CHILENGEWE CHA KALE NDI KUBADWA MWATSOPANO KAPENA, WOKHULUPIRIRA NDI MAVUTO AKE
George Cutting
Iwo amene ali mzambiri kuchita ndi zovuta za wotembenuka mtima watsopano, amamva izi, “Ndimaganiza kuti ndinapulumutsidwa koma pano ndikuwopa kuti ndikuzinamiza ndekha. Sindikumva bwino kokha koma mwinamwake moyipa kusiyana ndikale ndisanatembenuke mtima.”
Tsopano, zikatere wina apeza, kuti sikuti machimo awo ndi amene akuwavutitsa kwambiri monga mtima upweteka mkukhumudwa monga mopitilaza choonadi chikukakamizidwa pa iwo kuti kubadwa kwawo kwatsopano sikunasinthe chilengedwe chawo choipa koma kuti chilengedwe choipa chikuwoneka choipa kwambiri ksiyana ndi kale asanatembenuke. Ambiri amyesetsa kusintha koma amalephera ndipo amathera mumkukhumudwa kozama. Ngati moyo uli mnyengo iyi, Satana amapeza kuthekera koponya mivi yake yowopsa. Iye amati onse ali onamizira omvetsa chisoni, amangonamizira kukhala chomwe akudziwa kuti Sali icho; pomwe zingale bwino atangozisiya, kubwera poyera ndi kuonetsa moyo wawo wosatembenuka mtima.
Oh, ndi zowawitsa mtima bwanji pomwe kuchita chonsecho ufulu woona sakuchidziwa. Okhawo amene adutsa m’zochitika zotere ndi amene angazikire kuwawa kwawo kosananedwa. Ndi chikhumbokhumbo kulimbikitsa ndi kuthandiza ngati izi kudzera mu kabuki aka.
Mfundo za Mulungu ndi zomwe takumana nazo
Okhulupirira ambiri amadutsa m’masautso chifukwa amafunafuna m’mitima yawo umboni woti atsimikize kuti atembenukiradi kwa Mulungu. “Ndikamayerekeza moyo Wanga wa tsiku ndi tsiku ndi choonadi m`Mau a Mulungu“, Munthu uyu adzanena,”ndimayamba kuwopa kuti sindinatembenuke mtima. Mwa chitsanzo, ndimaona m’buku la 1 Yohane mfundo zitatu ya choonadi chokhudza amene “wina amene wobadwa mwa Mulungu ndipo sindingathe kuyankha ngakhale imodzi mwa izo, ndichita zomwe ndingathe.
Mfundo yoyamba: “Iye sachita tchimo ndipo sakhoza kuchimwa (1 Yohane 3:9)
Mfundo yachiwiri: “Iye anagonjetsa dziko lapansi.” (1 Yohane 5:4)
Mfundo yachitatu: “Woyipayo samkhudza.” (1 Yohane 5:18)
Tsopano molingana ndi mau awa, ndikuyenera kuvomereza kuti:
Choyamba: Ine ndikhoza ndipo ndimachita tchimo.
Chachiwiri: M’malo mogonjetsa dziko, dziko limagonjetsa ineyo.
Chachitatu: Kuti Mdani wakhala akundigonjetsa ine nthawi zambiri popanda chiwerengero ndi chimene amachita kukhudza ine.
´´Kodi pali kudabwa kwina pamenepo m´mene ndifanizira malemba oterewa pamaso pa zomwe ndikukumana nazo ngati zanga? ´´
Chabwino, kuyera kumereza kuti kulibe; koma tiyeni tinene pa chinthozo chako kuti iwo amene “ali akufa mu machimo awo” samakumana ndi kulimbana kotere. Ndi okhawo otembenuka omwe amakhala ndi chilakolako chofuna kuyankha ku malingaliro ndi khumbo la Mulungu. Onse osatembenuka safuna kudziwa njira za Mulungu (Yobu 21:14). “Kumuopa Mulungu palibe pamaso pawo” (Aroma 3:18).
Koma tiyeni tibwerere.
Taona chinthu chimodzi chosatheka chakuti, “Aliyense wobadwa mwa Mulungu sangachimwe.” Tiyeni tiwonenso mawu ena (Aroma 8:7-8), “Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero. Ndipo iwo amene ali mthupi sangathe kukondweretsa Mulungu.” Dziwani bwino izi zofunikira zosiyana:
- Iye amene ali “mthupi” – monga “anabadwa mthupi” – sangakondweretse Mulungu.
- Iye amene ali “wobadwa mwa Mulungu sachita tchimo” (1 Yohane 3:9).
Ndi chofunikira kudziwa tanthauzo la mau akuti “mthupi” kwa ife. Ichi ndi choipa kapena kugwa kwa chilengedwe mwa mwana aliyense wa Adamu, munayikidwa chiphe mwa tchimo lokhalamo. Ichi ndi chiyambi chenicheni cha machitidwe aliwonse a uchimo ochitidwa ndi iye.
