake ndi kukhulupirika kwake kukuposa wina aliyense. “Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse” (Mateyu 26:33). Petro sakanayankhula izi akanakhala kuti anali mu chiyanjano ndi Ambuye, pakuti kumeneko chithupithupi ndi kudzikweza zilibe malo.
Ambuye anagwiritsira ntchito mau ake a Petro kumuchenjeza, komanso kumudziwitsa kuti Iye, Ambuye, amadziwa zonse. Petro anayenera kukumbukira zimenezi pamene anamkana Ambuye. Ndipo anayenera kulimbikitsidwa ndi malingaliro akuti, ngakhale Ambuye wadziwa zimenezi, sanamkane ayi, kapenanso kuti achita zimenezi.
Ubwino ndi chisomo chotani ichi! Chikondi chotani! Chisamaliro chotani! Petro asanachimwe, Ambuye amamupempherera. Osati kuti Satana asakamuyese — ayi ndithu, Petro anafunika kugwa kumeneku kuti akadzidziwe yekha. Mau abwino, odzichepetsa ochokera kwa Ambuye sanakwaniritse cholinga chimenechi, ngakhalenso mau a chindunji ochokera mkamwa mwa Ambuye sanatulutse zotsatira.
Kotero Ambuye sanapemphere kuti mayesero asafike kwa Petro, koma kuti chikhulupiriro chake chisalephere. Komanso kuti Petro asakhumudwitsidwe ndi kugwa kwakeko, Ambuye anampatsiratu maitanidwe nthawi imene anabwenzeretsedwa.
Koma Petro anali ochulukidwa kotero kuti palibe chimene chinafikira chikumbumtima chake. Mosakaika konse anali wovutika ndi mau amene Ambuye Yesu anayankhula kwa iye:“Simukhoza kuchezera ndi Ine mphindi imodzi” (Mateyu 26:40). Komabe mauwa sanamupangitse kudziweruza yekha, kapenanso mfundo yakuti iyenso anathawa namsiya Ambuye yekha mu mphamvu ya adani Ake (Mateyu 27:56).
Inde, ngakhale anamukana Ambuye, pamene anayamba kulumbira ndi kutemberera, “Sindim’dziwa ine munthu uyu” - Petro yemweyu amene ananena kuti: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wa moyo” ngakhale pamenepa Petro sanatembenuke. Mtima wa munthu ndi womvetsa chisoni!
Komano, chikondi chodabwitsa! Mu nyengo imeneyo pamene akapolo aja amamkwapula, kum’bwanyula, komanso kumlavulira ku nkhope yake (Mateyu 26:67), Ambuye anatembenuka namyang’ana Petro. Kuyang’ana kumeneku m’nyengo imeneyi, kuphatikiza ndi mau a Ambuye kumene kunatsimikizidwa ndi kulira kwa tambala kunabweretsa chikumbutso, ndi kutsegula maso a Petro. “Ndipo anatuluka kunja ndi kukalira kwambiri.”
KUBWENZERETSEDWA
Koma ngakhale zinachitika izi ntchito ya Ambuye sinathe. Ngati chinthu choyambirira kuchita atauka anatumiza uthenga umene anafotokoza za Petro (Marko 16:7), ndipo zitapita izi anakhala pa mkhumano ndi iye (Luka 24:34). Malemba samafotokoza zimene amakambirana nthawi imeneyi.
Ambuye amakhala ndi mau apadera kwa liyense mwa anthu ake, mau oyenera kwa iye amene akuuzidwa mawuwo. Koma zitatha izi timapeza kuti mkhumano umenewu unali wopweteka komanso wa mdalitso, mkhumano umenewu ukufotokozedwa ku Yohane 21.
Kodi sitikananena kuti kuchitisidwa manyazi pagulu kwa Petroku sikunali koyenerera? Pamene tikuganizira za zimenezi, kodi sitikuganiza kuti kunali kusowa kwa chikondi? Petro anabwera kwa iye yekha, sanatero kodi? Analira kwambiri, sanatero kodi?
Koma Iye, amene ali ndi chidziwitso changwiro cha mtima wa munthu komanso ali ndi chikondi kwa onse amene ali ake, ndipo amene amaonetsa zonsezi mwa nzeru zakuya, anadziwa chimene chinali chabwino kwa Petro.
Ndipo tsopano pamene Petro, anafika moonadi pa mlingo wa kudzisanthula yekha, osati kungodzisanthula kapena kungodziweruza chifukwa cha machitidwe ake, koma iye yense — pamene anazindikira kuti zinatengera kudziwa konse kwa Mulungu kukazindikira chikondi cha Mulungu mwa iye — pamenepo Ambuye akanam’bwenzeretsa ndi kumutuma kuyang’anira nkhosa Zake ndi kudyetsa ana Ake a nkhosa ndi nkhosa Zake zimene.
Umenewu ndi utumiki wa Ambuye wathu monga Wotiyang’anira ndi Atate. Kodi tikanakhala tili kuti padakapanda Iye kukhala Wotiyang’anira wathu? Lingaliro lililonse loipa, mau onse wopanda pake, machitidwe onse a odziyenereza amaononga chiyanjano chathu. Ndipo chiyanjano chimenechi sichibwenzeretsedwa pokhapokha tavomereza zoipa ndi kudziweruza tokha.
Wotiyang’anira wathu amandipempherera ndisanachimwe kuti chikhulupiriro changa chisalephere. Amayankhula nane kudzera m’Mau ake ndi cholinga chakuti ndikafike pa mlingo wa kudziweruza ndekha ndisanachite uchimo ulionse. Amandiyang’ana mu nyengo yoyenerera ndi kugwiritsa ntchito abale, mabuku, m’zochitika — inde, ngakhale nkhuku ngati ndi koyenerera kutero — kubweretsa mau ake ku chikumbutso changa.
Amanditsogolera ku kudziweruza ndi ku kuvomereza, cholinga kuti chiyanjano ndi Atate komanso Mwana chikabwenzeretsedwe. Iye ndi Wondiyang’anira wanga, Wakundiimira mlandu ndi Atate. Iye samapuma kufikira nditabwenzeretsedwa kwathunthu, kufikira kubwenzeretsedwa kwathunthu kwachitika.
Ngakhale pakali pano mu ulemerero amanditumikira ndi kusambitsa mapazi anga, cholinga kuti ndikakhale ndi gawo ndi Iye, kuti chimwemwe change padziko pano chikakhale chodzala.
Ndine Mzako,
H.L.H.
MUTU 11
KUYERETSEDWA
Okondedwa Amzanga,
Mwamsangala tsopano ndikambe nanu zokhudza kuyeretsedwa. Koma tisanayambe kukamba zimenezi poyamba ndi kofunika kupima zimene Mau a Mulungu amatanthauza pa nkhani imeneyi. M’makambidwe achindunji mau akuti woyera amatanthauziridwa kuti munthu amene alibe tchimo kapena kulephera, kapenanso mwina osakhala ndi tchimo lodziwika kapena kulephera kowonekera.
Pa chifukwa chimenechi okhulupirira amene asocheretsedwa ndi chiphunzitso cha chiyero chotere nthawi zina amaona ngati achita bwino pa kuyeretsedwa kwawo chifukwa sanachiteko machimo owonekera kapena odziwika ku gulu.
Chifukwa cha maganizidwe otere, Paulo akunena ku 1 Akorinto 4:4 kuti samadziwa kanthu kakumupalamulitsa, koma kuti sanalungamitsidwe ndi zimenezi. Ndipo ku Masalmo 19:12 Davide akupemphera kuti amasulidwe ku zolakwa zobisika. Onaninso 1 Yohane 3:20 ndi Levitiko 5. Pamene Ambuye adzabwera “adzaonetsera zobisika za mdima; ndipo pamenepo yense adzakhala nawo uyamiko wake wa kwa Mulungu” (1 Akorinto 4:5).
Ngati sitikuonanso cholakwika chilichonse mwa ife, chimenechi si chisonyezo kuti mwa ife mulibedi koipa kena kalikonse. Koma ndi ndani amene saona zolakwika zambirimbiri mwa iye yekha pamene m’kuunika kwa Mulungu ayesa moyo wake ndi Mau a Mulungu?
Koma kupatula Lemba limeneli tiyeni tionenso kuti kupanda tchimo ndi kuyeretsedwa si chinthu chimodzi. Ku Eksodo 28:38 timawerenga zokhudza mphulupulu ya zinthu zopatulidwa; ndipo ku Aefeso 1:4 ndi Akolose 1:22 akuti tikhale woyera ndi wopanda chilema. Chiyero ndi Kupanda uchimo kusiyanitsidwa ndithu.
KODI KUYERETSEDWA NDI CHIYANI?
Tikatsatira bwino ndime zambiri m’Baibulo zimene zimafotokoza za “chiyero” ndi “kuyeretsedwa,” ndikukhulupirira kuti zikhala zomveka bwino kuti kuyeretsedwa kumatanthauza kupatulidwa. Kwa ife zimatanthauza kupatulidwa ku zinthu zonse zimene timakonda kale ndi cholinga chakuti tikayeretsedwe kwa Mulungu. Zikutanthauzanso kuti tikafunitsitse kusenza zoonetsera chiyanjano chimenechi ndi Mulungu komanso kuyeretsedwa kwa Iye. Onani, mwachitsanzo, Numeri 6:1-11.