MAKHALIDWE AWIRI WOSIYANA MWA MUNTHU MMODZI
Tawona kuti tikamabadwa timakhala ndi chikhalidwe choipa, choncho choipa chomwe Mulungu amanena sichingagwirizane ndi chiyero chake. Sichingathe kukondweretsa Mulungu. “Onani”, olemba Salimo akuti, “Ndinabadwa mphulupulu ndipo mayi anga anandilandira m’zoipa” (Masalimo 51:5). Ndipo ife amene tinabadwanso mwa mzimu kapena tinabadwanso kachiwiri, kudzera mwa mzimu mu njira ya Mawu a Mulungu (Yakobo 1:18, 1 Petro 1:23), chikhalidwe china chapadera-dera, chikhalidwe chauzimu (2 Petro 1:4). Ambuye anayankhula ndi Nikodemo kuti, “Chobadwa mthupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala Mzimu (Yohane 3:6).
Chotere wokhulupilira amakhala ndi makhalidwe awiri, “chobadwa m’thupi” chomwe “sichingakondweretse Mulungu” komanso “chobadwa mwa Mzimu” chomwe mwa chibadwidwe chake “sichingachimwe chifukwa ndi chobadwa mwa Mulungu”. Pa Aroma 7 tidzapeza makhalidwe awiri osiyana omwe akutchulidwa mwachindunji. Onani mwachitsanzo, vesi yomaliza. “Pakuti monga mwa Munthu wa m’kati mwanga (mukati mosinthika kapena chikhalidwe chasopano), ine nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi (chikhalidwe chakale) chilamulo cha uchimo”. Komanso muma vesi 22 ndi 23: “Ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziwalo zanga, kulimbana ndi lamulo la mtima wanga.”
Palinso chitsanzo chomwe chingakhale chothandiza:
Mkazi wa mlimi akanakhazika nkhuku pa mazira a bakha. Patatha sabata, mazira aja anaonongedwa ndi mmodzi mwa adani ake. Tsiku loti mazira asweke, nkhuku inazindikira kuti panali mitundu iwiri ya ana. Izi sizinadabwitse kwambiri nkhukuyi koma tsiku lina nkhukuyi inadabwa kuwona ana a bakha akupita padziwe lomwe linali pafupi kukasambira ndipo anawa anali wosangalala. Nkhuku inayetsetsa kuwaitana ana aja koma sanamvere. Koma ana a nkhuku sanawonetse chidwi chilichonse kuti alowe m’madzi muja. Iwo akanakakamizidwa kuti alowe akanamvetsa chisoni.
Apa tikuwona makhalidwe awiri osiyana kwathunthu musochitika zawo ndi zofuna zawo. Khalidwe loyamba lochokera mu dzira linali ndi makhalidwe a bakha ndipo lina lachiwiri lochokera mu dzira la nkhuku linali ndi makhalidwe ankhuku. Komatu mazira onsewa anali mu chitsa chimodzi.
Tsopano, akazi onse a alimi m’dziko lonse pamodzi ndi abambo onse analephera kusintha chikhalidwe cha bakha kuti chikhale cha nkhuku. Bakha anapitiriza kukhala m’chikhalidwe cha bakha komanso nkhuku zinakhala m’chikhalidwe cha nkhuku.
Nthawi zambiri pamakhala zikhalidwe ziwiri mwa m’khristu, izi zimakhala chonchi chifukwa cha komwe akutenga chikhalidwecho. Chikhalidwe china chimachokera kwa munthu yemwe ndi wotayika, wochimwa, wakugwa, pamene chikhalidwe china chimachokera kwa Mulungu ndi chiyero cha kusachimwa kwake. Wina ndi wotayika pamene wina ndi woyera ndipo sangadetsedwe. Choipa chilichonse chimachokera kuchikhalidwe chakale pamene zabwino zimachokera kuchikhalidwe chatsopano.
Mwachitsanzo, kumbukirani tsiku lomwe munali ndi chikhumbokhumbo chofuna kupemphera panokha mu chipinda chanu. Chikhumbokhumbochi chinachokera ku chikhalidwe chanu chatsopano koma mwina maganizo oipa anakubwelerani mukupemphera mutagwada, ichi chinali chochokera ku chikhalidwe chakale, komano pali funso lina lofunikira.
Kodi chikhalidwe chakale chikhoza kusinthika mwaubwino ndi chikhalidwe chatsopano?