Ndipo chinsinsi kapena njira yake ya chiyero siili m’manja mwathu. “Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha” (1 Samuel 2:2). “Chifukwa Inu nokha muli woyera” (Chivumbulutso 15:4). “Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima” (1 Petro 1:16).
Ambuye yekha ndiye muyeso wa chiyero. Aliyense amene amadziyesa yekha mwa iye yekha ali wopusa, monga mau amanenera: “Koma iwowa podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru” (2 Akorinto 10:12). Ndi zachidziwikire kuti Mulungu yekha ndiye angathe kuweruza m’mene mlingo wathu wa moyo wa umulungu ukufikira.
Ku Yohane 17:17 Ambuye Yesu akupemphera: “Patulani iwo m’choonadi; mau anu ndi choonadi.” Choonadi ndi chimene Mulungu wachivumbulutsira chokhudza Iye mwini komanso chimene chikutsatira pamenepa — chiyanjano chathu ndi Iye ndi chopambana ndipo chiuyenera kukhala choncho ndithu! Ichi ndi chifukwa chake Ambuye Yesu ananena za Iye yekha kuti ali Choonadi (Yohane 14:6).
Iye anaonetsera poyera Mulungu, sanatero kodi (Yohane 1:18)? Komanso chimodzimodzi Mau a Mulungu, m’mene Mulungu anadzivumbulutsira yekha, ndi oona.
Kudzera mu choonadi — kudzera mu chimene Mulungu anadzivumbulutsira zokhudza Iye mwini komanso zofunikira zake pa munthu — amene amakhala wolekanitsidwa ku zinthu zonse zimene munthu analumikizidwa nazo ndi cholinga chakuti akakhale wake wa Mulungu.
M’Chipangano Chakale sitinapezeko vumbulutso la Mulungu. M’menemo anadzivumbulutsira yekha monga Yehova, amene anali ndi kachisi womangidwa ndi manja padziko lapansi pakati pa anthu ake, m’mene amakondwera kukhalamo. Chomwechonso m’Chipangano Chakale kuyeretsedwa kukulumikizidwa ndi zimenezi.
Phiri, mzinda wa Yerusalemu, chihema, kachisi, ansembe, Alevi, inde ngakhalenso anthu onse, zipangizo zogwirira ntchito, nsembe, ndi zina zotere zimayeretsedwa. Zonsezi zimakhala zolumikizana ndi Yehova monga amene amakhala pakati pa anthu ake. “Chiyero chiyenera nyumba yanu” (Masalmo 93:5). “Mwa iwo akuyandikiza ndipatulidwa Ine” (Levitiko 10:3).
Koma tsopano Mulungu wavumbulutsidwa mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, Mulungu kuvumbulutsidwa mthupi. Ngakhale Ambuye Yesu anali munthu weniweni, komabe utumiki wake padziko lapansi unaonekera ndi zimenezi, kuti anavumbulutsira Mulungu.
Koma pamene anavumbulutsira Mulungu kwathunthu pa mtanda, komanso mu nthawi yomweyo ndi kubweretsa chiombolo chamuyaya, Iye anauka pakati pa anthu akufa natenga malo ake kudzanja lamanja la Mulungu. Ndipo — Yohane 17:4,5 amatiuza kuti anachita zimenezi ngati Munthu.
Monga Mulungu anatenga ulemerero onse wamuyaya lisanakhale dziko lapansi. Koma tsopano, monga Iye amene anatsiriza ntchito pamtanda wa Gologota amene kwathunthu analemekeza Mulungu, anapempha kuti akalandirenso ulemerero umenewu monga Munthu. Ndipo tsopano ngati Munthu wokwezedwa akukhala kudzanja lamanja la Mulungu mu ulemerero — Munthu kumwamba.
Chinali chifuniro chamuyaya cha Mulungu kuti tikakhale monga mwa chifanizo cha Mwana Wake, kuti akakhale mwana woyamba wa abale ambiri (Aroma 8:29). Pano mu Yohane 17:17-19 Ambuye Yesu akuti amadziyeretsa yekha kwa Iye mwini. Amadzipatulira yekha kumwamba, kukhala kumeneko wake wa Mulungu kwathunthu nthawi zonse, ndipo amapanga zimenezi “kuti nawonso akayeretsedwe mwa choonadi.” Pamenepa tili ndi mlingo wa kuyeretsedwa kwathu, komanso nthawi yomweyo njira imene timayeretsedwera. Ndi mwa Kristu mu ulemerero.