Pali yankho limodzi lokha, palibe chomwe chingasinthe mwaubwino thupi. Izi zinayesedwa mu njira iri yonse kuyamba nthawi yakugwa ya Adamu mu munda wa Edeni mpaka pa mtanda wa Yesu pa kavali. Kodi chotsatira chake chinali chani? Chifukwa chiani zinali izi zokha:
Lamulo la Mulungu linaphwanyidwa mwadala mmene Mulungu amafuna kumvera kuchokera kwa munthu. Mwana wake anaphedwa momvetsa chisoni mmene anabwera pa dziko lapansi mwachisomo kwa munthu. Zoonadi mmalo moti kupezeka kwa moyo wachiyero usinthe mwaubwino chikhalidwe chakale chimango onesera kuipa kwake kweni kweni. Chikhalidwe choipa ndi chomwe chimaonekera, zili ngati kumpatsa munthu wosauka chovala chabwino kuti chovala chake chong’ambikang’ambika chisaonekere, koma sizikhala choncho.
Koma ngati chikhalidwe changa chakale sichingakhululukidwe kapena kusinthidwa mwaubwino, izi zikhoza kupangitsa kuti mavuto awiri atumphuke paoka.
- Kodi ndingapulumuke bwanji kuchoka kwa iwo?
- Kodi ndingapeze bwanji mphamvu zogonjetsera?
Poganizira mavutowa, ndikofunika kudziwa mmene mawu a Mulungu akufotokozera za ’tchimo’ m’thupi ndi ‘machimo.’
Nthawi zambiri lamulo la choipa ndi lakuti, tchimo lili mwa ife, komanso zochitika zoipa, mawu ndi maganizo zimene ziri zotsatira zakukhala ndi chikhalidwe choipa zimatchedwa machismo. Tiona kusiyana kwa izi mu 1 Yohane 1:8,9: “Ngati tinena kuti tilibe uchimo tizinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi” komanso “Ngati tivomeleza machimo athu ali wokhulupirika ndi wolungama iye kuti atikhululukire machimo athu”, kusiyana kwa mavesiwa awa ndi kofunika kwambiri pamene tipeza mu mmawu akuti kupyolera m’kukhetsa mwazi wa Yesu Khristu Mulungu amatikhululukira zolakwa zathu zomwe zili mmachimo; Iye sakhululukira tchimo m’thupi koma iye amatiweruza ndi kutsutsana ndi tchimolo.
Tiyerekeze kuti muli ndi mwana yemwe amakonda kukhala waukali, tsiku lina anaganiza zomponyera m’chimwene wake buku ndipo anaphwanya zenera, poti iye wazindikira kulakwa kwake mukhonza kumukhululukira. Nanga m’kwiyo womwe wampangitsa kuti apange chonchi? Kodi mungamukhululukire? Ayi ndi zosatheka! Ndipo mukhoza kuwonetsetsa kuti simunagwirizane nazo ndiponso kuthetserathu muchitidwe umenewu.
Choncho m’kwiyo kapena kupsa mtima kukhonza kuyankha zambiri zokhudza tchimo: monga kuzochitika zake ngati kumukwiyitsa mchimwene ndi kuswa zenera zikhonza kuyankha zambiri zokhudza machimo, choncho ndikubweleza kuti ngakhale Mulungu anamukhululukira munthu machimo ake, Iye sakhululuka tchimo lokhazikika. Chomwe Iye akhonza kuchita ndi kulanga tchimo – Imfa ndi njira yokhayo (Aroma 8:3). “Mulungu anatumiza mwana wake wa Iye yekha m’chifaniziro cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m’thupi.”
Koma mu machaputala oyambilira a Aroma, mtumwi akutionetsera mmene tingapulumukire kuchokera ku machimo; koma pa Aroma 6 akutiwonetsa mmene tingapulumukire ku tchimo, monga muma vesi a m’chaputala 4 akukamba za Khristu yemwe “anatipulumutsa ku machimo athu ndipo anaukanso kuti tilungamitsidwe”.
Ndipo ubwino wopulumutsidwa ndi woti “Onse okhulupilira mwa Iye ndi wokhululukidwa ndipo ndiwolungamitsidwa, iwo ali ndi mtendere wa Mulungu, komanso pa Aroma 6 akukamba za kupulumutsidwa ku tchimo ngati chinthu china, “pakuti iye amene anafa anamasulidwa ku uchimo” (vesi 7).
Tsopano titha kuona kusiyana pakati pa zinthu ziwiri izi, posiyanitsa kuyeretsedwa kwa wa khate mu Levitiko 14:1-7 ndi kuyeretsedwa kwa Namani mu 2 Mafumu 5:10-14. Mu bukhu loyambilira tikuwona kuti wakhateyu akulephera kudziyeretsa yekha, iye wangoima ndipo akuwona akudikira kuti amuchitire zonse. Mbalame yamoyo komanso yoyeletsedwa ya viikidwa mu mwazi wa mbalame yophedwa, kenako ayitaira mu munda ndiye kuti munthu wa khate ndi wa moyo komanso woyeletsedwa wina akamufera iye yemwe anali wosayeletsedwa, magazi apakidwa pa iye apangitsa kuti wa nsembe wa Mulungu anene kuti wa khate wayeletsedwa.