KUYERETSEDWA KWA MZIMU
Tikamawerenga m’Chipangano Chatsopano timaona kuti kuyeretsedwa kwathu kukufotokozedwa m’njira ziwiri. Mbali ina imanena kuti tayeretsedwa (1 Akorinto 6:11; 2 Atesalonika 2:13; 1 Petro 1:2; ndi zina zotere.) Kotero timatchulidwa woyeretsedwa m’madera osiyanasiyana — mwachitsanzo, m’mawu oyambirira a makalata. Kuyeretsedwa kumeneku kwachitika kudzera m’kubadwanso. Kenako Mzimu Woyera anatipatula kudziko limene ife timapezeka pakutipatsa ife moyo watsopano, chikhalidwe cha kumwamba (Yohane 3; 2 Petro 1:4; Aefeso 4:24).
Mbali inanso akutiuza kuti tikuyenera kuyeretsedwa m’machitidwe athu (Ahebri 12:14; Aefeso 5:25-27; ndi zina zotere.) Mbali zonse ziwiri zikuikidwa pamodzi ku Chivumbulutso 22:11 “Ndi Iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.”
Tikupeza mfundo imeneyi ikugwiritsidwa ntchito m’ndime zosiyanasiyana m’Baibulo. Monga m’mene taonera ku Aroma 8:29, Mulungu anatipangiratu kukakhala m’chifanizo cha Mwana Wake. Ku Aefeso 1:4-5 tikupeza malingaliro omwewo koma akukambidwa m’mau ena. 1 Akorinto 15:49 imatiuza kuti “Ndipo monga tavala fanizo la wamthakayo (Adamu), tidzavalanso fanizo la wakumwambayo (Ambuye Yesu).”
Ndipo ku 1 Yohane 3:2 akutiuza nthawi imene izi zidzakwanitsidwa: “Tidziwa kuti, pakuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, pakuti tidzamuona Iye monga ali.” Mwanjira ina, m’ndime zina za m’Baibulo tinadziwika kale ndi Ambuye Yesu. Mu 1 Yohane 3:1 dziko lapansi silizindikira ife, popeza silidam’zindikire Iye. Ndipo pa 1 Yohane 4:17 akunena kuti tili kale padziko lapansi monganso Iye ali mu ulemerero tsopano.
Mafotokozedwe a zimenezi ndi akuti zonse zikutengera pa ntchito ya Ambuye Yesu. Kutengera malo athu ife tinapeza kale zinthu zonse tsopano (1 Akorinto 1:30). Kudzera m’kubadwa kwatsopano tinapatulidwa kudziko lapansi ndi kupeza moyo wosatha. Kudzera mu nsembe imodzi tinapangidwa kukhala angwiro, ndipo tikukhala olungamitsidwa pamaso pa Mulungu.
Ndife ana komanso cholowa cha Mulungu ndipo tili m’zakumwamba mwa Kristu Yesu (Aefeso 2:6). Molingana ndi miyoyo yathu, ife tinapeza zinthu zonse. Koma matupi athu sanapeze gawo mu zinthu zonse, ndipo chikhalidwe chathu chakale chidakalipobe. Ichi n’chifukwa chake machitidwe athu Sali ogwirizana ndi malo amene tinatengedwera potengera ntchito ya Ambuye Yesu.
KUYERETSEDWA MONGA MWA MAKHALIDWE ATHU
Kupempha kumadzala ndi zimenezi, ichi ndicho chindunji cha utumiki: kuti tsopano tikazindikire m’chikhalidwe chimene tsiku lina tidzakhala (Aefeso 4:11-16; Akolose 1:28). Kodi tidzakhala chiyani? Ngati Iye, Munthu Wolemekezedwa wa m’mwamba! Ndiye mlingo wa mayendedwe athunso a chikhalidwe. Kotero: “yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali woyera” (1 Yohane 3:3; onaninso 1 Atesalonika 3:12,13).
Kodi tingathe bwanji kukhala monga Iye m’makhalidwe athu? Pakuyetsetsa kutero? Pakuzitanganidwitsa ndi kuyetsetsa kwathu kusintha miyoyo yathu ndi kukhala miyoyo ya chiyero chochuluka? Ku Aroma 7 timapeza munthu wina akuchita zimenezi. Zotsatira zake iye anafuula nati: “Munthu wosauka ine: adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?”
Mau a Mulungu amationetsera njira yabwino. “Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalilole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera mu ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera ku ulemerero kumka ku ulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu” (2 Akorinto 3:18).
Pakuyang’ana Ambuye Yesu Kristu monga momwe alili pano, wokwezedwa kumwamba, pakuwerenga zonse zolembedwa m’Mau a Mulungu zokhudza Iye, ndi kuwalingalira Mauwo, miyoyo yathu imasinthika. Kotero timakhala osinthika chikhalidwe ndi kufanana Naye. Chinthu chimene mitima yathu ya kangalika nacho chimasiya chisonyezo kapena chizindikiro pa miyoyo yathu.
Zilinso chimodzimodzi ndi chiyeretso. Kunena chimene tidzakhala tsiku lina — kufanana ndi Ambuye Yesu wolemekezedwa — ndiwo mlingo wa chiyeretso chathu. Kutembenukira kwa Iye ndiko kumabweretsa chiyeretso chimenechi. Tsopano chiyero monga mwa chikhalidwe chake ndi machitidwe ake ndicho chimene chimaonekera mwa ife pamene Kristu wavumbulutsidwa mwa ife.
Ichi n’chifukwa chake Ambuye Yesu akunena: “Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m’choonadi” (Yohane 17:17-19). Tsopano akukhala ku mpando wachifumu wa Mulungu monga Munthu wolemekezedwa, “woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopirira miyamba” (Ahebri 7:26), kuti tikakhale oyeretsedwa pakuyang’ana kwa Iye. Choonadi, Mau a Mulungu, chimatifotokozera ife za Iye.
Zimaonetsera Iye mu ulemerero wa Umunthu Wake. Mitima yathu imadzala ndi ungwiro wake ndi zonse zimene zalumikizidwa ndi Iye. Kotero mkati mwathu mulibenso malo a za m’dziko lapansi. Miyoyo yathu imakhalabe ikufanana ndi chikhalidwe Chake, komanso kusiyanitsidwa ndi zonse zapansi pano kuti tikayeretsedwe mwa Mulungu yekha. Uku ndiko kuyeretsedwa.
Ndipo munjira imeneyi tingathe kudalira ndi chiyembekezo pa kukhulupirika kwa Mulungu. “Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m’kukondwera, kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayamba nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen” (Yuda 24,25. Onaninso Mateyu 19:26).
Ndi malonje onse abwino
Ndine mzako
H.L.H.
MUTU 12
PHINDU LA KUWERENGA MAU A MULUNGU
Okondedwa Anfffzanga,
Nditakufunsani ngati mumawerenga Baibulo pafupipafupi. Sindikutanthauza kuwerenga Baibulo pamodzi ndi banja lonse pa nthawi ya chakudya, komanso ngati mumatero, koma ndikutanthauza kuwerenga Baibulo panokha. Ndi zofunikira kwambiri kuti muzitero. Pamene wokhulupirira sakuwerenga Baibulo sakhalabe mu chiyanjano ndi Ambuye ndipo sakhala ndi chisangalalo chenicheni.
Sitingathe kukokomeza phindu la Baibulo, pakuti ndilo Mau a Mulungu. Pakuti ndi pakuwerenga Mau pamene timamdziwa Mulungu ndi malingaliro ake. M’Chipangano Chakale Mulungu anadzivumbulutsira yekha kupyolera m’Mau amene anayankhula ndi kuperekedwa kuti alembedwe. M’menemo anatiuza ife chimene Iye anali, chimene anachita, chimene amayenera kuchita, komanso m’mene munthu akanamutumikirira.
Kenako Mwana anabwera padziko lapansi kudzafotokozera za Mulungu (Yohane 1:18). Komanso tikudziwa zonse zokhudza Mwana — Kubadwa Kwake, moyo ndi kufa Kwake, Mau Ake ndi zintchito Zake — kudzera m’Mau okha. Komanso Mulungu Mzimu Woyera, amene tsopano ali padziko lapansi ndi kukhala mwa onse akukhulupirira, kuvumbulutsira zinthu zonse kwa ife kudzera m’Mau.
Kotero ndi kusowa umunthu ngati wokhulupirira sakonda Baibulo. Kukula kwake m’chisomo ndi m’chidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu kumalumikizidwa kwambiri ndi chikondi chake pa Mau ndi kugwiritsa kwake kwa Mau.
KUBADWANSO
Tikawerenga, mwachitsanzo, Masalmo 119, timaona kuti gawo lililonse la moyo wa uzimu wa Mlembi wa Masalmo likulumikizidwa ndi Mau. Choyambirira tikuona kuti moyo watsopano ukhalapo ndi mau (ndime 93): “Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse; popeza munandipsatsa nawo moyo.” Onaninso ndime 25, 37, 40, 50, 88, 107, 116, 144, 149, 154, 156, 159 ndi 175. Izinso zalembedwa bwino lomwe m’ndime zina. “Mwachifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi” (Yakobo 1:18).
“Inu amene munabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa” (1 Petro 1:23). Ambuye Yesu akunenanso izi ku Yohane 3:5 “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.” Kuchokera ku Aefeso 5:26 komanso ndime zina pali umboni kuti madzi ndi chithunzithunzi cha Mau kuikidwa pa munthu ndi Mzimu Woyera.