Apa tikuona kuti “Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi chifukwa cha machimo, wolungama mmalo mwa osalungama kuti akatifikitse kwa Mulungu” (1 Petro 3:18). Palibe mulandu wina uliwonse kwa onse okhulupilira iye, “Mwazi wa Yesu mwana wache utisambitsa kutichotsera uchimo wonse” (1 Yohane 1:7); ndipo “Mwa iye yense wokhulupilira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse” (Machitidwe 13:39). Koma mu nkhani ya Namani sikuti ndikumufera koma iye mwini apite ku mtsinjewu wa Yolodani (kuwona mtsinjewu ngati chinthunzinthunzi cha imfa). Tisataye nthawi ndi chochitika chosangalatsa ichi koma tidziwe kuti khate lonse analisiya m’madzi muja (mtsinje wa Yolodani).
Komanso mau a Mulungu amatiphunzitsa kuti Khristu sanafere wokhulupilira yekha koma kuti monga Namani nayenso anafa, “Pakuti munafa” (Akolose 3:3). Koma pali kusiyana kumodzi kwa chipulumutso chathu ndicha Namani. Iye anapulumutsidwa ku khate lomwe anali nalo, pamene ife sitidzapulumutsidwa tili pansi pompano ku tchimo lomwe lilipo. Ndi mmene tilili, komanso ndi zonse zimene tichita zinatha pa mtanda, ndipo amene anatenga zoipa zathu anati “Kwatha”. Kodi ndani adzatitcha ife ochimwa? Kodi pali china chotsalira kutinena ife kuti ndi wochimwa? Ayi. Kodi Satana amatibweretsera machismo athu pamaso pathu? Sitikuyenera kukana kapena kudziyesa ngati tilibe machismo koma mwachikhulupiliro tikuyenera kuyankha “Yesu anawafera”. Kodi ndi chifukwa cha uchimo wathu kuti akhoza kutiyalutsa ife? Chikhulupiliro chitha kwonjezera kuti “Nanenso ndinafa”.
Komano masikuano pakubwera vuto ili kwa anthu ambiri, wolemba anamvapo munthu wokhulupilira akupemphera motere; “kuti iye adzichimva kuti naye anafa Pamodzi ndi Khristu” Kodi Mulungu amakambapo zoti ife tizimva choti tinafa? Ayi. Iye amati: “monga mudzitenge nokha kuti mwafa ku uchimo, koma mwauka mwa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu” (Aroma 6:11). Tiyenera kukhulupilira kuti kudzera mwa imfa ya Khristu nafenso tinafa chifukwa Mulungu akutero osati chifukwa choti ndi mmene tikumvera.
Mulungu mwiniwake amati choonadi kwa ife ndi choti “pakuti munafa”, ndipo iye akuyembekezera ife kuti tikhulupilire monga timakhulupilira kuti Khristu anatifera ife, machimo athu. Mulungu amadziwa yemwe anapilira mmalo mwathu ndikutifera ife, ndipo chikhulupiliro chimenechi chingagwirizane ndi chake. Ife achikhalidwe chakale, monga ana a Adamu yemwe anachimwa zonse zinathera pa mtanda, ndipo mawu amati “Podziwa ichi kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi iye” (Aroma 6:6) ndipo tsopano talumikizidwa ndi moyo kwa Adamu womalizira, uyu ndi Khristu yemwe anaukanso monga akunenera pa Aroma 7:4: “Kuti mukakhale ake a iye ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa.” Ife ngati wokhulupilira tabweresedwa mmalo atsopano. Iye amene anazunzika m`malo mwathu pokhala tchimo pa mtanda, tsopano anauka kwa akufa; poti Mulungu amationa ife mwa Iye, ife ndi athu oyeletsedwa.
Kodi kupezeka kwa tchimo lokhazikika kusokoneze chiyanjano chathu ndi Mulungu?
“Zingakhale bwanji”, wina akhonza kufunsa, “kuti kodi nchifukwa chiyani kupezeka kwa choipa mu thupi la wokhulupilira sikungalepheletse chiyanjano ndi Mulungu?” Mundilole kupereka chitsanzo china motere:
Bambo ndi mwana wake anali kunyumba kwawo ndipo anali pa chiyanjano mosangalala. Kodi chiyanjano ndi chiyani? Chiyanjano ndi kuti iwo azicheza limodzi ndikumagwirizana maganizo awo pa chili chonse chimene angakumane nacho. Mwadzidzidzi mwana wina wafika kuchokera ku tchire ndipo wayika zipatso zomwe wabwera nazo pa gome. Bambo wake anena kuti zipatsozo zimapha ndipo ndizosayenera kuti zidyedwe ndipo akulakalaka atazitaya nthawi yomweyo ndipo mwana uja akagwirizana ndi zomwe bambo wake akunena ndiye kuti sizingavute kuti mwana uja avomereze ndipo onse akhoza kukhala pa chiyanjano. Apa tikuona kuti kupezeka kwa zipatso zoipa sikungapangitse kusagwirizana pakati pawo. Koma ngati mwana uja savomereza zomwe abambo ake akunena ndipo atengeka ndi maonekedwe okoma a zipatso zija, iye sakhala pa chiyanjano ndi atate ake ndipo akayesera kudya iwo akuona, zikhoza kubweretsa mavuto. Ndipo iye akadzichepetsa ndikulapa pa zomwe wachita ndikugwirizana ndi zomwe atate wake ananena kuti zipatso ndi zoipa, iye ayanjananso ndi atate ake.