Mau a Mulungu amabweretsa chikumbumtima cha munthu wochimwa m’kuunika kwa Mulungu. Kupyolera m’menemu munthu amadziona yekha chimene ali nadzitsutsa yekha, kuvomereza machimo ake pamaso pa Mulungu. Uku ndiko kutembenuka. Koma kudzera m’kudziweruza yekhaku, mtima wa munthu wayeretsedwa ndipo Mzimu Woyera kudzera m’Mau amapanga mwa munthuyo moyo watsopano ndi wa umulungu.
Zimatsatira kuti pamene tiyankhula ndi osakhulupirira kuwabweretsera uthenga wabwino, tikuyenera kudziwa Mau a Mulungu. Mau athu okha sangam’bweretse munthu ku kutembenuka. Mau a Mulungu okha amachita zimenezi. “Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu” (Aroma 10:17).
Komanso Mau a Mulungu ndi:
CHAKUDYA CHA MOYO WATSOPANO
“Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m’kamwa mwanga” (Masalmo 119:103). “Zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake” (Masalmo 19:10). Ambuye Yesu akunena kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu” (Mateyu 4:4). Onaninso Ahebri 5:12-14 ndi 1 Petro 1:25-2:2.
Moyo watsopano umene umabwera kudzera m’Mau umafunika chakudya chogwirizana ndi moyowu. Chakudya chimenechi ndi Ambuye Yesu monga Mpulumutsi amene anafa (Yohane 6:56), monga Iye amene anayenda padziko lapansi monga woyera, munthu woona (Yohane 6:33-35), komanso ngati Ambuye wokwezedwa kumwamba, tiligu wakale wam’dziko (Yoswa 5:11).
Koma timamupeza Iye m’Mau mokha. M’Chipangano Chakale timamuona m’njira zonse ndi m’zithunzithunzi ndi m’mauneneri a aneneri. M’Chipangano Chatsopano timamuona akudzionetsera bwino lomwe m’moyo wake padziko lapansi ndi mu imfa yake m’mauthenga abwino, Machitidwe Atumwi, m’makalata atumwi; komanso monga Ambuye wakwezedwa ku Machitidwe Atumwi, m’makalata atumwi, komanso ku Chivumbulutso.
Kodi ndizodabwitsa kuti miyoyo ya uzimu ya anthu ambiri ndi yofooka ndi kudwala, ndipo kuti imangomwa mkaka, osati chakudya cholimba (Ahebri 5:12-14), pamene sabwera ku misonkhano ya utumiki kapena m’kusanthula Baibulo, ngakhalenso pamene safufuza Mau kawirikawiri pa iwo okha?
Njira yokhayo imene tingathe kukulira ndi kukhala ndi moyo wa uzimu wa thanzi ndi pamene tidya chakudya choyenera pafupipafupi.
MAU A MULUNGU NDIWO MLOZO WATHU
“M’nyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu…Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu…Mau anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga” (Masalmo119:9,11,105).
Ambuye anamuuza Yoswa: “Komatu khala wamphamvu nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipambukire kudzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru” (Yoswa 1:7,8).
Pakuona zoopsa zazikulu zakudza mtsogolo, Paulo ku Machitidwe 20:32 akupereka akuluakulu a ku Aefeso “kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake.” Kwa Timoteo analemba za “malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso” (2 Timoteo 3:15).
Kodi tingadziwe bwanji kuti tchimo ndi chiyani ngati sitidziwa Mau a Mulungu? umbuli sungatipangitse kukhala anthu osalakwa (Levitiko 5:17). Kodi tingadziwe bwanji zofunika kuchita komanso kuti malingaliro a Mulungu ndi chiyani, ngati sitisanthula m’Mau omwe Iye amatiuzamo zinthu zonse? Kodi tingadziwe bwanji momwe tingachitire chisankho cha zinthu zina komanso njira yofunika kutenga ngati sitidziwa Mau a Mulungu?
“Potsegula mau anu paunikira; Kuzindikiritsa opusa...Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire. Ndiri nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu. Ndizikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu” (Masalmo 119:130,98-100).
MAU A MULUNGU NDI CHIDA CHATHU
“Lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu” (Aefeso 6:17), “Kuti ndikhale nawo mau akuyankha wonditinthoza; popeza ndikhulupirira mau anu” (Masalmo 119:42). M’mene Ambuye Yesu anagwiritsira ntchito lupanga limeneli! Mfundo iliyonse yomuyesa yochokera kwa Satana imakumana ndi mau akuti “kwalembedwa” (Mateyu 4:4,7,10). Ndipo zotsatira zake zinali zakuti Satana anathawa. Iye analibe mphamvu pa Mau a Mulungu.