Pamene wokhulupilira waphunzira choonadi chochokera kwa Mulungu, chakuti tchimo limakhalabe “mwa iye” ndi kuti umunthu wa kale umakhala chimodzimodzi kapena kupitilira apo, iye akuyenera kudana ndi tchimo ndikukhala mbali ya Mulungu m`malo muti aziyesetsa kuti zikhale bwino, akulephera. Iye asalitengere konse koma, alione ngati mdani ndipo asalumikizane nalo. Iye amadziwa kuti Mulungu analigonjetsa pa mtanda ndipo iyenso akuyenera kulitaya. Iye “afe ku tchimo koma auke mwa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu”.
Ndi chilimbikitso kuti Mulungu sakuyembekeza zabwino kuchoka ku thupi. Iye amadziwirathu kuthi thupi ndi chithu chopanda pake ndipo akufunanso kuti nafe tichite chimodzimodzi. Ndipo thupi lilibe gawo pa ife. Ife tiri amangawa si ache a thupi ayi, kukhala ndi moyo monga mwa thupi (Aroma 8:12). Ngakhale tili ndi udindo wowonetsetsa kuti sitili mthupi ndipo thupi lilibe ulamuliro uliwonse pa ife koma Mulungu amatipatsa kuthekera kuti tisakhalenso mthupi kudzera mu imfa ndi kuukanso kwa Khrisitu kuti tisaliwone kuti lili ndi gawo mu moyo wathu watsopano Muzimu pa maso pake.
Mtanda wa Yesu Khristu wachotsa chiyanjano chomwe chinalipo pamodzi ndi Adamu woyamba wochimwa ndipo Mzimu woyera watibweretsera mmoyo mwathu Adamu womalizira woukanso. Ife sitili m’thupi monga mmene Mulungu amatidziwira koma tili m’Mzimu. Ndipo moyo umene timaudziwa ndi wamwa Yesu Khristu. Ndipo moyo umene tili nawo tsopano ndi moyo wa Khristu. Choncho Paulo kuti anene kuti: “Ndapachikidwa ndi Khristu, koma ndiri ndi moyo; wosatinso ine ayi, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nawo: tsopanu m´thupi, ndiri nao m’chikhulupiliro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine” (Agalatiya 2:20).
Kodi chinsinsi cha mphamvu yathu ndi chiyani?
Ngati tingakumbukire zomwe timanena zokhudza nthano ya nkhuku ndi bakha ndiganiza kuti mukhala ndi chinthunzithunzi cha miyoyo ya anthu masiku ano. Kodi vuto lenileni ndi chiyani? Nkhuku singathe kupanga abakha kuti azikhala mmene nkhuku zimachitira, izo zimakula, makhalidwe amasintha. Abakha amafunitsitsa atamalowa mmadzi mwayi ukapezeka. Nthawi zina ndi zoona onse akhoza kukhala otetezedwa kudzera mmapiko ake ndipo iye akhoza kuganiza kuti wapambana ndipo akhoza kuwasunga bwinobwino. Koma ayi sichoncho, iye ayembekezele mavuto, chifukwa aziyipirayipira, mkazi wa mlimi pakumva kulira kwake momvetsa chisoni atmuma mwana wake wankazi kuti akawachotse abakha m´madzi pa kuti iye akuwona kuti vuto la nkhuku likumulepheletsa kuti asamalire bwinobwino tinkhuku. Nkhuku zikusangalala ndi mthandizi watsopanoyo, ngakhale mkazi wa mlimi sanapeze njira zeni zeni zosinthira chikhalidwe cha abakha, koma tsopano iye ali ndi mphamvu yowalamulira.
Tsopano aliyense wobadwa ndi Mzimu wa Mulungu ali ndi umunthu wa tsopano womwe waikidwa mwa iye ndipo amati “Ndimakondwera ndi chilamuo cha Mulungu ndi umunthu wa mkati mwanga” (Aroma 7:22). Komanso amawonanso kuti ayenera kuchitanso ndi zilakolako zinanso monga zomwezo ndi umunthu wakale, timawerenga kuti “Zinthu za kuthupi” komanso “zinthu za Mzimu”, ndipo zonsezi zimakhala zosiyana.