Koma Ambuye anagwiritsanso Mau motsutsana ndi anthu: “Kodi sikunalembedwa” (Yohane 10:34)? “Nchiyani ichi chinalembedwa” (Luka 20:17)?
“Pakuti mau a Mulungu ali a moyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima. Ndipo palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye” (Aheberi 4:12,13).
Chimenechi ndi chida chokhacho chimene tingagwiritse ntchito pa kudzitetezera kwa Satana ndi dziko lapansi komanso pomenyera nkhondo. Sitikuyenera kuiwalira kuti amenewa ndi Mau a Mulungu wamoyo, ndi kutinso ali ndi mphamvu paokha. Pamene tagwiritsa ntchito chidachi onse amene tidzalimbana nawo adzaimva mphamvu imeneyi.
Ngakhale kwa munthu amene tidzayankhula naye ngati alibe mphamvuyi, ndipo iye nakhala osasunthika kapena wa upandu, komabe chikumbumtima chake chidzamutsutsa kuti zimene mwamuuzazo ndi zoona.
Pamene ine ndinali wamng’ono, ndinayesako chinthu chimenechi. Ndimagawa timatirakiti towerenga m’sitima, ndipo munthu wina anayamba kundinyoza pa nkhani yokhudza chiKristu. Ndinatenga Baibulo ndipo ndinawerenga mofuula ndime imene imayankha za mtsutso wakewo. Pamene ndinachita izi kawiri kapena katatu, anayankhula: “Akulu, ine sindikutsutsana ndi Baibulo koma ndikutsutsana ndi inu.”
Ine ndinamuyankha kuti Baibulo ndilo tsinde la ulamuliro wanga. Anayesanso kawiri kapena katatu, ndipo mopsa mtima anandicheukira nayamba kuwerenga ka tirakiti kaja. Palibe munthu amene angatsutsane ndi Mau a Mulungu.
Nthawi yonga yomweyi panachitikanso chinthu china chofanana ndi chomwechi. Koma nthawi imeneyi sindinatenge Baibulo langa, koma ndinayamba kutsutsana ndi munthu wina. Sizinatenge nthawi kuti ndizindikire kuti ndayamba kugonjetsedwa!
Zaka zingapo zapitazo ndinayima podikirira sitima pamene panali anthu ambiri. M’modzi mwa anthu aja amadandaulira mzake za nyengo zokhoma zimene timadutsamo ndipo amatsimikizira kuti masiku abwino sadzabweranso.
Ndinalowerera nkhaniyo ndipo ndinamutsimikizira kuti ndikudziwa bwino lomwe kuti pangatalike maka koma nyengo zabwino zidzafika tsiku lina, ndipo kuti ine ndidzaziona nyengozo. Kenako ndinamuwerengera ndime kuchokera m’Mau a Mulungu.
Anandiseka kwambiri nandinyogodola, pamenepo ndinamuwerengeranso ndime zina zokhudza nyengo za munthu ndi dziko lapansi, komanso za chipulumutso chopezeka mwa Yesu Kristu. Anatembenukira kumbali nayamba kucheza ndi munthu wina.
Kenako, patantha mphindi khumi ndi zisanu anandipempha kuti ndipite naye kwawo. Ndipo misozi ikulengeza m’maso anandipempha Baibulo — pakuti iye anafunitsitsa kukhala nacho chinthu chimene ndimamuwerengeracho.
NJIRA YA KUDZIYERETSA
Mau a Mulungu ndi njira yokhayo imene tingayeretsedwere nayo. “Monganso Kristu anaconda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake; kuti akampatule atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau” (Aefeso 5:25,26). “Patulani iwo m’choonadi; mau anu ndi choonadi” (Yohane 17:17).
Miyoyo yathu imayeretsedwa pokhapokha tikagwiritsa ntchito Mau a Mulungu pa kuyenda ndi kukhala kwathu, pokhapo ndi pamene timalekanitsidwa ku zoipa. Wotiimira kwa Atate amatsuka mapazi athu ndi Mau (1 Yohane 2:2; Yohane 13); koma ndi udindo wathu kuvomereza kuti mapazi athu atsukidwe.
“Ndinawabisa mau anu mu mtima mwanga, kuti ndisalakwire inu” (Masalmo 119:11). “Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo: M’kuzisunga izo muli mphoto yaikulu. Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika?” (Masalmo 19:11,12).
Kuonjezera pamenepa, Maunso ndi:
MUYESO WA KACHITIDWE NDIPONSO KAPHUNZITSIDWE KATHU
“Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu” (Masalmo 119:168). “Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo” (Chivumbulutso 2 ndi 3). Tikuyenera kuyesa chilichonse chochitika mu mpingo, kupyolera mu zophunzitsidwa ndi zochitika, pa zimene Mzimu anena ku mpingo, kupyolera m’Mau. “Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire” (1 Akorinto 14:29).
Tikuyeneranso kuyesa mayendedwe athu komanso malingaliro athu ndi Mau a Mulungu. Malingaliro athu ali opanda phindu. Koma chokhacho chimene Mau a Mulungu anena chili nawo ulamuliro. Onani, mwachitsanzo, (Levitiko 5:14-19).
Ku Machitidwe 17:11 Ayuda aku Bereya anali a nzeru kuposa a ku Atesalonika chifukwa amayesa mau a mtumwi Paulo ndi Mau a Mulungu. Ku 1 Akorinto 15:3,4 mtumwi mwini akunena kuti Malembo ndiwo gwero la chiphunzitso chake.
“Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino” (2 Timoteo 3:16,17).
KUMVERA NDI KUDZIPEREKA
“Inu munatilandira tisamalire malangizo ndi changu” (Masalmo 119:4). “Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake” (Yohane 15:10). “Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa mwa iye mokhalamo” (Yohane 14:23). “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa” (1 Yohane 5:3).
Pamenepa tikuona m’mene Mulungu amatengera kukhala za mtengo wapatali kukhala ndi chidziwitso komanso kumvera Mau a Mulungu. Sizingatheke kuchoka pa mfundo imeneyi popanda kufunsa kuti: “Ambuye, kodi chifuniro chanu ndi chiyani choti ine ndichite?”
Tchimo loyamba linali kusamvera Mau a Mulungu. Indedi, tchimo ndiko kuchita zinthu kapenanso kulephera kuchita zinthu popanda kuganizira pa mfundo yakuti Mulungu ali ndi ulamuliro pa ife. Ndiko kusayeruzika (1 Yohane 3:4). Zonse zimene timachita popanda kufunsira upangiri monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi tchimo.
Mwa Ambuye Yesu Kristu timaona moyo wakumvera! Iye anabwera padziko lapansi kudzachita chifuniro cha Mlungu (Ahebri 10:7). Pa chifukwa chimenechi anayenera kuphunzira kumvera (Ahebri 5:8), pakuti kumvera chinali chinthu chachilendo kwa Iye, Mulungu wamuyaya. Koma padziko lino lapansi angathe kunena: “Ndimachita chifuniro cha Iye”. “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake” (Yohane 4:34).
Kodi chikanachitika ndi chiyani kwa Mulungu kuona padziko lapansi, kumene anthu akuchita chifuniro chawo chawo, Munthu ameneyu amene anachita chifuniro cha Mulungu chokhachokha, ngakhale chifuniro chake chimene chinali changwiro ndi choyera!
Mulungu angathe kumva bwanji kuti ngakhale tsopano atapeza anthu amene chikhumbokhumbo chawo ndi chimwemwe chawo ndicho kum’tumikira Iye, amenenso mwa chidwi afufuza Mau ake ndi cholinga chakumdziwitsitsa Iye ndi chifuniro Chake!
Ndiponsotu pali phindu lalikulu kwa ife pamene tiwerenga Mau ndi kuphunzira kuwadziwa mauwo. Mitima yathu imakhala yosangalala pamene tiwona ulemerero wa Ambuye m’menemo, pamodzi ndi zonse zimene chikondi cha Mulungu chatikonzera. Timawadziwa kwambiri ndi kuphunziranso kumvetsetsa malingaliro a Mulungu pamwamba pa zonse.
Nthawi yomweyo timalandiranso nkhokwe yodzala ndi zimene tingagwiritsire pa kudziteteza tokha ku nkhondo yochokera kwa Satana komanso pa kukamuputa iye — pamene tigwiritsira ntchito pobweretsa miyoyo ku chipulumutso.
Kodi wina angathe kudandaula kuti malingaliro ake ali ngati sefa, imene sisunga kanthu — bwino lomwe, ngakhalenso kuti sefa singasunge madzi, komabe imakhala yoyera ndi madzi amene akudutsa mu sefayo. Chimodzimodzinso ndi Mau a Mulungu. Koma musangowerenga Mau a Mulungu kokha — alingalireninso.
Mokondweretsedwa gwiritsani zina mwa mfundo zimene mungathe kuzisunga. Koma yesani zonse ndi Mau a Mulungu. Musalole ndemanga zochokera ku mabuku ena zitenge malo a Mau a Mulungu. Chimenechi chingathe kukhala chizolowezi choipa ndithu.
“Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga; kucherera makutu ako ku nzeru, kulodzetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu” (Miyambo 2:1-5)
H.L.H