Koma chimene chimamuvutitsa wobadwanso mwatsopano ndi choti iye sangathe kupanga thupi kukhala chomwe mawu a Mulungu amaphunzitsa, chokhudza mmene wobadwanso mwatsopano ayenera kukhalira, komanso lamulo ngakhale iye amakondwera mwa ilo silimamupatsa Mphamvu. Mu njira yina tikhonza kunena kuti, iye akuyesera kukwanilitsa chomwe Mulungu wanena kuti sichingatheke monga, chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu (Aroma 8:7-8). Iye akuti yemwe ali m’thupi amapanga za kuthupi ndipo ndi mdani wa chilamulo cha Mulungu komanso Mulungu amene. Tikachilimika kutengera chilamulo ku thupi tikungovutika pachabe. Tingozibweretsera udani ngakhale udani unalipo kale. Pamene tithira madzi pa alyimu otentha mmalo mozizilitsa ndiye kuti ukonza kubuka moto womwe unali mkati, ndi momwe thupi liliri. Lamulo limangobweretsa chidani ngakhale chidani chinalipo kale, “Pakuti uchimo udziwika ndi chilamuro” (Aroma 3:20). Ngakhale obadwanso mwatsopano ali ndi umunthu wochita zabwino, koma amaonanso kuti “Choipa chimapezekaso mwa iye”, ndipo iye amalimbana nacho ndipo amadzimvera chisoni kuti “Ine munthu wosauka adzandilanditsa ndani?” Ndipo pamenepo chipulumutso chabwerandi. Ndipo iye amathokoza Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu. Apa ndiye kuti iye waphunzira chomwe munthu aliyense ayenera kudziwa, kuti chipulumutso chisanafike, choyambilira ndi chakuti thupi ndilopanda pake, mulibe chabwino kapena chothandiza (Aroma 7:18, 8:7), ndipo chachiwiri ndichakuti, ngakhale umunthu watsopano mulibe mphamvu yeniyeni yabwino kapena yoipa. Choncho Mzimu wa Mulungu wachita zambiri kuposera kumuukitsa wochimwa kenako umakhala ndi mphamvu pa moyowo. Ngati wobadwanso mwatsopano wakhulupilira uthenga wa chipulumutso, Mzimu woyera ngati munthu wapadera amalowa mwa iye ngati mwini (Aefeso 1:13). Iye ndi wosindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu woyera mpaka pa tsiku la maomboledwe kapena tinene kuti “Chipulumutso cha thupi” (Aefeso 4:30, muonenso Aroma 8:9, 14, 16 koma mawu a Mulungu Mwini pa Yohane 14:17). Malingana ndi 1 Akorinto 6:19, thupi lake limakhala “kachisi wa Mzimu woyera” yemwe ali mwa iye. Iye sali mwa yekha koma “ndiwogulidwa ndi mtengo wapatali”.
Miyezi yapitayo ndinaona uthenga utapachikidwa pa nyumba yayikulu (yonga ngati hotela), “Nyumbayi itsekulidwanso pa tsiku lakuti, koma ndi wogwira ntchito atsopano”. Ine ndimaganiza kuti inapita kwa anthu ena ndipo mwini wake ndi winanso, uthenga umenewu wandikumbutsa mawu ochokera pa (1 Akorinto 6:19, 20). Nyumba inali yomweyo, mazenera, zitseko, motulukira utsi, nyumba za panja zonse zinali mmene zinaliri koma mwini wake anali wina ndipo “ogwiranso ntchito nawo atsopano”. Choncho zili ngati munthu wokhulupirira, ndi yemweyo, ndi zonse zimene anali pachiyambi asanasinthike, akupanga bizinesi yomweyo mwinanso akuchezanso ndi omwewo omuzungulira, koma tsopano ndi wa wina. Iye ndi wa Khristu ndipo monga mwa ichi waikidwa pansi pa ulamuliro watsopano. Mzimu woyera umalowa m´thupi mwake nakhazikikamo kuti unkalamulire kulingana ndi mfundo zakumwamba. Izi ndi zosowa! Ndipo zodalitsika kwambiri!
Tsopano chifukwa cha ichi mphamvu ya okhulupilira inakhala yogwirizana ndi Mulungu. Iyi ndi mphamvu yake imene imatha kulamulira thupi ndipo imagonjetsa zochita za thupilo (Aroma 8:13). Monga mmene mwana uja analekanitsira zofuna za bakha kuti nayo nkhuku ithe kulamulira monga atiuzira mu Agalatiya 5:17 kuti “pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi, pakuti izi sizilingana, kuti zimene muzifuna musazichite”. Chomwe tiyenera kusamala ndi choti musamvetse chisoni Mzimu woyera wa Mulungu amene anabwera kudzakhala nafe ndipo tinasindikizidwa chizindikiro mwa iye kufikira tsiku la maomboledwe (Aefeso 4:30). Pali zinthu ziwiri zofunika kukumbukira zokhudza mphamvu:
- Kuti tidziwe kuti tilibe china chilichonse chomwe ndi chathu.
- Kuti tikuyenera kudalira Khristu kuti mphamvu ya Mzimu woyera ikhale yopambana mwa ife. Mphamvu yathu ndi yofooka yomwe ikuyenera kudalira wina.
Koma pakhonza kukhala funso, loti choipa chikhalabe bwanji mwa okhulupilira komanso kuti ngati choipa chili chokonzeka kuziteteza.
“Yense obadwa mwa Mulungu sangachimwe”
Tiyeni tiwone poyambilira kuti sikuti amene amakhala ndi chikhulupiriro ndi ochepa, ndipo abadera-dera, m´meine anthu ena amanenera koma zimatengera m’badwo wonse umene ndiwokhulupilira pakuti “yense obadwa mwa Mulungu”.
Koma mawuwa amatsutsana ndi mmene ine ndimadzionera ndekha kapena m´mene ndimaonera anthu ena. Izi zikhoza kukhala ngati choncho, koma tione mopemphera, kuganizira kuti choyambilira kuti timvetse mawu a Mulungu ndikukhulupilira mawuwo. „Ndi chikhulupiliro tidzindikira“ (Ahebri 11:3). Ndipo apa ndikupatsani chitsanzo, cha monga m´mene timakwatitsira mtengo wa chipatso cha apozi ndi chipatso cha mtundu wina, mutu wa mtengo umadulidwa kenako ka nthambi kakang’ono kamaphatikizidwa ku mtengo wina uja monga m´mene timanenera kuti kukwatitsa mitengo ndipo umasamalidwa powuteteza ndi dothi pomwe palumikizidwapo ndipo umasamalidwa kuti ukule ndi kulimba m’nyengo ya chilimwe.
Tiyeni titanthauzire chinthunzinthunzichi. Chipatso chakuthengochi chikuimira munthu, ndi umunthu wake pamene iye asanabadwe mwa Mulungu. Pa nthawi yake yobadwanso kachiwiri, monga ngati mtengo wa apozi womwe wakwatitsidwa chikhalidwe chatsopano chimalengedwa mwa iye ndi Mzimu komanso ndi mau.
Tsopano mtumiki Yohane mu mabuku ake akuyankhula za zinthu izi mokuluwika. Monga ngati mlimi uja akhoza kulimbikira kunena kuti unali mtengo wa apozi, chomwecho Yohane akutiwonetsa kuti izi zikugwilizana ndi chikhalidwe chatsopano – chimene chili chikhalidwe cha Umulungu chimene amakhala nacho pamene wabadwanso mwa Mulungu. Monga sizotheka kuti mtengo wa apozi ubereke chipatso chosiyana, komanso chifukwa choti ndi mtengo wa apozi, ndipo ndizosatheka kuti yemwe wabadwa mwa Mulungu achite tchimo. “Chifukwa mbeu yache ikhala mwa iye, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.” Kodi chikhalidwe cha Umulungu chingachimwe bwanji?
Chikhalidwe cha Umulungu ichi ndi chimenedi Khrisitu anachionetsera mu njira yake yodalitsika mu dziko lapansi. Choncho iye sanachimwe. Iye akanachimwa bwanji? Iye anagonjetsa dziko. Oipa sakanamukhudza iye. “Pakuti mkulu wa dziko lapansi adza, ndipo alibe kanthu mwa ine” (Yohane 14:30). Monga tawona kale izi ndi zinthu zomwe ndi zoona kwa anthu obadwa mwa Mulungu. Kuti Mtumwi akhonza kunena kuti “Ndicho chimene chiri choona mwa iye (Khristu) ndi mwa inu“ (Yohane 2:8). Chinthu chosangalatsa kwambiri! Tiyeni tisangalale kuti, “Taonani chikondicho Atate watipatsa kuti titchedwe ana a Mulungu, ndipo tili ife otere mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silizindikira Iye” (1 Yohane 3:1). Pamene Yohane akuyankhula za chikhalidwe cha Umulungu mokuluwika motere wangwiro mosawonetsera, iye mbali ina sakusiya kupezeka kwa tchimo mwa wokhulupilira. Choncho 1 Yohane 1:8 akuti “Tikati kuti tilibe uchimo tizinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi”, komanso pa 1 Yohane 2:1 tikuuzidwa kuti tisachimwe ndipo akutitsimikizira kuti ngati tigwa mu uchimo mwachitsanzo kulekana ndi Atate, Yesu Khristu woyera, amene amatilumikiza mu chiyanjano ndi Atate potibweretsa kwa iye ngati ana ake kuti tilape machimo. Komanso tili ndi chilimbikitso mu 1 Yohane 1:9 choti: “Ngati tivomereza machimo athu ali wokhulupirika ndi wolungama Iye kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chili chonse.” Koma chifukwa chiyani ali wokhulupirika ndi wolungama? Chifukwa chakuti Yesu Khristu yemwe ndi wolungama anagonjetseratu tchimo ndi mwazi wake pa mtanda.
Tsopano mu zolemba za Paulo, tabweretsa ife chiphunzitso cha Mzimu woyera kwa wokhulupirira kuchokera ku umunthu wake wakale mwa Adamu mpaka ku umunthu wake wolungamitsidwa komanso kuvomerezedwa ndi Yesu Khristu iye amatiwonetsa kuti ngakhale pali zikhalidwe ziwiri zosiana mwa okhulupirira koma chifukwa Mulungu adagonjetsa tchimo kudzera m’thupi la mwana wake pa mtanda, ife ndi okhulupirira omwe tili ndi mwayi odziwa kuti chikhalidwe chathu chakhale, monga “chipatso chija” chinatheratu pamenepo, pamaso pake mwa lamulo, kuti chikhalidwe chathu chakhale chinapachikidwa ndi Iye Khristu, kotero kuti tadulidwa monga anthu m´thupi (Akolose 2:11) ndipo sitilinso m´thupi.
Chomwecho akhoza kuyankhula za nthawi yomwe ife tinali m’thupi (Aroma 7:5), komanso Aroma 8:9, m´mene akunena kuti “koma inu simuli m’thupi ayi, koma mu Mzimu”, monga ngati m´tengo ukanati umayankhula ukananena kuti, “Ine sindinataye chikhalidwe changa ngati mtengo komabe ngakhale ndinali chipatso m’thengo tsopano ndine mtengo wa apozi m’mundamu.” Ndi chinthu chodalitsa kuti si ifenso a umunthu wa kale wa Adamu woyamba koma ife ndife oukanso amoyo a Khristu, amene ali Adamu womaliza. “Pakuti munafa”, Iye akutero, “ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu” (Akolose 3:3). “Chifukwa chache tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa” (Aroma 8:1).
Kodi ndi chikhalidwe chiti chomwe ndiyenera kuphatikikako?
Tawona kuti sikuti pali zikhalidwe ziwiri zokha koma kuti ndi ziyambi zawo zosiyana, zilinso ndi zikhalidwe zosiyana zambiri. Ndipo pali “zinthu za thupi” komanso “zinthu za Uzimu”. Tiyeni tisayiwale kuti zikhalidwe zawo zidzitiyitana tsiku lililonse ku zofuna zawo.
Tawonani mbalame zazing’ono ziwiri mu chitsa, ndipo zikulimbirana chakudya. Mbalame yaying’ono yomwe ikulira kuti “Ndidyetseni ine” komanso mbalame inanso yaying’ono ikuliranso ndikumati, “Ndidyetseni ine” koma chifukwa cha umunthu osiyana, ngakhale zikulimbanirana chakudya mu chitsamo, zikhalidwe ziwiri zimene zili mwa M´Khristu sizingadye limodzi, pakuti chimene chikhalidwe chakale chimadya, chikhalidwe chatsopano sichingadye, chimodzimodzi chomwe chili chakudya cha chikhalidwe chatsopano ndichoipa ku chikhalidwe chakale.
Choncho akutiuza ku Aroma 13:14 kuti “musaganizire za thupi kuchita zofuna zache” ndipo 1 Petro 2:11 akuti usachite “zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo”. Koma kumbali ina akutiuza kuti “Lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nawo kufikira chipulumutso” (1 Petro 2:2). Tiyeni tikhale a tcheru ndikulingalira zomwe tawerenga, kuganiza, kuchita kapena kuyankhula ndikuzifunsa funsoli: Kodi ichi chikhala chakudya cha umunthu watsopano kapena chigwira ntchito ku thupi? Tiyeni tiwonetsetse kuti tisalole chilakolako chilichonse cha thupi. Petro akutichenjeza ife kuti ndi chilakolako chathu cha thupi chimene “chimalimbana ndi nkhondo pa moyo”. Ndi angati amene angathe kuyankha funso lovutali! Ndipo tiyeni tisaiwale kuti kupatula funso lokhudza chipulumutso, palinso zitsanzo za zotsatira zake mu dziko ili pamene “tidzala mu thupi”, komanso pamene, “tidzala mu Mzimu”. “Chimene munthu achifesa chimenenso adzachituta” (Agalatiya 6:7), choncho ngati tifesa ku thupi tiyembekezere kuti “tidzatuta chivundi”. Tiyeni tisalole kuti boma lomwe lili m’manja mwa Atate athu kuti liwononge chikhulupiliro chathu mu chikondi chomwe chili m’mtima mwa Atate athu. Tiyeni tikhale ndi chikumbumtima komanso tisadzidalire tokha, wokondedwa mnzanga wokhulupilira. Koma Khristu yekha akhale chakudya chathu chambiri tsiku ndi tsiku – mawu ake amtengo wapatali akhale chotisangalatsa.